1 Mbiri 13:1-14
13 Davide anakambirana ndi atsogoleri a anthu 1,000 ndi a anthu 100 ndiponso mtsogoleri aliyense.+
2 Kenako anauza gulu lonse la Isiraeli kuti: “Ngati mukuona kuti ndi bwino ndiponso ngati zili zovomerezeka kwa Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kwa abale athu mʼmadera onse a Isiraeli. Uthengawu upitenso kwa ansembe ndi Alevi mʼmizinda yawo yonse+ yokhala ndi malo odyetserako ziweto, kuti abwere kuno.
3 Ndiyeno tikatenge Likasa+ la Mulungu wathu nʼkubwera nalo kuno.” Ananena zimenezi chifukwa mʼmasiku a Sauli likasalo silinkasamalidwa.+
4 Gulu lonse linagwirizana nazo, chifukwa onse anaona kuti ndi bwino kutero.
5 Choncho Davide anasonkhanitsa Aisiraeli onse kuchokera kumtsinje* wa Iguputo mpaka kukafika polowera ku Lebo-hamati,*+ kuti akatenge Likasa la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu.+
6 Davide ndi Aisiraeli onse anapita ku Baala,+ ku Kiriyati-yearimu, amene ali mʼdera la Yuda kukatenga Likasa la Mulungu woona, Yehova, amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+ Pa Likasa limeneli, anthu amaitanirapo dzina lake.
7 Koma iwo ananyamulira Likasa la Mulungu woonalo pangolo yatsopano+ kuchokera kunyumba ya Abinadabu. Uza ndi Ahiyo ndi amene ankatsogolera ngoloyo.+
8 Davide ndi Aisiraeli onse ankasangalala kwambiri pamaso pa Mulungu woona. Iwo ankaimba nyimbo ndi azeze, zoimbira zina za zingwe, maseche,+ zinganga+ ndi malipenga.+
9 Koma atafika kumalo opunthira mbewu a Kidoni, Uza anatambasula dzanja lake nʼkugwira Likasalo, chifukwa ngʼombe zinatsala pangʼono kuligwetsa.
10 Zitatero Yehova anakwiyira kwambiri Uza ndipo anamupha chifukwa anatambasula dzanja lake nʼkugwira Likasa,+ moti Uza anafera pomwepo pamaso pa Mulungu.+
11 Koma Davide anakwiya* chifukwa Yehova anakwiyira kwambiri Uza. Malo amenewa amadziwika ndi dzina lakuti Perezi-uza* mpaka lero.
12 Choncho Davide anachita mantha kwambiri ndi Mulungu woona tsiku limenelo ndipo anati: “Ndiye ndilitenga bwanji Likasa la Mulungu woona nʼkupita nalo kumene ine ndikukhala?”+
13 Davide sanatenge Likasalo kupita nalo kumene ankakhala, ku Mzinda wa Davide. Mʼmalomwake iye analamula kuti lipite kunyumba ya Obedi-edomu wa ku Gati.*
14 Likasa la Mulungu woona linakhala kunyumba ya Obedi-edomu kwa miyezi itatu ndipo Yehova ankadalitsa banja la Obedi-edomu komanso zonse zimene anali nazo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “kuchokera ku Sihori.”
^ Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
^ Mabaibulo ena amati, “pakati.”
^ Kapena kuti, “anakhumudwa.”
^ Kutanthauza “Kukwiyira kwambiri Uza.”
^ Mawu akuti “Gati” mwina akunena za mzinda wa Gati-rimoni.