Kalata Yoyamba Yopita kwa Atesalonika 5:1-28
5 Koma tsopano za nthawi ndi nyengo abale, simukufunika kuti tikulembereni chilichonse.
2 Chifukwa inuyo mukudziwa bwino kuti tsiku la Yehova*+ lidzabwera ndendende ngati wakuba usiku.+
3 Akadzangonena kuti, “Bata ndi mtendere!” nthawi yomweyo adzawonongedwa. Tsoka limeneli lidzawagwera modzidzimutsa+ ngati ululu umene mkazi woyembekezera amamva akatsala pangʼono kubereka ndipo sadzapulumuka.
4 Koma inu abale simuli mumdima kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene akuba amadzidzimukira kunja kukawachera.
5 Chifukwa nonsenu ndi ana a kuwala ndiponso ana a masana.+ Si ife a usiku kapena a mdima.+
6 Choncho tisapitirize kugona ngati mmene ena onse akuchitira,+ koma tikhalebe maso+ ndipo tikhalebe oganiza bwino.+
7 Chifukwa amene akugona amagona usiku ndipo amene amaledzera, amaledzera usiku.+
8 Koma ife amene tili a masana, tikhalebe oganiza bwino ndipo tivale chodzitetezera pachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi. Tivalenso chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa,+
9 chifukwa Mulungu sanatisankhe kuti adzatilange, koma anatisankha kuti tidzapulumuke+ chifukwa cha zimene Ambuye wathu Yesu Khristu anachita.
10 Iye anatifera,+ kuti kaya tikhala maso kapena tigona,* tikhale ndi moyo limodzi ndi iye.+
11 Choncho pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana+ ngati mmene mukuchitira.
12 Tsopano tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolerani mwa Ambuye komanso kukulangizani.
13 Muziwasonyeza chikondi komanso ulemu waukulu chifukwa cha ntchito yawo.+ Muzikhala mwamtendere pakati panu.+
14 Komanso tikukulimbikitsani abale, kuti muzichenjeza* anthu ochita zosalongosoka,+ muzilankhula molimbikitsa kwa anthu amene ali ndi nkhawa,* muzithandiza ofooka, muzikhala oleza mtima kwa onse.+
15 Onetsetsani kuti pasapezeke wobwezera choipa pa choipa kwa wina aliyense,+ koma nthawi zonse muziyesetsa kuchita zabwino kwa okhulupirira anzanu ndi kwa ena onse.+
16 Muzikhala osangalala nthawi zonse.+
17 Muzipemphera nthawi zonse.+
18 Muzithokoza pa chilichonse.+ Mulungu akufuna kuti muzichita zimenezi chifukwa ndinu otsatira a Khristu Yesu.
19 Musazimitse moto wa mzimu.+
20 Musamanyoze mawu aulosi.+
21 Muzifufuza zinthu zonse nʼkutsimikizira zimene zili zabwino+ ndipo gwirani mwamphamvu zabwinozo.
22 Muzipewa zoipa zamtundu uliwonse.+
23 Mulungu wamtendereyo akupatuleni kuti muchite utumiki wake. Ndipo pa mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu komanso thupi lanu, zikhale zopanda chilema kapena cholakwa chilichonse, pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+
24 Amene akukuitanani ndi wokhulupirika ndipo adzachitadi zimenezi.
25 Abale, pitirizani kutipempherera.+
26 Mupereke moni kwa abale onse ndipo mukisane ndi mtima woyera.
27 Ndikukupemphani mwa Ambuye kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.+
28 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu.
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “tigona mu imfa.”
^ Kapena kuti, “muzilangiza.”
^ Kapena kuti, “amene afooka.”