Kalata Yoyamba Yopita kwa Timoteyo 5:1-25

  • Zoyenera kuchita ndi achikulire komanso achinyamata (1, 2)

  • Kuthandiza akazi amasiye (3-16)

    • Kusamalira banja (8)

  • Kulemekeza akulu akhama (17-25)

    • ‘Vinyo pangʼono, chifukwa cha vuto la mʼmimba’ (23)

5  Usadzudzule mokalipa mwamuna wachikulire,+ koma uzilankhula naye mokoma mtima ngati bambo ako. Amuna achinyamata uzilankhula nawo ngati achimwene ako 2  ndipo akazi achikulire ngati amayi ako. Akazi achitsikana uzilankhula nawo ngati achemwali ako, ndipo pochita zimenezi usakhale ndi maganizo alionse olakwika. 3  Uziganizira* akazi amasiye amene alidi amasiye.*+ 4  Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, iwowo akhale oyamba kusamalira anthu a mʼbanja lawo+ posonyeza kuti ndi odzipereka kwa Mulungu. Azibwezera kwa makolo ndi agogo awo zowayenerera+ chifukwa zimenezi zimakondweretsa Mulungu.+ 5  Mkazi amene alidi wamasiye, amene akusowa womusamalira, amadalira Mulungu+ ndipo amapitiriza kupemphera ndi kupembedzera masana ndi usiku.+ 6  Koma amene amangochita zinthu motsatira zilakolako zake, ndi wakufa ngakhale kuti ali moyo. 7  Choncho upitirize kuwapatsa malangizo* amenewa kuti asakhale ndi chifukwa chowanenezera. 8  Ndithudi, ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, makamaka a mʼbanja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.+ 9  Mkazi wamasiye wolembedwa pamndandanda wa akazi amasiye, akhale wazaka zoposa 60. Akhalenso amene anali wokhulupirika kwa mwamuna wake,* 10  wodziwika kuti anachita ntchito zabwino,+ analera bwino ana ake,+ ankachereza alendo,+ anasambitsa mapazi a oyera,+ anathandiza anthu amene anali pa mavuto+ ndiponso ankagwira modzipereka ntchito iliyonse yabwino. 11  Koma usaike akazi amasiye achitsikana pamndandanda umenewu, chifukwa ngati atengeka ndi chilakolako chofuna mwamuna mʼmalo motumikira Khristu, amasankha kukwatiwa. 12  Zikatero, amapezeka olakwa chifukwa sanasunge lonjezo lawo.* 13  Komanso amangokhala osachita kanthu nʼkumangoyendayenda mʼmakomo mwa anzawo. Kuwonjezera pa kumangokhala osachita kanthu, amakondanso miseche, kulowerera nkhani za eni+ komanso kulankhula zinthu zimene sayenera kulankhula. 14  Choncho ndingakonde kuti akazi amasiye achitsikana azikwatiwa,+ kubereka ana+ ndiponso kusamalira banja nʼcholinga choti otsutsa asatipezere chifukwa. 15  Ndipotu ena asocheretsedwa kale moti ayamba kutsatira Satana. 16  Ngati mkazi aliyense wokhulupirira ali ndi achibale amene ndi akazi amasiye, iyeyo aziwathandiza, kuti akazi amasiyewo asachititse mpingo kupanikizika. Zikatero, mpingowo ungathe kuthandiza amene alidi akazi amasiye.*+ 17  Akulu amene amatsogolera bwino+ azilemekezedwa kwambiri,+ makamaka amene amachita khama polankhula Mawu a Mulungu ndiponso kuphunzitsa.+ 18  Paja Mawu a Mulungu amati: “Usamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha* mbewu.”+ Komanso amati: “Wantchito ayenera kulandira malipiro ake.”+ 19  Usavomereze mlandu woneneza mwamuna wachikulire,* kupatulapo ngati pali mboni ziwiri kapena zitatu.+ 20  Anthu amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo,+ uziwadzudzula+ pamaso pa onse kuti ena onsewo akhale ndi mantha.* 21  Ndikukulamula mwamphamvu, pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu ndiponso angelo ochita kusankhidwa, kuti uzitsatira malangizo amenewa popanda tsankho kapena kukondera.+ 22  Usafulumire kuika munthu aliyense pa udindo,*+ kapena kugawana ndi anthu ena machimo awo. Pitiriza kukhala ndi khalidwe loyera. 23  Usamamwenso madzi,* koma uzimwa vinyo pangʼono, chifukwa cha vuto lako la mʼmimba ndiponso kudwaladwala kwako kuja. 24  Machimo a anthu ena amadziwika kwa anthu, ndipo amaweruzidwa nthawi yomweyo. Koma anthu ena, machimo awo amadzaonekera pakapita nthawi.+ 25  Nazonso ntchito zabwino zimadziwika kwa anthu,+ ndipo zimene sizidziwika sizingabisike mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Uzilemekeza.”
Kapena kuti, “akazi amasiye amene akusowadi zinthu”; kutanthauza kuti alibe owathandiza.
Kapena kuti, “malamulo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkazi wa mwamuna mmodzi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhulupiriro choyamba.”
Kapena kuti, “akazi amasiye amene akusowadi zinthu”; kutanthauza kuti alibe owathandiza.
Kapena kuti, “mkulu.”
Kapena kuti, “likhale chenjezo kwa ena onsewo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuika manja ako pa munthu.”
Kapena kuti, “Usiye kumwa madzi okha.”