Kalata Yoyamba Yopita kwa Timoteyo 3:1-16

  • Zoyenera kuti munthu akhale woyangʼanira (1-7)

  • Zoyenera kuti munthu akhale mtumiki wothandiza (8-13)

  • Chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwa Mulungu (14-16)

3  Mawu awa ndi oona: Ngati munthu akuyesetsa kuti akhale woyangʼanira,+ akufuna ntchito yabwino. 2  Choncho woyangʼanira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi, wosachita zinthu mopitirira malire, woganiza bwino,+ wochita zinthu mwadongosolo, wochereza alendo+ ndiponso wodziwa kuphunzitsa.+ 3  Asakhale munthu womwa mowa mwauchidakwa,+ kapena wankhanza,* koma wololera.+ Asakhalenso wokonda kukangana+ kapena wokonda ndalama.+ 4  Akhale mwamuna woyangʼanira bwino banja lake ndiponso woti ana ake amamumvera ndi mtima wonse.+ 5  (Ngati munthu sadziwa kuyangʼanira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?) 6  Asakhale woti wangobatizidwa kumene,*+ kuopera kuti angayambe kudzitukumula chifukwa cha kunyada nʼkulandira chiweruzo chofanana ndi chimene Mdyerekezi analandira. 7  Akhalenso ndi mbiri yabwino kwa osakhulupirira*+ kuti asanyozedwe ndi anthu komanso kukodwa mumsampha wa Mdyerekezi. 8  Nawonso atumiki othandiza akhale opanda chibwana, osanena pawiri,* osamwa vinyo wambiri ndiponso osakonda kupeza phindu mwachinyengo.+ 9  Akhale ogwira chinsinsi chopatulika cha chikhulupiriro, ali ndi chikumbumtima choyera.+ 10  Ndiponso amenewa ayesedwe kaye ngati ali oyenerera, ndipo akakhala opanda chifukwa chowanenezera angakhale atumiki.+ 11  Nawonso akazi akhale opanda chibwana, ochita zinthu mosapitirira malire, okhulupirika pa zinthu zonse+ ndipo asakhale amiseche.+ 12  Atumiki othandiza akhale amuna a mkazi mmodzi, oyangʼanira bwino ana awo ndi mabanja awo. 13  Chifukwa amuna amene amatumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino ndi ufulu waukulu wolankhula za chikhulupiriro chimene chili mwa Khristu Yesu. 14  Ndikukhulupirira kuti ndibwera posachedwa, koma ndikukulembera zimenezi 15  kuti ngati ndingachedwe, udziwe zimene uyenera kuchita mʼnyumba ya Mulungu,+ imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo. Mpingowo ndi umene umalimbikitsa ndi kuteteza choonadi. 16  Kunena zoona, chinsinsi chopatulika chokhudza kukhala odzipereka kwa Mulungu kumeneku nʼchachikulu: ‘Iye anaonekera ngati munthu,+ anaonedwa kuti ndi wolungama pamene anali mzimu,+ anaonekera kwa angelo,+ analalikidwa kwa mitundu ya anthu,+ anthu padziko lapansi anamukhulupirira+ ndiponso analandiridwa kumwamba mu ulemerero.’

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wandewu; wachiwawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wotembenuka kumene.”
Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wa Chikhristu.
Kapena kuti, “osalankhula mwachinyengo.”