Kalata Yoyamba ya Yohane 3:1-24

  • Ndife ana a Mulungu (1-3)

  • Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi (4-12)

    • Yesu adzawononga ntchito za Mdyerekezi (8)

  • Muzikondana (13-18)

  • Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu (19-24)

3  Taganizirani za chikondi chachikulu chimene Atate watisonyeza+ potitchula kuti ana ake.*+ Ndipo ndifedi ana ake. Nʼchifukwa chake dziko silikutidziwa,+ popeza iyeyo silikumudziwanso.+ 2  Okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu,+ koma panopa sizinaonekerebe kuti tidzakhala otani.+ Tikudziwa kuti akadzaonekera, tidzakhala ngati iyeyo, chifukwa tidzamuona mmene alili. 3  Ndipo aliyense amene akuyembekezera zimenezi kuchokera kwa iye, amadziyeretsa+ chifukwa iyenso ndi woyera. 4  Aliyense amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo akuphwanya malamulo, choncho tchimo ndi kuphwanya malamulo. 5  Inu mukudziwanso kuti iye anaonekera kuti achotse machimo athu+ ndipo mwa iye mulibe tchimo. 6  Aliyense amene ali wogwirizana ndi Yesu sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo.+ Amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo ndiye kuti samukhulupirira* kapena kumudziwa. 7  Ana anga okondedwa, wina asakusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama ngati mmene Yesu alili. 8  Amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo amatsanzira Mdyerekezi, chifukwa Mdyerekezi wakhala akuchimwa kuyambira pachiyambi.*+ Nʼchifukwa chake Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.+ 9  Aliyense amene ali mwana wa Mulungu sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo,+ chifukwa ali ndi mzimu wa Mulungu.* Ndipo sangakhale ndi chizolowezi chochita tchimo, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.+ 10  Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi tingawadziwe ndi mfundo iyi: Aliyense amene sachita zolungama ndiye kuti satsanzira Mulungu, chimodzimodzinso amene sakonda mʼbale wake.+ 11  Pajatu uthenga umene munamva kuyambira pachiyambi ndi wakuti tizikondana.+ 12  Tisakhale ngati Kaini, amene ankatsanzira woipayo ndipo anapha mʼbale wake.+ Nʼchifukwa chiyani anapha mʼbale wake? Chifukwa chakuti zochita zake zinali zoipa,+ koma za mʼbale wake zinali zolungama.+ 13  Abale, musadabwe kuti dziko limadana nanu.+ 14  Tikudziwa kuti tinali ngati akufa koma tsopano ndife amoyo+ chifukwa timakonda abale athu.+ Amene sakonda mʼbale wake ndiye kuti adakali wakufa.+ 15  Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wopha munthu,+ ndipo mukudziwa kuti aliyense wopha munthu sadzalandira moyo wosatha.+ 16  Tadziwa chikondi chifukwa chakuti Yesu Khristu anapereka moyo wake chifukwa cha ife,+ ndipo ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.+ 17  Aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo ndipo akuona mʼbale wake akuvutika chifukwa chosowa zinthuzo, koma osamusonyeza chifundo, kodi tingati munthu ameneyu amakonda Mulungu?+ 18  Ana anga okondedwa, tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha,+ koma tizisonyezana chikondi chenicheni mʼzochita zathu.+ 19  Tikamachita zimenezi tidzasonyeza kuti timayendera mfundo za choonadi. Ndipo tidzatsimikizira mitima yathu kuti Mulungu sakutiimba mlandu 20  pa chilichonse chimene mitima yathu ingatitsutse, chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.+ 21  Okondedwa, ngati mitima yathu sikutitsutsa, tikhoza kulankhula momasuka ndi Mulungu.+ 22  Ndipo chilichonse chimene tingamupemphe adzatipatsa,+ chifukwa timamvera malamulo ake komanso tikuchita zinthu zomusangalatsa. 23  Lamulo limene anatipatsa ndi lakuti, tikhale ndi chikhulupiriro mʼdzina la Mwana wake Yesu Khristu+ ndiponso tizikondana,+ monga mmene iye anatilamulira. 24  Komanso, munthu womvera malamulo ake amakhalabe wogwirizana naye ndipo iyenso amakhala wogwirizana ndi munthuyo.+ Ndiponso chifukwa cha mzimu umene anatipatsa, timadziwa kuti ndife ogwirizana naye.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Mulungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sanamuone.”
Kapena kuti, “wakhala akuchimwa kuchokera pamene iye anayamba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa mbewu Yake ili mwa iye.”