Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 7:1-40

  • Malangizo a anthu amene sali pabanja ndi amene ali pabanja (1-16)

  • Mukhale mmene munalili pamene munkaitanidwa (17-24)

  • Anthu omwe sali pabanja ndiponso akazi amasiye (25-40)

    • Ubwino wosakhala pabanja (32-35)

    • Kukwatiwa “mwa Ambuye” (39)

7  Tsopano pa nkhani imene munalemba ija, ndi bwino kuti mwamuna asakhudze* mkazi. 2  Koma chifukwa cha kufala kwa chiwerewere,* mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake+ ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.+ 3  Mwamuna azipereka kwa mkazi wake zimene amafunikira,* mkazinso azipereka kwa mwamuna wake zimene amafunikira.+ 4  Mkazi asakhale ndi ulamuliro pathupi lake. Ulamulirowo ukhale ndi mwamuna wake. Mwamunanso asakhale ndi ulamuliro pathupi lake, koma ulamulirowo ukhale ndi mkazi wake. 5  Musamakanizane, pokhapokha ngati mwagwirizana kudikira kaye kwa nthawi inayake kuti mugwiritse ntchito nthawi imeneyo popemphera, kenako nʼkuyambiranso mwa nthawi zonse, kuopera kuti Satana angapitirize kukuyesani mukalephera kudziletsa. 6  Sindikunena zimenezi ngati lamulo, koma kuti mudziwe zololeka. 7  Koma ndikanakonda amuna onse akanakhala ngati ineyo. Komabe aliyense ali ndi mphatso+ imene Mulungu anamupatsa ndipo timamutumikira mʼnjira zosiyanasiyana. 8  Tsopano kwa osakwatira ndiponso akazi amasiye ndikunena kuti, ndi bwino akhalebe mmene ineyo ndililimu.+ 9  Koma ngati sangathe kudziletsa, akwatire, chifukwa ndi bwino kukwatira kusiyana nʼkuvutika ndi chilakolako.+ 10  Kwa okwatira ndikupereka malangizo awa, kuti mkazi asasiye mwamuna wake.+ Malangizo amenewa ndi ochokera kwa Ambuye. 11  Koma ngati angamusiye, akhale choncho wosakwatiwa. Apo ayi, abwererane ndi mwamuna wakeyo. Mwamunanso asasiye mkazi wake.+ 12  Koma kwa enawa, ineyo, osati Ambuye,+ ndikunena kuti: Ngati mʼbale ali ndi mkazi wosakhulupirira, ndipo mkaziyo akulola kukhala naye, asamusiye. 13  Ngatinso mkazi ali ndi mwamuna wosakhulupirira, ndipo mwamunayo akulola kukhala naye, asamusiye. 14  Mwamuna wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mkazi wake, ndipo mkazi wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mʼbaleyo, apo ayi, ana anu sakanakhala oyera, koma tsopano ndi oyera. 15  Koma ngati wosakhulupirirayo wasankha kuchoka, achoke. Zikatero mʼbale kapena mlongo sakhala womangika, koma Mulungu wakuitanani kuti mukhale mwamtendere.+ 16  Mkaziwe, ukudziwa bwanji, mwina ukakhalabe ndi mwamuna wako ungamʼpulumutse?+ Kapena mwamunawe, ukudziwa bwanji, mwina ukakhalabe ndi mkazi wako ungamʼpulumutse? 17  Ngakhale zili choncho, munthu aliyense akhale mmene analili pamene Yehova* Mulungu ankamuitana.+ Amenewa ndi malangizo amene ndikupereka kumipingo yonse. 18  Kodi pali mwamuna amene anaitanidwa ali wodulidwa?+ Akhalebe wodulidwa. Nanga alipo amene anaitanidwa ali wosadulidwa? Asadulidwe.+ 19  Mdulidwe sutanthauza chilichonse ndipo kusadulidwa sikutanthauzanso chilichonse,+ koma chofunika nʼkusunga malamulo a Mulungu.+ 20  Aliyense akhalebe mmene analili pamene ankaitanidwa.+ 21  Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usade nazo nkhawa zimenezo.+ Koma ngati mwayi wokhala womasuka ulipo, ugwiritse ntchito. 22  Aliyense amene anaitanidwa mwa Ambuye ali kapolo, ndi mtumiki wa Ambuye womasuka+ ndipo amene anaitanidwa asali kapolo, ndi kapolo wa Khristu. 23  Munagulidwa pa mtengo wokwera,+ siyani kukhala akapolo a anthu. 24  Abale, aliyense akhalebe mmene analili pamene ankaitanidwa ndi Mulungu. 25  Tsopano kunena za amene sali pabanja,* ndilibe lamulo lililonse la Ambuye, koma ndikupereka maganizo anga+ monga munthu amene anasonyezedwa chifundo ndi Ambuye kuti ndikhale wokhulupirika. 26  Chifukwa cha mavuto amene tili nawo, ndikuganiza kuti ndi bwino kuti mwamuna akhalebe mmene alili. 27  Kodi uli ndi mkazi? Siya kufunafuna njira yomasukira.+ Kodi ulibe mkazi? Siya kufunafuna mkazi. 28  Koma ngakhale utakwatira, sikuti uchimwa. Ndipo ngati amene sali pabanja* walowa mʼbanja, sikuti wachimwa. Komabe, olowa mʼbanjawo adzakumana ndi mavuto pa moyo wawo.* Ine ndikungoyesa kukutetezani. 29  Komanso abale dziwani izi: Nthawi yotsalayi yafupika.+ Kuyambira panopa, amene ali ndi mkazi azikhala ngati alibe 30  ndipo amene akulira azikhala ngati amene sakulira. Amene akusangalala azikhala ngati amene sakusangalala, ndipo amene amagula zinthu azikhala ngati opanda kanthu. 31  Amene amagwiritsira ntchito dzikoli azikhala ngati amene sakuligwiritsira ntchito mokwanira, chifukwa zochitika zapadzikoli zikusintha. 32  Ndikufuna kuti mukhale opanda nkhawa. Mwamuna wosakwatira amadera nkhawa zinthu za Ambuye, mmene angakondweretsere Ambuye. 33  Koma mwamuna wokwatira amadera nkhawa zinthu zamʼdziko,+ mmene angakondweretsere mkazi wake 34  ndipo amakhala wogawanika. Nayenso mkazi wosakwatiwa komanso namwali, amadera nkhawa zinthu za Ambuye,+ kuti akhale woyera mʼthupi lake ndi maganizo ake.* Koma mkazi wokwatiwa amadera nkhawa zinthu zamʼdziko, mmene angakondweretsere mwamuna wake. 35  Ndikunenatu zimenezi kuti ndikuthandizeni, osati kuti ndikupanikizeni, koma kuti ndikulimbikitseni kuchita zoyenera ndiponso kutumikira Ambuye nthawi zonse popanda zosokoneza. 36  Koma ngati munthu amene sali pabanja akulephera kudziletsa, ndipo wapitirira pachimake pa unyamata, ndi bwino kuti akwatire.+ Sakuchimwa. 37  Koma ngati wina watsimikiza mumtima mwake kuti akhoza kukhala wosakwatira ndipo akutha kulamulira maganizo ake komanso wasankha mumtima mwake kukhalabe wosakwatira,* wachita bwino.+ 38  Amenenso wasiyana ndi moyo wokhala yekha nʼkulowa mʼbanja wachita bwino, koma amene sanalowe mʼbanja wachita bwino kwambiri.+ 39  Mkazi amakhala womangika pa nthawi imene mwamuna wake ali moyo.+ Komano mwamuna wake akamwalira, mkaziyo amakhala womasuka kukwatiwa ndi aliyense amene akufuna, koma akwatiwe mwa Ambuye.+ 40  Komabe ndikuona kuti angakhale wosangalala kwambiri ngati atapitiriza kukhala mmene alili. Ndipo ndikukhulupirira kuti ndilinso ndi mzimu wa Mulungu.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza kugonana.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza zokhudza kugonana.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anamwali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “namwali.”
Kapena kuti, “adzakhala ndi nsautso mʼthupi mwawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mumzimu wake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kusungabe unamwali wake.”