Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 13:1-13
-
Chikondi—njira yopambana (1-13)
13 Ngati ndimalankhula zilankhulo* za anthu ndi angelo koma ndilibe chikondi, ndili ngati belu longolira kapena chinganga chosokosera.
2 Ndipo ngati ndili ndi mphatso yonenera, yomvetsa zinsinsi zonse zopatulika komanso yodziwa zinthu zonse,+ ndipo ndili ndi chikhulupiriro cholimba moti ndingathe kusuntha mapiri, koma ndilibe chikondi, zomwe ndimachita zilibe ntchito.+
3 Ngati ndingapereke zinthu zanga zonse kuti ndidyetse ena,+ ndipo ngati ndingapereke thupi langa kuti ndidzitame, koma ndilibe chikondi,+ sindingapindule chilichonse.
4 Chikondi+ nʼcholeza mtima+ ndiponso nʼchokoma mtima.+ Chikondi sichichita nsanje,+ sichidzitama, sichidzikuza,+
5 sichichita zosayenera,*+ sichisamala zofuna zake zokha,+ sichikwiya+ ndipo sichisunga zifukwa.+
6 Sichisangalala ndi zosalungama,+ koma chimasangalala ndi choonadi.
7 Chimakwirira zinthu zonse,+ chimakhulupirira zinthu zonse,+ chimayembekezera zinthu zonse+ komanso chimapirira zinthu zonse.+
8 Chikondi sichitha. Koma kaya pali mphatso za kunenera, zidzatha. Kaya Kulankhula malilime,* kudzatha. Ngakhale mphatso yodziwa zinthu, idzatha.
9 Chifukwa sitikudziwa zonse+ ndipo tikunenera moperewera.
10 Koma tikadzadziwa zonse, zoperewerazi zidzatha.
11 Pamene ndinali mwana, ndinkalankhula ngati mwana, kuganiza ngati mwana ndiponso kuona zinthu ngati mwana. Koma mmene ndakulamu, ndasiya zachibwana.
12 Panopa sitikuona bwinobwino chifukwa tikugwiritsa ntchito galasi losaoneka bwino, koma pa nthawiyo tizidzaona bwinobwino. Panopa sindikudziwa zonse, koma pa nthawiyo ndidzadziwa zonse ngati mmene Mulungu akundidziwira ineyo.
13 Komabe, tsopano patsala zitatu izi: Chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “malilime.”
^ Kapena kuti, “mwano.”
^ Kutanthauza kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana modabwitsa.