1 Samueli 9:1-27

  • Samueli anakumana ndi Sauli (1-27)

9  Panali mwamuna wina wochokera kudera la Benjamini dzina lake Kisi,+ mwana wa Abiyeli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya. Iye anali wa fuko la Benjamini+ ndipo anali wolemera kwambiri. 2  Anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Sauli+ ndipo anali mnyamata wooneka bwino. Mu Isiraeli munalibe mwamuna wooneka bwino kuposa iyeyu. Komanso Sauli anali wamʼtali kwambiri moti panalibe munthu aliyense amene ankapitirira mʼmapewa ake. 3  Ndiyeno abulu* a Kisi atasowa, Kisi anauza mwana wake Sauli kuti: “Tenga wantchito mmodzi ndipo mupite mukafunefune abulu.” 4  Ndiyeno anayendayenda mʼdera lamapiri la Efuraimu mpaka kukafika mʼdera la Salisa, koma abuluwo sanawapeze. Atatero anafika mʼdera la Saalimu ndipo kumenekonso sanawapeze. Anafufuza dera lonse la Benjamini koma sanawapeze. 5  Atafika mʼdera la Zufi, Sauli anauza wantchito wake uja kuti: “Tiye tibwerere kunyumba, chifukwa bambo anga angasiye kuganizira za abulu nʼkuyamba kutidera nkhawa ifeyo.”+ 6  Koma iye anayankha kuti: “Mumzinda uwo muli munthu wa Mulungu ndipo anthu amamulemekeza. Zonse zimene wanena zimachitika.+ Bwanji tipite kumeneko, mwina angakatiuze kumene tingalowere.” 7  Koma Sauli anafunsa wantchito wakeyo kuti: “Tikapita kumeneko tikamʼpatsa chiyani? Tilibe chakudya chilichonse kapena mphatso yoti tikamʼpatse munthu wa Mulungu woonayo. Nanga tili ndi chilichonse ngati?” 8  Wantchitoyo anauza Sauli kuti: “Ndili ndi siliva* woti ndingakapatse munthu wa Mulungu woonayo ndipo akatiuza kumene tingalowere.” 9  (Kalekale mu Isiraeli, munthu akafuna kukafunsira kwa Mulungu ankanena kuti: “Tiyeni tipite kwa wamasomphenya.”+ Chifukwa kalelo mneneri ankatchedwa wamasomphenya.) 10  Kenako Sauli anauza wantchito wakeyo kuti: “Maganizo abwino. Tiye tipite.” Choncho anapita kumzinda kumene kunali munthu wa Mulungu woonayo. 11  Pamene ankakwera mtunda kuti akalowe mumzindawo, anakumana ndi atsikana akupita kukatunga madzi, ndipo anawafunsa kuti: “Kodi wamasomphenya+ ali mumzindawu?” 12  Iwo anawayankha kuti: “Inde, alipo. Ali kumene mukuloweraku. Fulumirani, wafika lero lomwe mumzindawu chifukwa lero anthu akupereka nsembe+ pamalo okwezeka.+ 13  Mukangolowa mumzinda, mumʼpeza asanapite kukadya kumalo okwezeka. Anthu sangayambe kudya pokhapokha iye atafika, chifukwa iyeyo ndi amene amadalitsa nsembeyo. Akatero oitanidwa amadya. Ndiye pitani musachedwe, mumʼpeza.” 14  Choncho anapita kukalowa mumzindawo. Atatsala pangʼono kufika pakati pa mzindawo, anangoona Samueli akubwera kudzakumana nawo kuti apite kumalo okwezeka. 15  Dzulo lake, Sauli asanafike, Yehova anali atauziratu* Samueli kuti: 16  “Mawa cha nthawi ngati ino ndidzakutumizira munthu kuchokera kudera la Benjamini.+ Udzamudzoze kuti akhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.+ Iye adzapulumutsa anthu anga mʼmanja mwa Afilisiti, chifukwa ndaona mmene akuvutikira ndiponso ndamva kulira kwawo.”+ 17  Samueli ataona Sauli, Yehova anamuuza kuti: “Munthu amene ndinakuuza uja ndi ameneyu. Uja ndinati, ‘Ndi amene adzalamulire anthu anga.’”+ 18  Kenako Sauli anakumana ndi Samueli pageti ndipo anati: “Ndifunse nawo, kodi nyumba ya wamasomphenya ili kuti?” 19  Samueli anayankha Sauli kuti: “Wamasomphenyayo ndineyo. Tiyeni tsogolani tipite kumalo okwezeka ndipo mudya ndi ine lero.+ Ndidzakulolani kupita kwanu mawa mʼmawa ndipo ndikuuzani zonse zimene mukufuna kudziwa.* 20  Koma musadandaule za abulu amene anasowa masiku atatu apitawo+ chifukwa anapezeka. Ndipo kodi zabwino zonse mu Isiraeli ndi za ndani? Mmesa ndi zako ndi anthu onse amʼnyumba ya bambo ako?”+ 21  Sauli anayankha kuti: “Kodi ine si wa fuko la Benjamini, lomwe ndi lalingʼono kwambiri pa mafuko onse a Isiraeli?+ Ndipo kodi banja lathu si lalingʼono kwambiri pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Ndiye nʼchifukwa chiyani mukundilankhula chonchi?” 22  Ndiyeno Samueli anatenga Sauli ndi wantchito wake nʼkupita nawo mʼchipinda chodyera. Atafika, anawapatsa malo apamwamba kuposa oitanidwa ena onse. Mʼchipindamo munali anthu pafupifupi 30. 23  Kenako Samueli anauza wophika kuti: “Bweretsa nyama ndinakupatsa ija, imene ndinakuuza kuti usunge ija.” 24  Wophikayo anatenga mwendo wonse nʼkumupatsa Sauli. Kenako Samueli anati: “Nyama imene inasungidwa ndi imeneyi. Idya. Anasungira iweyo kuti udye pa nthawi ya mwambowu chifukwa ndinawauza kuti, ‘Ndaitana alendo.’” Choncho Sauli anadyera limodzi ndi Samueli pa tsikulo. 25  Zitatero, anatsika pamalo okwezeka+ aja nʼkupita mumzinda ndipo Samueli anapitiriza kulankhula ndi Sauli ali padenga la nyumba. 26  Samueli ndi Sauli anadzuka mʼmawa kwambiri ndipo mʼbandakucha, Samueli ali padenga la nyumba, anaitana Sauli nʼkumuuza kuti: “Konzeka ndikuperekeze.” Choncho Sauli anakonzeka ndipo iyeyo ndi Samueli anatuluka panja. 27  Pamene ankayandikira chakumapeto kwa mzindawo, Samueli anauza Sauli kuti: “Muuze wantchito wakoyu+ atsogole, koma iweyo uime kaye kuti ndikuuze mawu a Mulungu.” Atatero, wantchitoyo anatsogola.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “abulu aakazi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kota ya sekeli ya siliva.” Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anali atamutsegula khutu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zonse zimene zili mumtima mwanu.”