Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 15:1-58

  • Kuukitsidwa kwa Khristu (1-11)

  • Kuuka kwa akufa ndi maziko a chikhulupiriro (12-19)

  • Kuuka kwa Khristu kumatitsimikizira kuti akufa adzauka (20-34)

  • Thupi la mnofu ndiponso thupi lauzimu (35-49)

  • Thupi loti silingafe kapena kuwonongeka (50-57)

  • Kuchita zambiri pa ntchito ya Ambuye (58)

15  Tsopano abale, ndikukukumbutsani za uthenga wabwino umene ndinaulalikira kwa inu,+ umenenso inuyo munaulandira ndiponso kuukhulupirira. 2  Mukupulumutsidwa ngati mwagwira mwamphamvu uthenga wabwino umene ndinaulalikirawo. Koma ngati simunaugwire mwamphamvu ndiye kuti kukhala kwanu okhulupirira kulibe phindu. 3  Pa zinthu zoyambirira zimene ndinakuphunzitsani, zomwenso ineyo ndinalandira, panali zonena kuti, Khristu anafera machimo athu, mogwirizana ndi Malemba.+ 4  Ndiponso kuti anaikidwa mʼmanda,+ kenako anaukitsidwa+ pa tsiku lachitatu,+ mogwirizana ndi Malemba.+ 5  Panalinso zoti anaonekera kwa Kefa,*+ kenako kwa atumwi 12 aja.+ 6  Ndiyeno anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi,+ ndipo ambiri a iwo tidakali nawo, koma ena anagona mu imfa. 7  Atatero anaonekera kwa Yakobo,+ kenako kwa atumwi onse.+ 8  Koma pomaliza anaonekera kwa ine,+ ngati khanda lobadwa masiku osakwana. 9  Ineyo ndine wamngʼono kwambiri pa atumwi onse ndipo si ine woyenera kutchedwa mtumwi, chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu.+ 10  Koma chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili mmene ndililimu. Ndipo kukoma mtima kwakukulu kumene anandisonyeza sikunapite pachabe, koma ndinagwira ntchito mwakhama kuposa atumwi ena onse. Komabe sindinachite zimenezi ndi mphamvu zanga zokha, koma chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. 11  Kaya munaphunzitsidwa ndi ineyo kapena iwowo, uthenga umene tikulalikira ndi womwewo, umenenso munaukhulupirira. 12  Tsopano ngati timalalikira kuti Khristu anaukitsidwa,+ nʼchifukwa chiyani ena a inu akunena kuti akufa sadzaukitsidwa? 13  Chifukwa ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristu nayenso sanaukitsidwe. 14  Komanso ngati Khristu sanaukitsidwe, kulalikira kwathu nʼkopanda phindu, ndipo chikhulupiriro chanu nʼchopandanso phindu. 15  Ndiponso, ndiye kuti ndife mboni zonama za Mulungu,+ chifukwa ngati akufa sadzaukadi, tapereka umboni wonamizira Mulungu kuti anaukitsa Khristu+ pamene sanamuukitse. 16  Chifukwa ngati akufa sadzauka, Khristunso sanaukitsidwe. 17  Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu nʼchopanda ntchito ndipo machimo anu sanakhululukidwe.+ 18  Ndiye kutinso otsatira a Khristu amene anagona mu imfa, zawo zinathera pomwepo.+ 19  Ngati chiyembekezo chathu mwa Khristu ndi cha moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse. 20  Komabe, Khristu anaukitsidwa nʼkukhala ngati chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.+ 21  Popeza imfa inabwera kudzera mwa munthu mmodzi,+ kuuka kwa akufa kunabweranso kudzera mwa munthu mmodzi.+ 22  Monga zilili kuti anthu onse amafa chifukwa cha Adamu,+ anthu onse adzapatsidwanso moyo kudzera mwa Khristu.+ 23  Koma aliyense pa nthawi yoyenera: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyambirira,+ kenako anthu a Khristu pa nthawi ya kukhalapo* kwake.+ 24  Ndiyeno pamapeto pa zonse, adzapereka Ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake, atathetsa maboma onse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse.+ 25  Chifukwa ayenera kukhala mfumu nʼkumalamulira mpaka Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake.+ 26  Imfa nayonso, yomwe ndi mdani womaliza, idzawonongedwa.+ 27  Mulungu “anaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.”+ Koma pamene akunena kuti ‘waika zinthu zonse pansi pake,’+ nʼzodziwikiratu kuti sakuphatikizapo Mulunguyo, amene anaika zinthu zonsezo pansi pa iye.+ 28  Koma zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwanayonso adzasonyeza kuti ali pansi pa ulamuliro wa Mulungu,+ kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.+ 29  Apo ayi, kodi amene akubatizidwa kuti akhale akufa adzatani?+ Ngati akufa sadzaukitsidwa, nʼchifukwa chiyani anthuwo akubatizidwa kuti akhale akufa? 30  Nʼchifukwa chiyaninso ifeyo tikuika moyo wathu pachiswe nthawi zonse?+ 31  Tsiku lililonse ndimakhala pa ngozi yoti ndikhoza kufa. Zimenezi nʼzoona ngati mmene zilili zoona kuti ndimakunyadirani chifukwa cha ubwenzi wanu ndi Khristu Yesu Ambuye wathu. 32  Ngati ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso+ ngati mmene enanso anachitira,* ndinapindulapo chiyani? Ngati akufa sadzauka, “tiyeni tidye ndi kumwa chifukwa mawa tifa.”+ 33  Musapusitsidwe.* Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.+ 34  Yambani kuganiza mwanzeru nʼkumachita zoyenera ndipo musamachite tchimo. Ena a inu sadziwa Mulungu. Ndikulankhula zimenezi kuti ndikuchititseni manyazi. 35  Komabe, wina anganene kuti: “Kodi akufa adzaukitsidwa bwanji? Nanga adzauka ndi thupi lotani?”+ 36  Wosaganiza bwino iwe! Ukadzala chinthu sichikhala ndi moyo pokhapokha chitafa kaye. 37  Ndipo ukamadzala, sudzala mmera wokula kale, koma mbewu chabe, kaya ya tirigu kapena ina iliyonse. 38  Koma Mulungu amaikulitsa mogwirizana ndi kufuna kwake, ndipo mbewu iliyonse ikamakula sifanana ndi inzake. 39  Zinthu zonse zimene zimakhala ndi mnofu sizikhala zofanana. Anthu, nyama, mbalame ndiponso nsomba zili ndi mnofu, koma chilichonse nʼchosiyana ndi chinzake. 40  Palinso matupi akumwamba+ ndiponso matupi apadziko lapansi,+ koma ulemerero wa matupi akumwamba ndi wosiyana ndi ulemerero wa matupi apadziko lapansi. 41  Ulemerero wa dzuwa ndi wosiyana ndi ulemerero wa mwezi+ kapenanso wa nyenyezi. Ndipotu ulemerero wa nyenyezi ina, umasiyananso ndi wa nyenyezi ina. 42  Ndi mmenenso zilili ndi kuuka. Thupi limene limakwiriridwa limakhala loti lingawonongeke, koma limene limaukitsidwa limakhala loti silingawonongeke.+ 43  Limakwiriridwa lili lonyozeka, koma limaukitsidwa lili laulemerero.+ Limakwiriridwa lili lofooka, koma limaukitsidwa lili lamphamvu.+ 44  Limakwiriridwa lili thupi la mnofu, koma limaukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi la mnofu, palinso lauzimu. 45  Paja Malemba amati: “Adamu, yemwe anali munthu woyambirira, anakhala munthu wamoyo.”+ Adamu womalizira anakhala mzimu wopatsa moyo.+ 46  Komabe, amene anayamba kubwera si munthu wauzimuyo. Munthu wokhala ndi mnofu ndi amene anayamba kubwera kenako munthu wauzimu. 47  Munthu woyambayo anachokera padziko lapansi ndipo anapangidwa ndi dothi.*+ Wachiwiriyo anachokera kumwamba.+ 48  Anthu opangidwa ndi dothi ali ngati munthu woyambayo amene anapangidwa ndi dothi. Ndipo akumwamba ali ngati wochokera kumwambayo.+ 49  Monga zilili kuti panopa tikufanana ndi wopangidwa ndi dothi uja,+ tidzafanananso ndi wakumwambayo.+ 50  Koma abale, dziwani kuti mnofu ndi magazi sizingalowe mu Ufumu wa Mulungu. Komanso chinthu chimene chingawonongeke sichingalandire kusawonongeka. 51  Tamverani, ndikuuzeni chinsinsi chopatulika: Sikuti tonse tidzagona mu imfa, koma tonse tidzasintha,+ 52  mʼkanthawi kochepa, mʼkuphethira kwa diso, pa kulira kwa lipenga lomaliza. Chifukwa lipenga lidzalira,+ kenako akufa adzaukitsidwa ndi matupi oti sangawonongeke ndipo tidzasintha. 53  Chifukwa matupi oti akhoza kuwonongekawa adzasintha nʼkukhala oti sangawonongeke.+ Ndipo matupi oti angafewa adzasintha nʼkukhala oti sangafe.+ 54  Koma matupi oti akhoza kuwonongekawa akadzakhala oti sangawonongeke komanso matupi oti angafewa akadzasintha nʼkukhala oti sangafe, zimene Malemba amanena zidzakwaniritsidwa, zakuti: “Imfa yamezedwa* kwamuyaya.”+ 55  “Iwe Imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe Imfa, amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?”+ 56  Mphamvu imene imabweretsa imfa ndi uchimo,+ koma Chilamulo nʼchimene chimasonyeza mphamvu ya uchimo.+ 57  Koma tikuthokoza Mulungu chifukwa amatithandiza kuti tipambane kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 58  Choncho abale anga okondedwa, khalani olimba+ ndiponso osasunthika. Nthawi zonse muzikhala ndi zochita zambiri+ pa ntchito ya Ambuye, podziwa kuti zonse zimene mukuchita pa ntchito ya Ambuye sizidzapita pachabe.+

Mawu a M'munsi

Amatchedwanso Petulo.
Mabaibulo ena amati, “mogwirizana ndi kuona kwa anthu.”
Kapena kuti, “Musasocheretsedwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “fumbi.”
Kapena kuti, “yathetsedwa.”