1 Mbiri 10:1-14
-
Imfa ya Sauli ndi ana ake (1-14)
10 Afilisiti anayamba kumenyana ndi Aisiraeli ndipo asilikali a Isiraeli ankathawa moti ambiri anaphedwa mʼphiri la Giliboa.+
2 Afilisiti anayandikira kwambiri Sauli ndi ana ake ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Malikisuwa,+ ana a Sauli.
3 Nkhondo inamukulira kwambiri Sauli, moti kenako oponya mivi ndi uta anamupeza nʼkumuvulaza.+
4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako undibaye kuti anthu osadulidwawa asandipeze nʼkundipha mwankhanza.”+ Koma womunyamulira zidayo sankafuna chifukwa ankachita mantha kwambiri. Choncho Sauli anatenga lupanga lake nʼkuligwera.+
5 Womunyamulira zidayo ataona kuti Sauli wafa, nayenso anagwera lupanga lake nʼkufa.
6 Choncho Sauli ndi ana ake atatu anafa ndipo anthu onse amʼnyumba yake anafera limodzi.+
7 Aisiraeli onse amene anali mʼchigwa ataona kuti aliyense wathawa komanso Sauli ndi ana ake afa, anayamba kuthawa mʼmizinda yawo. Kenako Afilisiti anabwera nʼkuyamba kukhala mʼmizindayo.
8 Tsiku lotsatira, Afilisiti atabwera kudzatenga zinthu za anthu amene anaphedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa paphiri la Giliboa.+
9 Iwo anamuvula Sauli zida zake nʼkumudula mutu. Kenako anauza anthu mʼdziko lonse la Afilisiti kuti afalitse uthengawu kwa mafano awo+ ndiponso kwa anthu onse.
10 Kenako anakaika zida zakezo mʼnyumba* ya mulungu wawo ndipo mutu wake anaumangirira kunyumba ya Dagoni.+
11 Anthu onse a ku Yabesi+ ku Giliyadi anamva zonse zimene Afilisiti anamuchita Sauli.+
12 Ndiyeno asilikali onse anapita kukanyamula mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake nʼkupita nayo ku Yabesi. Atatero anakwirira mafupa a anthuwo pansi pa mtengo waukulu ku Yabesiko.+ Kenako anasala kudya masiku 7.
13 Choncho Sauli anafa chifukwa chakuti anasonyeza kuti ndi wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanamvere mawu a Yehova+ komanso anapita kukafunsa kwa wolankhula ndi mizimu+
14 mʼmalo mofunsa kwa Yehova. Choncho iye anamupha nʼkupereka ufumuwo kwa Davide mwana wa Jese.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mʼkachisi.”