Kalata Yoyamba ya Petulo 3:1-22
3 Mofanana ndi zimenezi, inu akazi muzigonjera amuna anu+ kuti ngati safuna kumvera Mawu a Mulungu, akopeke ndi khalidwe lanu, osati ndi mawu anu+
2 koma chifukwa choti aona khalidwe lanu labwino*+ komanso ulemu wanu waukulu.
3 Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa kunja kokha monga kumanga tsitsi, kuvala zodzikongoletsera zagolide+ kapena zovala zapamwamba.
4 Koma kukhalenso kwa munthu wobisika mumtima, atavala zovala zosawonongeka, zomwe ndi mtima wodekha komanso wofatsa+ umene ndi wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.
5 Ndi mmenenso akazi okhulupirika akale, omwe ankayembekezera Mulungu, ankadzikongoletsera. Akazi amenewa ankagonjera amuna awo.
6 Mwachitsanzo, Sara ankamvera Abulahamu ndipo ankamutchula kuti “mbuyanga.”+ Tsopano inuyo mwakhala ana ake, ndipo mukhalabe ana ake mukapitiriza kuchita zabwino komanso ngati simukuopa chilichonse.+
7 Inunso amuna, pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino. Muziwapatsa ulemu+ chifukwa akazi ali ngati chiwiya chosachedwa kusweka. Muzichita zimenezi kuti mapemphero anu asatsekerezedwe, chifukwa mudzalandira nawo limodzi moyo umene Mulungu adzakupatseni+ chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.
8 Pomaliza, nonsenu mukhale amaganizo amodzi,+ muzimverana chisoni, muzikonda abale, mukhale ndi chifundo chachikulu+ ndiponso mukhale odzichepetsa.+
9 Munthu akakuchitirani choipa musamabwezere ndi choipa,+ akakuchitirani chipongwe musamabwezere ndi chipongwe.+ Mʼmalomwake muziwachitira zabwino*+ chifukwa Mulungu anakusankhani kuti muzidalitsa ena kuti nayenso adzakudalitseni.
10 Munthu “amene amakonda moyo wake komanso amafuna kumakhala moyo wabwino, ayenera kusamala kuti asamalankhule zoipa ndi lilime lake+ ndiponso kuti asamalankhule zachinyengo ndi milomo yake.
11 Ayenera kusiya kuchita zoipa+ nʼkumachita zabwino.+ Ayeneranso kuyesetsa kumakhala mwamtendere ndi ena komanso kuulimbikitsa.+
12 Maso a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva mapemphero awo opembedzera,+ koma Yehova* amakwiyira anthu amene amachita zoipa.”+
13 Ndithudi, ndi ndani angakuchitireni zoipa mukamayesetsa kuchita zabwino?+
14 Koma ngakhale mutavutika chifukwa chochita zinthu mwachilungamo, mumakhalabe osangalala.+ Musamaope zimene amaopa* ndipo musamade nazo nkhawa.+
15 Koma muvomereze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera. Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu, koma muziwayankha mofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.+
16 Muzikhala ndi chikumbumtima chabwino,+ kuti kaya anthu akunenereni zoipa, amene akukunenerani zoipawo adzachite manyazi+ chifukwa cha khalidwe lanu labwino monga otsatira a Khristu.+
17 Ndi bwino kuvutika chifukwa chochita zabwino,+ ngati Mulungu walola kuti zimenezo zichitike, kusiyana ndi kuvutika chifukwa chochita zoipa.+
18 Pajatu ngakhale Khristu anafa kamodzi kokha kuti achotse uchimo.+ Munthu wolungamayo anafera anthu osalungama+ kuti akugwirizanitseni ndi Mulungu.+ Iye anaphedwa monga munthu,*+ koma anaukitsidwa monga mzimu.+
19 Kenako anapita kukalengeza uthenga wachiweruzo* kwa mizimu imene inali mʼndende.+
20 Mizimuyi sinamvere Mulungu pa nthawi imene ankaleza mtima mʼmasiku a Nowa.+ Pa nthawiyo, Nowa ankapanga chingalawa+ chomwe chinapulumutsa pamadzi anthu owerengeka, anthu* 8 okha basi.+
21 Tsopano ubatizo, womwe ukufanana ndi chingalawa, ukupulumutsanso inuyo (osati kungochotsa litsiro lamʼthupi, koma kupempha Mulungu kuti akupatseni chikumbumtima chabwino)+ chifukwa mumakhulupirira Yesu Khristu yemwe anaukitsidwa.
22 Iye anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu+ moti anamukweza kuti maulamuliro, mphamvu komanso angelo zikhale pansi pake.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “loyera.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mʼmalomwake muziwadalitsa.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mabaibulo ena amati, “Musamaope akamakuopsezani.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Iye anaphedwa mʼthupi.”
^ Kapena kuti, “Kenako anapita kukalalikira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “miyoyo.”