Kalata Yoyamba Yopita kwa Timoteyo 6:1-21

  • Akapolo azilemekeza ambuye awo (1, 2)

  • Aphunzitsi onyenga ndiponso kukonda ndalama (3-10)

  • Malangizo kwa munthu wa Mulungu (11-16)

  • Kulemera pa ntchito zabwino (17-19)

  • Sunga zimene unalandira (20, 21)

6  Anthu onse amene ndi akapolo aziona kuti ambuye awo ndi oyenera kuwalemekeza ndi mtima wonse,+ kuti dzina la Mulungu ndiponso zimene amatiphunzitsa zisanyozedwe.+ 2  Komanso akapolo amene ambuye awo ndi Akhristu, asamawachitire zinthu mopanda ulemu poona kuti ndi abale. Mʼmalomwake, azigwira ntchito mwakhama kwambiri, chifukwa ntchito yawo yabwinoyo ikuthandiza Akhristu anzawo omwe amawakonda. Pitiriza kuphunzitsa zinthu zimenezi ndiponso kulimbikitsa anthu kuti azichita zimenezi. 3  Ngati munthu akuphunzitsa zinthu zabodza, ndipo sakuvomereza malangizo abwino+ ochokera kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndiponso zinthu zimene timaphunzira zogwirizana ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu,+ 4  munthu ameneyo ndi wodzitukumula ndiponso wonyada ndipo samvetsa kalikonse.+ Mʼmalomwake, amakonda kukangana ndiponso kutsutsana pa mawu.+ Zimenezi zimayambitsa nsanje, mikangano, kunenerana mawu achipongwe* ndiponso kuganizirana zoipa. 5  Zimachititsanso kuti anthu opotoka maganizo+ ndiponso osadziwa choonadi, azikangana pa zinthu zazingʼono poganiza kuti kukhala wodzipereka kwa Mulungu ndi njira yopezera phindu.+ 6  Nʼzoona kuti kukhala wodzipereka kwa Mulungu+ komanso kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo, ndi njira yopezera phindu lalikulu. 7  Pajatu sitinabwere ndi kanthu mʼdziko ndipo sitingachokemo ndi kanthu.+ 8  Choncho, ngati tili ndi chakudya, zovala ndi pogona, tizikhala okhutira ndi zinthu zimenezi.+ 9  Koma anthu ofunitsitsa kulemera amakumana ndi mayesero ndiponso amakodwa mumsampha.+ Iwo amalakalaka zinthu zowapweteketsa komanso amachita zinthu mopanda nzeru. Zimenezi zimawawononga ndiponso kuwabweretsera mavuto.+ 10  Chifukwa kukonda ndalama kumayambitsa* zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo chifukwa chotengeka ndi chikondi chimenechi, ena asiya chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.+ 11  Koma munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu zimenezi. Mʼmalomwake yesetsa kukhala wachilungamo, wodzipereka kwa Mulungu, wachikhulupiriro, wachikondi, wopirira ndiponso wofatsa.+ 12  Menya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro. Gwira mwamphamvu moyo wosatha umene anakuitanira. Paja unalengeza momveka bwino zokhudza moyo umenewu pamaso pa mboni zambiri. 13  Pamaso pa Mulungu, amene amathandiza kuti zinthu zonse zikhalebe zamoyo ndiponso pamaso pa Khristu Yesu, amene anapereka umboni wabwino kwambiri pamaso pa Pontiyo Pilato,+ ndikukulamula 14  kuti uzisunga malamulo. Uziwasunga uli woyera ndiponso wopanda chifukwa chokunenezera mpaka pamene Ambuye wathu Yesu Khristu adzaonekere.+ 15  Iye ndi wachimwemwe ndi Wamphamvu komanso ndi Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,+ ndipo adzaonekera pa nthawi yake. 16  Iyeyo ali ndi moyo woti sungafe+ ndipo amakhala pamalo owala kwambiri moti palibe munthu angafikepo.+ Palibenso munthu amene anamuonapo kapena amene angamuone.+ Iye apatsidwe ulemu ndipo mphamvu zake zikhalebe mpaka kalekale. Ame. 17  Ulangize* anthu achuma mʼdzikoli* kuti asakhale odzikweza, ndiponso kuti asamadalire chuma chosadalirika,+ koma azidalira Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse zomwe timasangalala nazo.+ 18  Uwauze kuti azichita zabwino, akhale olemera pa ntchito zabwino, owolowa manja komanso okonzeka kugawira ena+ 19  kuti asunge bwino chuma chochokera kwa Mulungu chomwe ndi maziko abwino a tsogolo+ lawo nʼcholinga choti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.+ 20  Timoteyo, usunge bwino zimene unalandira kwa Mulungu.+ Uzipewa nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zinthu zoyera. Uzipewanso kutsutsana pa zinthu zimene ena monama amati ndi “kudziwa zinthu.”+ 21  Chifukwa chodzionetsera ndi kudziwa zinthu kumeneku, ena asiya chikhulupiriro. Kukoma mtima kwakukulu kukhale nanu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kunenezana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi muzu wa.”
Kapena kuti, “a mʼnthawi ino.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “Ulamule.”