Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 4:1-18
4 Choncho, popeza tili ndi utumiki umenewu mogwirizana ndi chifundo chimene tinasonyezedwa, sitikutaya mtima.
2 Koma tasiya zinthu zochititsa manyazi zochitikira mseri, ndipo sitikuyenda mwachinyengo kapena kupotoza mawu a Mulungu.+ Koma pochititsa choonadi kuti chidziwike, takhala chitsanzo chabwino kwa munthu* aliyense pamaso pa Mulungu.+
3 Ngati uthenga wabwino umene tikulalikira uli wophimbika, ndi wophimbika kwa anthu amene akupita kukawonongedwa,
4 anthu osakhulupirira amene mulungu wa nthawi* ino+ wachititsa khungu maganizo awo+ kuti asaone kuwala+ kwa uthenga wabwino waulemerero wonena za Khristu, yemwe ndi chifaniziro cha Mulungu.+
5 Chifukwa sitikulalikira za ifeyo koma za Yesu Khristu, kuti iye ndi Ambuye ndipo ifeyo ndife akapolo anu chifukwa cha Yesuyo.
6 Popeza Mulungu ndi amene anati: “Kuwale kuchokera mumdima,”+ ndipo pogwiritsa ntchito nkhope ya Khristu waunika mitima yathu kuti iwale+ ndi ulemerero wokhudza kudziwa Mulungu.
7 Komabe, tili ndi chuma chimenechi+ mʼziwiya zadothi,*+ kuti mphamvu yoposa yachibadwa ichokere kwa Mulungu, osati kwa ife.+
8 Timapanikizidwa mʼnjira zosiyanasiyana, koma osati mpaka kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mpaka kusoweratu kothawira.*+
9 Timazunzidwa, koma Mulungu samatisiya.+ Timagwetsedwa pansi, koma sitiwonongeka.+
10 Nthawi zonse timapirira tikamazunzidwa ngati mmene Yesu anachitira+ ndipo timachita zimenezi kuti moyo wa Yesu uonekerenso mwa ife.*
11 Amoyofe nthawi zonse timakhala pa ngozi yoti tikhoza kuphedwa+ chifukwa cha Yesu, kuti moyo wa Yesu uonekerenso mʼmatupi athu oti angathe kufawa.
12 Choncho ngakhale kuti moyo wathu ukukhala pa ngozi, zimenezi zikubweretsa moyo kwa inuyo.
13 Ife tili ndi mtima wachikhulupiriro wofanana ndi zimene zinalembedwa kuti: “Ndinali ndi chikhulupiriro, choncho ndinalankhula.”+ Choncho ifenso tili ndi chikhulupiriro, ndipo tikulankhula,
14 podziwa kuti amene anaukitsa Yesu adzaukitsanso ifeyo ngati mmene anaukitsira Yesu, ndipo adzatipereka kwa Yesuyo pamodzi ndi inuyo.+
15 Chifukwa zonsezi zachitika kuti zikuthandizeni inuyo. Ndiponso zachitika kuti kukoma mtima kwakukulu kumene kunawonjezeka kuchulukebe chifukwa anthu ambiri akupereka mapemphero oyamikira ndipo zimenezi zikuchititsa kuti Mulungu alandire ulemerero.+
16 Choncho sitikutaya mtima. Koma ngakhale munthu wathu wakunja akutha, munthu wathu wamkati akuchititsidwa kukhala watsopano tsiku ndi tsiku.
17 Chifukwatu ngakhale kuti mavuto* amene tikukumana nawo ndi akanthawi ndiponso aangʼono, akutichititsa kuti tilandire ulemerero umene ukukulirakulira komanso womwe ndi wamuyaya,+
18 pamene tikuganizira kwambiri zinthu zosaoneka, osati zooneka.+ Chifukwa zooneka nʼzakanthawi, koma zosaoneka nʼzamuyaya.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chikumbumtima cha munthu.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “mʼmitsuko yadothi.”
^ Kapena kuti, “kusoweratu mtengo wogwira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmatupi athu.”
^ Kapena kuti, “mayesero.”