1 Mafumu 20:1-43

  • Asiriya anamenyana ndi Ahabu (1-12)

  • Ahabu anagonjetsa Asiriya (13-34)

  • Ulosi wotsutsana ndi Ahabu (35-43)

20  Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya+ anasonkhanitsa asilikali ake onse. Atatero ananyamuka pamodzi ndi mafumu ena 32 ndi mahatchi komanso magaleta awo ndipo anapita kukazungulira mzinda+ wa Samariya+ nʼkuyamba kumenyana nawo. 2  Kenako anatumiza anthu mumzindawo kwa Ahabu+ mfumu ya Isiraeli, kuti akamuuze kuti: “Beni-hadadi wanena kuti, 3  ‘Siliva ndi golide wako akhala wanga ndipo akazi ako ndi ana ako aamuna abwino kwambiri, akhala anga.’” 4  Mfumu ya Isiraeli inayankha kuti: “Mogwirizana ndi mawu anu mbuyanga mfumu, ine ndi zanga zonse tili mʼmanja mwanu.”+ 5  Kenako anthu aja anabweranso nʼkudzanena kuti: “Beni-hadadi wanena kuti, ‘Ndinakutumizira uthenga wakuti, “Undipatse siliva wako, golide wako, akazi ako ndi ana ako aamuna. 6  Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatumiza atumiki anga. Iwo adzafufuza paliponse mʼnyumba mwako ndi mʼnyumba za atumiki ako ndipo adzatenga zinthu zanu zonse zamtengo wapatali.”’” 7  Mfumu ya Isiraeli itamva mawu amenewa, inaitanitsa akulu onse amʼdzikolo nʼkuwauza kuti: “Munthuyu watsimikiza mtima kuti atibweretsere tsoka. Ananditumizira uthenga woti akufuna akazi anga, ana anga aamuna, siliva wanga ndi golide wanga, ndipo ine sindinamukanize.” 8  Koma akulu onsewo komanso anthu onse anauza mfumuyo kuti: “Musamvere zimenezo ndipo musalole.” 9  Choncho Ahabu anauza anthu amene anatumidwa ndi Beni-hadadi aja kuti: “Mukauze mbuyanga mfumu kuti, ‘Zonse zimene munandiuza poyamba, ine mtumiki wanu ndichita. Koma zimene mwanena kachiwirizi, sindingachite.’” Zitatero, anthuwo ananyamuka nʼkukapereka uthengawo kwa mfumu yawo. 10  Ndiyeno Beni-hadadi anatumizira Ahabu uthenga wakuti: “Milungu yanga indilange mowirikiza, ngati fumbi la ku Samariya lidzakwanire kuti anthu onse onditsatira apatsidwe lodzaza mʼmanja.” 11  Mfumu ya Isiraeli inayankha kuti: “Mukamuuze kuti, ‘Musayambe kudzitama nkhondo isanayambe ngati kuti mwapambana kale nkhondoyo.’”+ 12  Beni-hadadi anamva mawu amenewa pamene iye ndi mafumu amene anali naye ankamwa mowa mʼmatenti. Nthawi yomweyo, anauza antchito ake kuti: “Konzekerani nkhondo!” Choncho iwo anakonzekera kukamenyana ndi anthu amumzindawo. 13  Koma mneneri wina anapita kwa Ahabu+ mfumu ya Isiraeli nʼkumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Kodi waona chigulu chonsechi? Anthu onsewa ndiwapereka mʼmanja mwako lero ndipo udziwadi kuti ine ndine Yehova.’”+ 14  Ahabu anafunsa kuti: “Adzagwiritsa ntchito ndani?” Mneneriyo anayankha kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndidzagwiritsa ntchito atumiki a akalonga oyangʼanira zigawo.’” Kenako Ahabu anafunsa kuti: “Ndani akayambitse nkhondoyo?” Mneneriyo anayankha kuti: “Inuyo.” 15  Ahabu anawerenga atumiki a akalonga oyangʼanira zigawo ndipo anakwana 232. Atamaliza, anawerenganso asilikali onse a Isiraeli ndipo analipo 7,000. 16  Iwo ananyamuka masana ndipo pa nthawiyo nʼkuti Beni-hadadi ndi mafumu ena 32 amene ankamuthandiza aja, akumwa mpaka kuledzera mʼmatenti. 17  Atumiki a akalonga oyangʼanira zigawo ndi amene anatsogola. Atangofika, Beni-hadadi anatumizako anthu ndipo anthuwo atabwerera anamuuza kuti: “Kwabwera anthu ochokera ku Samariya.” 18  Iye atamva anati: “Kaya abwerera mtendere kapena nkhondo, abweretseni amoyo.” 19  Koma atumiki a akalonga oyangʼanira zigawo komanso asilikali amene ankabwera mʼmbuyo mwawo atangotuluka mumzinda, 20  aliyense anayamba kupha mdani wake. Asiriyawo anayamba kuthawa+ ndipo Aisiraeli anawathamangitsa. Koma Beni-hadadi mfumu ya Siriya anathawa atakwera hatchi, pamodzi ndi amuna ena okwera pamahatchi. 21  Mfumu ya Isiraeli inapitiriza kuwatsatira nʼkumapha mahatchi ndi kuwononga magaleta awo ndipo inapha Asiriya ambiri. 22  Kenako mneneri uja+ anapita kwa mfumu ya Isiraeli nʼkunena kuti: “Pitani, kalimbitseni asilikali anu ankhondo ndi kuganizira zomwe mudzachite,+ chifukwa kumayambiriro kwa chaka chamawa mfumu ya Siriya idzabweranso kudzamenyana nanu.”+ 23  Atumiki a mfumu ya Siriya anauza mfumuyo kuti: “Mulungu wawo ndi Mulungu wa mapiri, nʼchifukwa chake anatigonjetsa. Koma ngati titamenyana nawo pamalo afulati tikhoza kuwagonjetsa. 24  Komanso muchite izi: Muchotse mafumu onse+ pa maudindo awo ndipo muike abwanamkubwa mʼmalo mwawo. 25  Kenako musonkhanitse asilikali ndipo chiwerengero chawo chikhale chofanana ndi cha asilikali amene anafa aja. Chiwerengero cha mahatchi ndi magaleta chikhalenso chofanana ndi choyamba chija. Tikatero tikamenyane nawo pamalo afulati ndipo ndithu tikawagonjetsa.” Choncho mfumuyo inamvera malangizo awo ndipo inachitadi zimenezo. 26  Kumayambiriro kwa chaka, Beni-hadadi anasonkhanitsa Asiriya nʼkupita ku Afeki+ kuti akamenyane ndi Aisiraeli. 27  Nawonso Aisiraeli anasonkhana pamodzi ndipo anatenga zonse zofunikira nʼkupita kukakumana nawo. Aisiraeliwo atamanga msasa kutsogolo kwa Asiriya ankangooneka ngati timagulu tiwiri ta mbuzi, pamene Asiriyawo anadzaza dera lonselo.+ 28  Kenako munthu wa Mulungu woona uja anapita kwa mfumu ya Isiraeli nʼkunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Popeza Asiriya anena kuti: “Yehova ndi Mulungu wa mapiri, osati Mulungu wa zigwa,” ndipereka chigulu chonsechi mʼmanja mwako+ ndipo anthu inu mudziwadi kuti ine ndine Yehova.’”+ 29  Magulu awiriwa anakhala moyangʼanizana mʼmisasa kwa masiku 7. Pa tsiku la 7 nkhondo inayambika ndipo Aisiraeli anapha asilikali oyenda pansi a Asiriya okwana 100,000 tsiku limodzi. 30  Asilikali otsalawo anathawira mumzinda wa Afeki+ ndipo khoma linagwera 27,000 mwa asilikali amenewa. Nayenso Beni-hadadi anathawa nʼkukafika mumzindawo ndipo anakabisala mʼchipinda chamkati. 31  Ndiyeno atumiki ake anamuuza kuti: “Tamva kuti mafumu a nyumba ya Isiraeli amakhala achifundo.* Tiyeni tivale ziguduli mʼchiuno nʼkumanga zingwe kumutu ndipo tipite kwa mfumu ya Isiraeli. Mwina sikakuphani.”+ 32  Choncho anavala ziguduli mʼchiuno nʼkumanga zingwe kumutu kwawo. Atatero anapita kwa mfumu ya Isiraeli nʼkunena kuti: “Kapolo wanu Beni-hadadi akupempha kuti, ‘Chonde musandiphe.’” Ahabu anati: “Kodi adakali ndi moyo? Amene ujatu ndi mʼbale wanga.” 33  Anthuwo anaona kuti chimenechi ndi chizindikiro choti zinthu zikhala bwino, ndipo nthawi yomweyo anaona kuti mfumuyo ikunenadi zochokera mumtima. Choncho anati: “Beni-hadadi ndi mʼbale wanu.” Ahabu atamva zimenezi anati: “Pitani mukamutenge.” Choncho Beni-hadadi anabwera kwa Ahabu ndipo Ahabu anauza anthu kuti akweze Beni-hadadi mʼgaleta. 34  Beni-hadadi anauza Ahabu kuti: “Ndibweza mizinda imene bambo anga analanda bambo anu ndipo mukhoza kukhazikitsa misika* ku Damasiko ngati mmene bambo anga anachitira ku Samariya.” Ahabu anayankha kuti: “Tikapanga pangano loti zikhaladi chonchi, ndikusiya kuti uzipita kwanu.” Atatero anachita naye pangano ndipo anamusiya kuti azipita. 35  Munthu wina yemwe anali mmodzi wa ana a aneneri,*+ pomvera mawu a Yehova anauza mnzake kuti: “Ndimenye!” Koma mnzakeyo anakana. 36  Choncho mneneriyo anauza mnzakeyo kuti: “Chifukwa sunamvere mawu a Yehova, tikasiyana mkango ukupha.” Atasiyana, mkango unabwera nʼkumupha mnzakeyo. 37  Ndiyeno anapita kwa munthu wina nʼkumuuza kuti: “Ndimenye!” Munthuyo anamʼmenyadi mpaka kumuvulaza. 38  Kenako mneneriyo anakaima mʼmbali mwa msewu nʼkumadikirira mfumu ija ndipo anali atadzimanga kansalu kumaso kuti asadziwike. 39  Pamene mfumu inkadutsa, mneneriyo anauza mfumuyo kuti: “Ine mtumiki wanu ndinapita pakatikati pa nkhondo. Kenako munthu wina anabwera nʼkundisungitsa munthu ndipo anandiuza kuti, ‘Uyangʼanire munthu uyu. Akangosowa, moyo wako ulowa mʼmalo mwa moyo wake,+ apo ayi ulipira siliva wolemera talente* imodzi.’ 40  Koma ine mtumiki wanu nditatanganidwa ndi zina, mwadzidzidzi munthu uja anasowa.” Pamenepo mfumu ya Isiraeliyo inamuuza kuti: “Chiweruzo chako nʼchomwecho. Wagamula wekha.” 41  Nthawi yomweyo, mneneriyo anachotsa kansalu kamene kanali kumaso kwake kaja, ndipo mfumu ya Isiraeliyo inamuzindikira kuti anali mmodzi wa aneneri.+ 42  Mneneriyo anauza mfumuyo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Chifukwa sunaphe munthu amene ndinanena kuti ayenera kuphedwa,+ moyo wako ulowa mʼmalo mwa moyo wake+ ndipo anthu ako alowa mʼmalo mwa anthu ake.’”+ 43  Mfumu ya Isiraeliyo itamva zimenezi, inanyamuka nʼkumapita kunyumba kwake ku Samariya+ ili yachisoni ndiponso yokhumudwa.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amakhala ndi chikondi chokhulupirika.”
Kapena kuti, “kukhazikitsa misewu.”
Mawu akuti “ana a aneneri” mwina akutanthauza sukulu yopereka malangizo kwa aneneri, kapena kagulu ka aneneri.
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.