1 Mafumu 21:1-29
21 Kenako panachitika nkhani yokhudza munda wa mpesa wa Naboti wa ku Yezereeli. Mundawu unali ku Yezereeli,+ pafupi ndi nyumba yachifumu ya Ahabu mfumu ya Samariya.
2 Ahabu anauza Naboti kuti: “Ndipatse munda wako wa mpesawu kuti ndizilimamo masamba, chifukwa uli pafupi ndi nyumba yanga. Mʼmalo mwa munda wakowu ndikupatsa munda wina wa mpesa, wabwino kuposa umenewu. Kapena ngati ungafune, ndiugula ndi ndalama.”
3 Koma Naboti anayankha Ahabu kuti: “Ndikaiona nkhaniyi mmene Yehova akuionera, nʼkosayenera kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga.”+
4 Choncho Ahabu analowa mʼnyumba mwake ali wachisoni ndiponso wokhumudwa chifukwa cha zimene Naboti wa ku Yezereeli anamuuza kuti: “Sindikupatsani cholowa cha makolo anga.” Ndiyeno anakagona pabedi lake nʼkuyangʼana kukhoma ndipo anakana kudya.
5 Kenako mkazi wake Yezebeli+ anabwera nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani simukusangalala komanso mukukana kudya?”
6 Ahabu anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chakuti ndinauza Naboti wa ku Yezereeli kuti, ‘Ndigulitse munda wako wa mpesa. Kapena ngati ukufuna, ndikupatsa munda wina wa mpesa mʼmalo mwa umenewu.’ Koma wandiyankha kuti, ‘Sindingakupatseni munda wanga wa mpesawu.’”
7 Ndiyeno Yezebeli anamuuza kuti: “Kodi siinu amene mukulamulira Aisiraeli? Dzukani mudye ndipo musangalale. Ineyo ndikupatsani munda wa mpesa wa Naboti wa ku Yezereeli.”+
8 Choncho Yezebeli analemba makalata mʼdzina la Ahabu nʼkuwadinda ndi chidindo cha Ahabu.+ Kenako anatumiza makalatawo kwa akulu+ ndi anthu olemekezeka amumzinda umene Naboti ankakhala.
9 Mʼmakalatawo analembamo kuti: “Uzani anthu kuti asale kudya ndipo Naboti mumuike kutsogolo kwa anthu onse.
10 Ndiyeno mupeze anthu awiri opanda pake adzakhale kutsogolo kwake nʼkupereka umboni wotsutsana naye.+ Adzanene kuti, ‘Iwe wanyoza Mulungu ndi mfumu!’+ Kenako mukamutulutse kunja nʼkumuponya miyala kuti afe.”+
11 Choncho amuna a mumzinda umene Naboti ankakhala, akulu ndi anthu olemekezeka amumzindawo, anachita mogwirizana ndi zimene zinali mʼmakalata amene Yezebeli anawatumizira.
12 Iwo anauza anthu kuti asale kudya ndipo anaika Naboti kutsogolo kwa anthuwo.
13 Kenako amuna awiri opanda pake anabwera nʼkukhala kutsogolo kwa Naboti. Ndiyeno anayamba kupereka umboni wotsutsana ndi Naboti pamaso pa anthuwo. Iwo ananena kuti: “Naboti wanyoza Mulungu ndi mfumu!”+ Atatero anapita naye kunja kwa mzindawo nʼkukamuponya miyala mpaka kufa.+
14 Kenako anatumiza uthenga kwa Yezebeli wakuti: “Naboti waponyedwa miyala ndipo wafa.”+
15 Yezebeli atangomva kuti Naboti waponyedwa miyala ndipo wafa, anauza Ahabu kuti: “Pitani mukatenge munda wa mpesa wa Naboti wa ku Yezereeli+ umene anakana kukugulitsani uja, chifukwa Naboti panopa wafa.”
16 Ahabu atangomva kuti Naboti wafa, anapita kukatenga munda wa mpesa wa Naboti wa ku Yezereeli kuti ukhale wake.
17 Koma Yehova anauza Eliya+ wa ku Tisibe kuti:
18 “Pita ku Samariya+ ukakumane ndi Ahabu mfumu ya Isiraeli. Iye ali mʼmunda wa mpesa wa Naboti ndipo akufuna kutenga mundawo kuti ukhale wake.
19 Ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi wapha munthu+ nʼkutenganso munda wake?”’+ Ukamuuzenso kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pamalo amene agalu ananyambita magazi a Naboti, pamalo omwewo agalu adzanyambitanso magazi ako.”’”+
20 Ndiyeno Ahabu anafunsa Eliya kuti: “Wandipeza kodi mdani wanga?”+ Eliya anayankha kuti: “Inde ndakupezani. Mulungu wanena kuti, ‘Chifukwa watsimikiza mtima kuti uchite zoipa pamaso pa Yehova,+
21 ndikubweretsera tsoka ndipo ndidzaseseratu nyumba yako ndi kupha mwamuna* aliyense wa mʼbanja la Ahabu,+ ngakhalenso ooneka onyozeka ndi ofooka mu Isiraeli.+
22 Komanso ndidzachititsa nyumba yako kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati ndiponso nyumba ya Basa+ mwana wa Ahiya, chifukwa chakuti wandikwiyitsa ndiponso wachititsa kuti Aisiraeli achimwe.’
23 Komanso ponena za Yezebeli, Yehova wanena kuti, ‘Agalu adzamudya Yezebeli mʼmunda wa ku Yezereeli.+
24 Munthu aliyense wa mʼbanja la Ahabu wofera mumzinda, agalu adzamudya ndipo wofera kutchire, mbalame zidzamudya.+
25 Palibenso munthu wina amene anatsimikiza mumtima mwake kuchita zoipa pamaso pa Yehova ngati Ahabu.+ Mkazi wake Yezebeli anamulimbikitsa kuchita zimenezo.+
26 Ahabu anachita zinthu zonyansa kwambiri polambira mafano onyansa* ngati mmene Aamori onse anachitira, amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa Aisiraeli.’”+
27 Ahabu atangomva mawu amenewa, anangʼamba zovala zake nʼkuvala chiguduli. Iye anayamba kusala kudya, kugona pachiguduli ndipo ankayenda mwachisoni.
28 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Eliya wa ku Tisibe kuti:
29 “Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga?+ Chifukwa wadzichepetsa pamaso panga, sindidzabweretsa tsokali iye adakali moyo. Mʼmalomwake, ndidzalibweretsa kwa anthu a mʼnyumba yake mʼnthawi ya mwana wake.”+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wokodzera khoma.” Amenewa ndi mawu onyoza a Chiheberi otanthauza mwamuna.
^ Mawu ake a Chiheberi amatanthauzanso “ndowe,” ndipo amagwiritsidwa ntchito ngati mawu onyoza.