2 Mafumu 22:1-20
22 Yosiya+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 8 ndipo analamulira zaka 31 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Bozikati.+ Dzina lawo linali Yedida mwana wa Adaya.
2 Yosiya anachita zoyenera pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira zonse za Davide kholo lake.+ Iye sanapatukire kumanja kapena kumanzere.
3 Mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, mfumuyo inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu yemwe anali mlembi, kuti apite kunyumba ya Yehova.+ Inamuuza kuti:
4 “Pita kwa Hilikiya+ mkulu wa ansembe, ukamuuze kuti asonkhanitse ndalama zonse zimene zikubwera kunyumba ya Yehova,+ zimene alonda a pakhomo atolera kwa anthu.+
5 Azipereke kwa omwe asankhidwa kuti aziyangʼanira ntchito panyumba ya Yehova, kuti akazipereke kwa amene akugwira ntchitoyo mʼnyumba ya Yehova, kuti akonze* nyumbayo.+
6 Akazipereke kwa amisiri, kwa omanga nyumba ndiponso kwa amisiri omanga ndi miyala. Agulirenso matabwa ndi miyala yosema kuti akonzere nyumbayo.+
7 Koma anthu amene akupatsidwa ndalamazo asafunsidwe mmene akuziyendetsera chifukwa ndi anthu odalirika.”+
8 Kenako Hilikiya mkulu wa ansembe anauza Safani mlembi+ kuti: “Ndapeza buku la Chilamulo+ mʼnyumba ya Yehova!” Choncho Hilikiya anapereka bukulo kwa Safani ndipo iye anayamba kuliwerenga.+
9 Ndiyeno Safani mlembi anapita kwa mfumu kukanena kuti: “Atumiki anu akhuthula ndalama zimene anazipeza mʼnyumbayo ndipo azipereka kwa omwe anasankhidwa kuti aziyangʼanira ntchito panyumba ya Yehova.”+
10 Safani mlembi anauzanso mfumuyo kuti: “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku+ linalake.” Ndiyeno Safani anayamba kuwerengera mfumu bukulo.
11 Mfumuyo itangomva mawu a mʼbuku la Chilamulo, inangʼamba zovala zake.+
12 Kenako mfumuyo inalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu+ mwana wa Safani, Akibori mwana wa Mikaya, Safani mlembi ndi Asaya mtumiki wa mfumu, kuti:
13 “Pitani mukafunse kwa Yehova mʼmalo mwa ineyo, anthuwa ndiponso mʼmalo mwa Ayuda onse. Mukafunse zokhudza mawu a mʼbuku limene lapezekali, chifukwa Yehova watikwiyira kwambiri,+ popeza makolo athu sanamvere mawu a mʼbukuli. Iwo sanachite zonse zimene zalembedwamo zokhudza ife.”
14 Choncho wansembe Hilikiya, Ahikamu, Akibori, Safani ndi Asaya anapita kwa Hulida mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe ankayangʼanira mosungira zovala, mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi. Hulidayo ankakhala Kumbali Yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu.+
15 Iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Munthu amene wakutumaniyo mukamuuze kuti:
16 “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka pamalo ano ndiponso kwa anthu ake pokwaniritsa mawu onse amʼbuku limene mfumu ya Yuda yawerenga.+
17 Chifukwa chakuti andisiya nʼkumapereka nsembe zautsi kwa milungu+ ina kuti andikwiyitse ndi ntchito zonse za manja awo,+ mkwiyo wanga udzayakira malo ano ndipo sudzazimitsidwa.’”+
18 Mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova, mukaiuze kuti, “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: ‘Ponena za mawu amene wamvawo,
19 chifukwa chakuti mtima wako unali womvera* ndipo unadzichepetsa+ pamaso pa Yehova utamva zimene ndanena zokhudza malo ano ndi anthu ake, kuti malowa adzakhala chinthu chodabwitsa ndi temberero ndipo unangʼamba zovala zako+ nʼkuyamba kulira pamaso panga, ineyo ndamva, watero Yehova.
20 Nʼchifukwa chake ndidzakuika mʼmanda a makolo ako ndipo udzaikidwa mʼmanda ako mwamtendere. Maso ako sadzaona tsoka lonse limene ndidzabweretse pamalo ano.’”’” Kenako iwo anakauza mfumuyo zimenezi.