Kalata Yoyamba ya Yohane 4:1-21
4 Abale okondedwa, musamakhulupirire mawu alionse ouziridwa,*+ koma muzifufuza mawu ouziridwawo* kuti muone ngati alidi ochokera kwa Mulungu,+ chifukwa aneneri abodza* ambiri ayamba kupezeka mʼdzikoli.+
2 Kuti tidziwe ngati mawu ouziridwa ndi ochokera kwa Mulungu, timadziwira izi: Mawu alionse ouziridwa amene amavomereza zoti Yesu Khristu anabwera monga munthu ndi ochokera kwa Mulungu.+
3 Koma mawu alionse ouziridwa amene amatsutsa zoti Yesu anabwera monga munthu, amenewo si ochokera kwa Mulungu.+ Mawu amenewo ndi ouziridwa ndi wokana Khristu. Munamva kuti wokana Khristuyu adzalankhula mawu amenewo+ ndipo panopa akuwalankhuladi mʼdzikoli.+
4 Ana okondedwa, inu ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo mwagonjetsa aneneri abodzawo.+ Zili choncho chifukwa amene ali wogwirizana ndi inu+ ndi wamkulu kuposa amene ali wogwirizana ndi dziko.+
5 Aneneri abodzawa ndi ochokera mʼdzikoli,+ nʼchifukwa chake amalankhula zinthu zogwirizana ndi dzikoli ndipo dziko limawamvera.+
6 Ife tinachokera kwa Mulungu. Amene amadziwa Mulungu amatimvera,+ koma amene sanachokere kwa Mulungu satimvera.+ Mmenemu ndi mmene timadziwira mawu ouziridwa oona kapena mawu ouziridwa abodza.+
7 Abale okondedwa, tiyeni tipitirize kukondana,+ chifukwa chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene amakonda anthu ena, ndi mwana wa Mulungu ndipo akudziwa Mulungu.+
8 Munthu amene sakonda anthu ena sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndi chikondi.+
9 Zimene Mulungu anachita potisonyeza chikondi chake ndi izi: Anatumiza Mwana wake wobadwa yekha+ mʼdzikoli kuti tidzapeze moyo wosatha kudzera mwa iye.+
10 Mulungu anatumiza Mwana wake monga nsembe yophimba+ machimo athu.*+ Anachita zimenezi chifukwa chakuti anatikonda, osati chifukwa choti ifeyo ndi amene tinamukonda.
11 Abale okondedwa, ngati Mulungu anatikonda chonchi, ndiye kuti ifenso tikuyenera kumakondana.+
12 Palibe amene anaonapo Mulungu.+ Tikapitiriza kukondana, Mulungu apitiriza kukhala nafe ndipo azitisonyeza chikondi chake mokwanira.+
13 Tikudziwa kuti ndife ogwirizana naye ndiponso iye ndi wogwirizana ndi ife chifukwa watipatsa mzimu wake.
14 Komanso ife taona ndipo tikuchitira umboni kuti Atate anatumiza Mwana wake kuti akhale mpulumutsi wa dziko.+
15 Aliyense amene amavomereza kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu,+ amakhalabe wogwirizana ndi Mulungu ndipo Mulungu amakhalanso wogwirizana naye.+
16 Ife tikudziwa komanso tikukhulupirira kuti Mulungu amatikonda.+
Mulungu ndi chikondi,+ ndipo munthu amene amapitiriza kusonyeza chikondi, amakhalabe wogwirizana ndi Mulungu ndiponso Mulungu amakhala wogwirizana naye.+
17 Nʼchifukwa chake ife tikusonyeza chikondi mokwanira kuti tidzathe kulankhula momasuka+ pa tsiku lachiweruzo, chifukwa mmene Yesu Khristu alili, ndi mmenenso ife tilili mʼdzikoli.
18 Mantha amatichititsa kukhala omangika. Koma munthu amene amakonda Mulungu sachita mantha,+ chifukwa chikondi chimene chili chokwanira chimathetsa mantha. Munthu amene amachita mantha, chikondi chake si chokwanira.+
19 Ife timasonyeza chikondi, chifukwa Mulungu ndi amene anayamba kutikonda.+
20 Ngati wina amanena kuti, “Ndimakonda Mulungu,” koma nʼkumadana ndi mʼbale wake,+ ndiye kuti ndi wabodza. Chifukwa amene sakonda mʼbale wake+ amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.+
21 Ndipo iye anatipatsa lamulo lakuti, munthu amene amakonda Mulungu azikondanso mʼbale wake.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “aneneri onyenga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mizimuyo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu uliwonse.”
^ Kapena kuti, “monga njira yosangalatsira Mulungu.”