Kalata Yoyamba Yopita kwa Timoteyo 2:1-15

  • Kupempherera anthu osiyanasiyana (1-7)

    • Mulungu mmodzi, mkhalapakati mmodzi (5)

    • Dipo lokwanira ndendende (6)

  • Malangizo kwa amuna ndi akazi (8-15)

2  Choyamba, ndikulimbikitsa anthu onse kuti azipemphera, kupereka mapembedzero, kupemphererana ndiponso kupereka mapemphero oyamika Mulungu mʼmalo mwa anthu osiyanasiyana. 2  Komanso mʼmalo mwa mafumu ndi anthu onse audindo wapamwamba,+ kuti tipitirize kukhala mwabata ndiponso mwamtendere komanso odzipereka kwambiri kwa Mulungu ndi oganiza bwino.+ 3  Zimenezi ndi zabwino ndiponso zovomerezeka kwa Mulungu, yemwe ndi Mpulumutsi wathu,+ 4  amene amafuna kuti anthu osiyanasiyana apulumuke+ nʼkukhala odziwa choonadi molondola. 5  Chifukwa pali Mulungu mmodzi+ ndiponso mkhalapakati mmodzi+ pakati pa Mulungu ndi anthu.+ Mkhalapakatiyu ndi Khristu Yesu,+ munthu 6  amene anadzipereka kuti akhale dipo* la anthu onse lokwanira ndendende.+ Zimenezi ndi zimene zidzachitiridwe umboni pa nthawi yake. 7  Chifukwa cha umboni umenewu,+ ine ndinasankhidwa kuti ndikhale mlaliki ndi mtumwi.+ Ndikunenatu zoona, sindikunama ayi. Ndinasankhidwa kuti ndiziphunzitsa anthu a mitundu ina+ za chikhulupiriro ndi choonadi. 8  Choncho, ndikufuna kuti kulikonse amuna apitirize kupemphera. Azikweza manja mʼmwamba mokhulupirika kwa Mulungu,+ popanda kukwiya+ ndi kutsutsana.+ 9  Nawonso akazi ayenera kudzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu ndiponso mwanzeru osati kumangodzikongoletsa ndi masitayilo omangira tsitsi, golide, ngale, kapena zovala zamtengo wapatali.+ 10  Koma azidzikongoletsa mogwirizana ndi mmene akazi odzipereka kwa Mulungu amayenera kudzikongoletsera.+ Azidzikongoletsa ndi ntchito zabwino. 11  Pophunzira, mkazi azikhala chete ndipo azigonjera ndi mtima wonse.+ 12  Sindikulola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kulamulira mwamuna, koma azikhala chete.+ 13  Chifukwa Adamu ndi amene anayamba kupangidwa kenako Hava.+ 14  Komanso Adamu sanapusitsidwe, koma mkaziyo ndi amene anapusitsidwa+ ndipo anachimwa. 15  Komabe, mkazi adzatetezeka akabereka ana+ ngati akupitiriza kukhala ndi chikhulupiriro, chikondi komanso kukhala woyera ndiponso woganiza bwino.+

Mawu a M'munsi