Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 14:1-40
14 Mukhale ndi chikondi koma muziyesetsanso kuti mulandire mphatso za mzimu woyera, makamaka mphatso ya kunenera.+
2 Chifukwa wolankhula malilime* salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu. Palibe amene amamva zonena zake,+ koma iye amalankhula zinsinsi zopatulika+ mothandizidwa ndi mzimu.
3 Komabe, wonenera amathandiza anthu ndipo amawalimbikitsa komanso kuwatonthoza ndi mawu ake.
4 Wolankhula malilime* amadzilimbikitsa yekha, koma wonenera amalimbikitsa mpingo.
5 Ndikanakondadi kuti nonsenu muzilankhula malilime,*+ koma ndikuona kuti ndi bwino kuti muzinenera.+ Kunena zoona, wonenera amaposa wolankhula malilime, kupatulapo ngati wamalilimeyo akumasulira kuti alimbikitse mpingo.
6 Abale, kodi mungapindule chiyani ngati pa nthawi ino nditabwera kwa inu ndikulankhula malilime* amene simukuwadziwa? Zingakhale zothandiza ngati ndingabwere ndi mawu amene ndalandira kuchokera kwa Mulungu,+ kapena mphatso yodziwa zinthu,+ kapena ulosi kapenanso chiphunzitso.
7 Nʼzofanana ndi zipangizo zoimbira ngati chitoliro kapena zeze. Ngati maliridwe ake atangokhala amodzi osasinthasintha, kodi nʼzotheka kudziwa nyimbo imene ikuimbidwa ndi chitoliro kapena zezeyo?
8 Ngati lipenga silikulira momveka bwino, ndani angakonzekere nkhondo?
9 Nʼchimodzimodzinso ngati mukulankhula zosamveka. Kodi munthu angadziwe bwanji zimene mukunena? Mudzakhala kuti mukulankhula kwa mphepo.
10 Padziko lapansi pali zilankhulo zambiri, koma palibe chimene chilibe tanthauzo.
11 Ngati sindikudziwa tanthauzo la chilankhulo, ndimakhala mlendo kwa wolankhulayo, ndipo wolankhulayo amakhala mlendo kwa ine.
12 Chimodzimodzinso ndi inuyo. Popeza mukufunitsitsa mphatso za mzimu, yesetsani kukhala ndi mphatso zimene zingalimbikitse mpingo.+
13 Choncho amene amalankhula malilime* apemphere kuti athe kumasulira.+
14 Chifukwa ngati ndikupemphera mʼchilankhulo chachilendo,* mphatso yanga ya mzimu ndi imene ikupemphera, koma maganizo anga sakuchita chilichonse.
15 Ndiye chofunika nʼchiyani? Ndiyenera kupemphera ndi mphatso ya mzimu, koma ndipempherenso ndi mawu omveka. Ndiimbe nyimbo zotamanda ndi mphatso ya mzimu, koma ndiimbenso ndi mawu omveka.
16 Chifukwa ngati mothandizidwa ndi mphatso ya mzimu mukutamanda Mulungu, kodi munthu wamba anganene bwanji kuti “Ame” pa pemphero lanu loyamikira, poti sakudziwa zimene mukunena?
17 Nʼzoona kuti mukupereka pemphero loyamikira mʼnjira yabwino, koma munthu winayo sakulimbikitsidwa.
18 Ndimathokoza Mulungu kuti ndimalankhula zilankhulo zambiri* kuposa nonsenu.
19 Ngakhale zili choncho, ndi bwino kuti mumpingo ndilankhule mawu 5 omveka kuti ndiphunzitse anthu ena, kusiyana nʼkulankhula mawu 10,000 mʼchilankhulo chachilendo.*+
20 Abale, musakhale ana aangʼono pa nkhani yomvetsa zinthu.+ Koma khalani ana pa zoipa,+ ndipo pa nkhani yomvetsa zinthu khalani anthu akuluakulu.+
21 MʼChilamulo muli mawu akuti: “‘Anthu awa ndidzawalankhula ndi malilime a anthu achilendo, ndipo ndidzawalankhula ndi milomo ya anthu achilendo, koma iwo adzakana kundimvera,’ watero Yehova.”*+
22 Choncho malilime* ndi chizindikiro cha osakhulupirira, osati okhulupirira,+ pomwe kunenera ndi chizindikiro cha okhulupirira, osati osakhulupirira.
23 Ndiye ngati mpingo wonse wasonkhana ndipo onse akulankhula malilime, ndiyeno mwalowa anthu wamba kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mitu yanu sikugwira?
24 Koma ngati nonse mukunenera, ndiyeno mwalowa munthu wosakhulupirira kapena munthu wamba, iye amadzudzulidwa ndiponso kufufuzidwa mosamala ndi nonsenu.
25 Amadziwa zinthu zobisika zamumtima mwake, moti adzawerama nʼkulambira Mulungu, ndi kunena kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.”+
26 Ndiyeno zizikhala bwanji abale? Mukasonkhana pamodzi, wina akhoza kukhala ndi salimo,* wina chiphunzitso, wina mawu amene walandira kuchokera kwa Mulungu komanso wina akhoza kulankhula malilime* wina nʼkumamasulira.+ Muzichita zonsezi kuti mulimbikitsane.
27 Ngati pali anthu olankhula malilime,* asapose awiri kapena atatu ndipo azipatsana mpata komanso wina azimasulira.+
28 Koma ngati palibe womasulira, wa malilimeyo akhale chete mumpingo ndipo azilankhula ndi Mulungu chamumtima.
29 Aneneri+ awiri kapena atatu alankhule, ndipo ena onse aziyesetsa kumvetsa tanthauzo la zimene iwo akulankhulazo.
30 Koma ngati mneneri wina amene wakhala pansi walandira mawu kuchokera kwa Mulungu, woyamba uja akhale chete.
31 Nonse mukhoza kunenera, koma muyenera kupatsana mpata kuti onse aphunzire ndiponso kulimbikitsidwa.+
32 Ndipo aneneri akamagwiritsa ntchito mphatso za mzimu ayenera kukhala odziletsa.
33 Chifukwa Mulungu si Mulungu wachisokonezo, koma wamtendere.+
Ngati mmene zilili mʼmipingo yonse ya oyerawo,
34 akazi azikhala chete mʼmipingo, chifukwa nʼzosaloleka kuti iwo azilankhula,+ koma azigonjera,+ ngati mmenenso Chilamulo chimanenera.
35 Ngati akufuna kumvetsa zinazake, akafunse amuna awo kunyumba, popeza nʼzochititsa manyazi kuti mkazi azilankhula mumpingo.
36 Kodi mawu a Mulungu anachokera kwa inu, kapena ndi inu nokha amene munauzidwa mawuwo?
37 Ngati munthu akuganiza kuti ndi mneneri kapena ali ndi mphatso ya mzimu, ayenera kuvomereza kuti zimene ndakulemberanizi ndi lamulo la Ambuye.
38 Koma ngati wina savomereza zimenezi, iyenso sadzavomerezedwa.*
39 Choncho abale anga, yesetsani kuti muzinenera,+ komabe musaletse kulankhula malilime.*+
40 Koma zinthu zonse zizichitika moyenera ndiponso mwadongosolo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”
^ Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”
^ Kapena kuti, “zilankhulo zachilendo.”
^ Kapena kuti, “zilankhulo.”
^ Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmalilime.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “malilime.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmalilime.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kutanthauza kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana modabwitsa.
^ Kapena kuti, “nyimbo zotamanda Mulungu.”
^ Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”
^ Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”
^ Mabaibulo ena amati, “ngati wina angakhale wosadziwa, akhalebe wosadziwa.”
^ Kapena kuti, “chilankhulo chachilendo.”