1 Samueli 16:1-23
16 Patapita nthawi, Yehova anauza Samueli kuti: “Kodi ulirira Sauli mpaka liti,+ munthu woti ine ndamukana kuti akhale mfumu ya Isiraeli?+ Thira mafuta mʼnyanga* yako+ ndipo unyamuke. Ndikutumiza kwa Jese+ wa ku Betelehemu, chifukwa ndasankha mmodzi wa ana ake aamuna kuti akhale mfumu yanga.”+
2 Koma Samueli anati: “Ndipita bwanji? Sauli akamva andipha ndithu.”+ Atatero, Yehova anamuuza kuti: “Popita utenge ngʼombe yaikazi yaingʼono ndipo ukanene kuti, ‘Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova.’
3 Ndiyeno ukaitanire Jese kopereka nsembeko, ndipo ine ndidzakuuza zochita. Ukandidzozere munthu amene ndidzakusonyeza.”+
4 Samueli anachita zimene Yehova anamuuza. Atafika ku Betelehemu,+ akulu a mzindawo anayamba kunjenjemera atakumana naye ndipo anamufunsa kuti: “Kodi nʼkwabwino?”
5 Iye anayankha kuti: “Inde, nʼkwabwino. Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. Dziyeretseni, ndipo tipite limodzi kopereka nsembe.” Kenako iye anayeretsa Jese ndi ana ake ndipo anawaitanira kopereka nsembe.
6 Pamene iwo ankalowa, Samueli anaona Eliyabu+ ndipo anati: “Sindikukayikira, Yehova wasankha ameneyu.”*
7 Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaganizire mmene akuonekera komanso kutalika kwake+ chifukwa ine ndamukana ameneyu. Chifukwatu mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera. Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mumtima.”+
8 Kenako Jese anaitana Abinadabu+ kuti Samueli amuone, koma Samueli anati: “Yehova sanasankhenso ameneyu.”
9 Kenako Jese anaitana Shama,+ koma Samueli anati: “Ameneyunso Yehova sanamusankhe.”
10 Choncho Jese anaitana ana ake 7 kuti Samueli awaone. Koma Samueli anauza Jese kuti: “Yehova sanasankhe aliyense wa amenewa.”
11 Kenako Samueli anafunsa Jese kuti: “Kodi anyamata anu onse ndi omwewa basi?” Iye anayankha kuti: “Wamngʼono kwambiri+ wachokapo. Wapita koweta nkhosa.”+ Zitatero Samueli anauza Jese kuti: “Tumizani munthu akamutenge, chifukwa sitikhala pansi kuti tidye mpaka iye atabwera.”
12 Iye anatumadi munthu kukamʼtenga. Mnyamatayo anali wa maso okongola ndiponso wooneka bwino.+ Ndiyeno Yehova anati: “Ndi ameneyu! Nyamuka umudzoze.”+
13 Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ nʼkumudzoza azichimwene ake akuona. Kuyambira tsiku limenelo, mzimu wa Yehova unayamba kuthandiza Davide.+ Kenako Samueli anabwerera ku Rama.+
14 Ndiyeno mzimu wa Yehova unamʼchokera Sauli,+ ndipo Yehova analola kuti maganizo oipa* azimuvutitsa Sauli.+
15 Atumiki a Sauli anamuuza kuti: “Tikuona kuti mzimu woipa wochokera kwa Mulungu ukukuvutitsani.
16 Mbuye wathu, uzani atumiki anu kuti akupezereni katswiri woimba zeze.+ Mzimu woipa wochokera kwa Mulungu ukakubwererani, iye azikuimbirani zeze ndipo inu muzimva bwino.”
17 Choncho Sauli anauza atumiki ake kuti: “Ndipezereni munthu wodziwa kuimba, ndipo mubwere naye kuno.”
18 Mmodzi wa atumikiwo ananena kuti: “Ine ndinaona mwana wa Jese wa ku Betelehemu akuimba, ndipo amaimba mwaluso. Iye ndi mwamuna wolimba mtima ndiponso msilikali wamphamvu.+ Ndiwodziwa kulankhula, wooneka bwino+ komanso Yehova ali naye.”+
19 Sauli atamva zimenezi, anatumiza uthenga kwa Jese wakuti: “Nditumizire mwana wako Davide amene amaweta nkhosa.”+
20 Choncho Jese anatenga mkate, thumba lachikopa la vinyo ndi mwana wa mbuzi nʼkuziika pa bulu kuti mwana wake Davide apite nazo kwa Sauli.
21 Davide anapita kwa Sauli nʼkuyamba kumutumikira.+ Sauli anamʼkonda kwambiri Davide, moti anakhala womunyamulira zida.
22 Zitatero, Sauli anatumiza uthenga kwa Jese, wakuti: “Ndikupempha kuti Davide apitirize kunditumikira chifukwa ndamʼkonda.”
23 Ndiyeno maganizo oipa* akamubwerera Sauli, Davide ankatenga zeze nʼkumuimbira. Akatero, Sauli ankamva bwino ndipo maganizo oipawo ankamuchokera.+
Mawu a M'munsi
^ Kalelo anthu ankagwiritsa ntchito nyanga ya nkhosa, mbuzi kapena ngʼombe ngati botolo.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wodzozedwa wa Yehova waonekera pamaso pake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu woipa wochokera kwa Mulungu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu woipa wochokera kwa Mulungu.”