Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 2:1-17

  • Paulo ankafuna kuti Akhristu a ku Korinto asangalale (1-4)

  • Wochimwa anakhululukidwa nʼkubwezeretsedwa (5-11)

  • Paulo anapita ku Torowa ndiponso ku Makedoniya (12, 13)

  • Utumiki, kuguba ponyadira kupambana (14-17)

    • Sitichita malonda ndi mawu a Mulungu (17)

2  Ndasankha kuti pobweranso kwa inu, ulendo wanga usadzakhale wachisoni. 2  Chifukwa ngati ndingakuchititseni kumva chisoni, adzandisangalatsa ndani poti inuyo ndakuchititsani kumva chisoni? 3  Ndinalemba zimene zija kuti ndikadzabwera kumeneko, ndisadzakhale wachisoni chifukwa cha anthu amene ndiyenera kusangalala nawo. Chifukwa ndikukhulupirira kuti zimene zimandipangitsa kusangalala, zimapangitsanso nonsenu kusangalala. 4  Inetu ndinakulemberani kalata ija ndikuvutika, ndili ndi nkhawa kwambiri komanso ndikulira, osati kuti mumve chisoni,+ koma kuti mudziwe kuti ndimakukondani kwambiri. 5  Ngati wina wachita zinthu zomvetsa chisoni,+ sanamvetse chisoni ineyo, koma kwenikweni wamvetsa chisoni nonsenu. Komabe sindikufuna kulankhula mwamphamvu za nkhani imeneyi. 6  Kudzudzulidwa ndi anthu ambiri chonchi nʼkokwanira kwa munthu ameneyu. 7  Tsopano mukhululukireni ndi mtima wonse ndiponso kumutonthoza,+ kuopera kuti iye angakhale ndi chisoni chopitirira malire mpaka kutaya mtima.+ 8  Choncho ndikukudandaulirani kuti mumutsimikizire kuti mumamukonda.+ 9  Ndinakulemberani nʼcholinga choti ndidziwe ngati mulidi omvera pa zinthu zonse. 10  Mukakhululukira munthu chilichonse, inenso ndimukhululukira. Ndipo chilichonse chimene ineyo ndakhululukira munthu (ngati chilipo chimene ndakhululuka) ndachita zimenezo chifukwa cha inuyo, pamaso pa Khristu, 11  kuti Satana asatichenjerere,+ chifukwa tikudziwa bwino ziwembu* zake.+ 12  Nditafika ku Torowa+ kukalengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, ndipo mwayi wogwira ntchito ya Ambuye utanditsegukira, 13  mtima wanga sunakhazikike chifukwa sindinamupeze mʼbale wanga Tito.+ Choncho ndinatsanzikana ndi abale kumeneko nʼkupita ku Makedoniya.+ 14  Koma tikuthokoza Mulungu amene nthawi zonse amatitsogolera limodzi ndi Khristu ngati kuti tikuguba pa chionetsero chonyadira kupambana. Ndipo kudzera mwa ife kafungo konunkhira bwino kodziwa Mulungu kakufalikira paliponse. 15  Chifukwa kwa Mulungu ndife kafungo konunkhira bwino konena za uthenga wa Khristu, kamene kakumvedwa ndi anthu amene akukapulumutsidwa komanso amene akukawonongedwa. 16  Kwa amene akupita kukawonongedwawo ndife fungo la imfa kupita ku imfa,+ koma kwa amene akupita kukapulumukawo ndife kafungo kabwino ka moyo kupita ku moyo. Ndipo ndani ali woyenera kugwira ntchito imeneyi? 17  Ifeyo ndife oyenerera. Chifukwa mawu a Mulungu sitichita nawo malonda*+ ngati mmene ambiri amachitira, koma timalalikira moona mtima mogwirizana ndi zimene ophunzira a Khristu ayenera kuchita. Tatumidwa ndi Mulungu ndipo timachita zimenezi pamaso pa Mulunguyo.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zolinga; mapulani.”
Kapena kuti, “sitipezerapo phindu.”