Kalata Yoyamba Yopita kwa Atesalonika 4:1-18

  • Anawachenjeza kuti azipewa chiwerewere (1-8)

  • Muzikondana kwambiri kuposa mmene mukuchitira (9-12)

    • “Musamalowerere nkhani za ena” (11)

  • Amene anafa mwa Khristu adzakhala oyambirira kuuka (13-18)

4  Pomalizira abale, tinakupatsani malangizo a mmene muyenera kuyendera kuti muzisangalatsa Mulungu+ ndipo mukuchitadi zimenezo. Ndiye tikukupemphani komanso kukuchondererani mʼdzina la Ambuye Yesu kuti mupitirize kuchita zimenezi kuposa mmene mukuchitira. 2  Chifukwa mukudziwa malangizo* amene tinakupatsani mʼdzina la Ambuye Yesu. 3  Mulungu akufuna kuti mukhale oyera+ komanso kuti muzipewa chiwerewere.*+ 4  Aliyense wa inu azidziwa kulamulira thupi lake+ kuti likhale loyera+ komanso lolemekezeka pamaso pa Mulungu. 5  Musakhale ngati anthu a mitundu ina omwe sadziwa Mulungu+ komanso ali ndi chilakolako chosalamulirika cha kugonana+ ndipo sakhutiritsidwa. 6  Pasapezeke aliyense wopweteka mʼbale wake pa nkhani imeneyi nʼkumubweretsera mavuto, chifukwa Yehova* adzapereka chilango kwa munthu aliyense amene akuchita zinthu zimenezi, monga mmene tinakuuzirani kale komanso kukuchenjezani mwamphamvu. 7  Chifukwa Mulungu sanatiitane kuti tizichita makhalidwe odetsa, koma kuti tikhale oyera.+ 8  Choncho munthu amene akunyalanyaza machenjezo amenewa sakunyalanyaza munthu, koma Mulungu+ amene amakupatsani mzimu wake woyera.+ 9  Koma zokhudza kukonda abale,+ nʼzosafunika kuti tichite kukulemberani chifukwa inuyo, Mulungu amakuphunzitsani kuti muzikondana.+ 10  Ndipotu mukuchita kale zimenezi kwa abale onse ku Makedoniya konse. Koma tikukulimbikitsani abale kuti mupitirize kuchita zimenezi kuposa mmene mukuchitira. 11  Muziyesetsa kukhala mwamtendere,+ musamalowerere nkhani za ena+ ndipo muzigwira ntchito ndi manja anu+ mogwirizana ndi malangizo amene tinakupatsani. 12  Muzichita zimenezi kuti mukhale ndi makhalidwe amene angachititse kuti anthu akunja azikulemekezani+ ndiponso kuti mukhale osasowa kanthu. 13  Komanso abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa zokhudza amene akugona mu imfa,+ kuti musakhale ndi chisoni chofanana ndi cha anthu amene alibe chiyembekezo.+ 14  Chifukwa ngati timakhulupirira kuti Yesu anafa nʼkuukitsidwa,+ ndiye kuti Mulungu adzaukitsanso amene akugona mu imfa kudzera mwa Yesu,+ kuti akakhale naye* limodzi. 15  Zimene tikukuuzani mogwirizana ndi mawu a Yehova* nʼzakuti, ife amene tipitirize kukhala ndi moyo mpaka pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye, sitidzakhala patsogolo pa amene akugona mu imfa. 16  Chifukwa Ambuyewo adzatsika kuchoka kumwamba ndi mfuu yolamula. Mawu awo adzamveka kuti ndi a mkulu wa angelo+ ndipo adzanyamula lipenga la Mulungu mʼdzanja lawo. Ndipo amene anafa mwa Khristu adzakhala oyambirira kuuka.+ 17  Pambuyo pake ife amene tidzakhale tidakali ndi moyo, limodzi ndi iwowo, tidzatengedwa kupita mʼmitambo+ kukakumana ndi Ambuye+ mumlengalenga ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.+ 18  Choncho pitirizani kulimbikitsana ndi mawu amenewa.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malamulo.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza Yesu.