1 Mbiri 14:1-17
14 Hiramu+ mfumu ya Turo anatumiza anthu oti akapereke uthenga kwa Davide. Anatumizanso matabwa a mkungudza, anthu oswa miyala ndi kumanga makoma ndiponso akalipentala kuti akamangire Davide nyumba.*+
2 Davide anadziwa kuti Yehova wachititsa kuti ufumu wake ukhazikike mu Isiraeli,+ popeza ufumu wakewo unakwezedwa kwambiri chifukwa cha anthu a Mulungu, Aisiraeli.+
3 Ku Yerusalemu, Davide anakwatiranso akazi ena+ ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.+
4 Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu mayina awo+ ndi awa: Samuwa, Sobabu, Natani,+ Solomo,+
5 Ibara, Elisua, Elipeleti,
6 Noga, Nefegi, Yafiya,
7 Elisama, Beliyada ndi Elifeleti.
8 Afilisiti atamva kuti Davide amudzoza kukhala mfumu ya Aisiraeli onse,+ Afilisiti onse anabwera kudzafunafuna Davide.+ Davide atamva zimenezi, anapita kukamenyana nawo.
9 Kenako Afilisitiwo anayamba kuukira anthu okhala mʼchigwa cha Arefai.+
10 Ndiyeno Davide anafunsira kwa Mulungu kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anauza Davide kuti: “Pita, amenewa ndiwaperekadi mʼmanja mwako.”+
11 Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu+ ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Ndiyeno Davide anati: “Mulungu woona wawononga adani anga ngati madzi achigumula pogwiritsa ntchito dzanja langa.” Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Baala-perazimu.*
12 Afilisiti anasiya milungu yawo kumeneko ndipo Davide atalamula, milunguyo anaitentha pamoto.+
13 Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso nʼkuyamba kuukira anthu okhala mʼchigwacho.+
14 Ndiyeno Davide anafunsiranso kwa Mulungu ndipo Mulungu woonayo anamuyankha kuti: “Usapite kukakumana nawo. Uwazembere kumbuyo nʼkuwaukira kutsogolo kwa zitsamba za baka.*+
15 Ndiyeno ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za bakazo, ukatuluke nʼkuyamba kumenyana nawo chifukwa Mulungu woona adzakhala atatsogola kukapha asilikali a Afilisiti.”+
16 Choncho Davide anachitadi zimene Mulungu woona anamulamula,+ moti iwo anapha asilikali a Afilisiti kuchokera ku Gibiyoni mpaka ku Gezeri.+
17 Davide anatchuka mpaka mbiri yake inamveka kumayiko onse ndipo Yehova anachititsa kuti anthu a mitundu yonse azimuopa Davideyo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
^ Kutanthauza, “Ambuye wa Zigumula.”
^ Dzina lakuti “baka” ndi lochokera ku Chiheberi. Chitsamba chimenechi sichikudziwika kuti chinali chotani.