Kalata Yoyamba Yopita kwa Atesalonika 1:1-10

  • Moni (1)

  • Kuthokoza chifukwa cha chikhulupiriro cha Atesalonika (2-10)

1  Ine Paulo ndili limodzi ndi Silivano*+ komanso Timoteyo+ ndipo ndikulembera mpingo wa Atesalonika, womwe ndi wogwirizana ndi Mulungu Atate komanso Ambuye Yesu Khristu kuti: Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zikhale nanu. 2  Nthawi zonse timathokoza Mulungu tikamakutchulani nonsenu mʼmapemphero athu.+ 3  Timachita zimenezi chifukwa nthawi zonse timakumbukira ntchito zanu zachikhulupiriro, ntchito zanu zachikondi komanso kupirira kwanu chifukwa cha chiyembekezo chimene muli nacho+ mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu amene ndi Atate wathu. 4  Chifukwa tikudziwa, inu abale okondedwa ndi Mulungu, kuti iye ndi amene anakusankhani. 5  Tikutero chifukwa pamene tinkalalikira uthenga wabwino kwa inu, sitinkangolankhula basi, koma uthengawo unali wamphamvu, unabwera ndi mzimu woyera komanso tinalalikira motsimikiza mtima kwambiri. Inunso mukudziwa zimene tinakuchitirani pofuna kukuthandizani. 6  Munalandira mawuwo ndi chimwemwe chimene mzimu woyera+ umapereka ngakhale kuti munali pamavuto aakulu. Pamenepa munatsanzira ifeyo+ komanso munatsanzira Ambuye,+ 7  moti munakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse ku Makedoniya ndi ku Akaya. 8  Sikuti mawu a Yehova* ochokera kwa inu amveka ku Makedoniya ndi ku Akaya kokha, koma kwina kulikonse chikhulupiriro chanu mwa Mulungu chafalikira,+ moti ife sitikufunika kunenapo kanthu. 9  Chifukwa iwo akunenabe za mmene ife tinakumanirana ndi inu koyamba komanso mmene inu munasiyira mafano anu nʼkutembenukira kwa Mulungu,+ kuti muzitumikira Mulungu wamoyo ndi woona. 10  Munatembenukiranso kwa Mulungu kuti muziyembekezera Mwana wake kuchokera kumwamba,+ amene anamuukitsa kwa akufa. Mwanayo ndi Yesu, amene akutipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwerawo.+

Mawu a M'munsi

Amene ankadziwikanso kuti Sila.