2 Mafumu 3:1-27

  • Yehoramu, mfumu ya Isiraeli (1-3)

  • Amowabu anagalukira Isiraeli (4-25)

  • Amowabu anagonjetsedwa (26, 27)

3  Yehoramu+ mwana wa Ahabu, anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya mʼchaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya Yuda ndipo analamulira kwa zaka 12. 2  Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova, koma osati ngati mmene anachitira bambo ake kapena mayi ake chifukwa anachotsa chipilala chopatulika cha Baala chimene bambo ake anapanga.+ 3  Komabe sanasiye kuchita machimo amene Yerobowamu mwana wa Nebati anayambitsa mu Isiraeli.+ 4  Mesa, yemwe anali mfumu ya Mowabu, anali woweta nkhosa. Ankapereka kwa mfumu ya Isiraeli msonkho wa ana a nkhosa 100,000 ndi nkhosa zamphongo zosameta ubweya zokwana 100,000. 5  Ahabu atangomwalira,+ mfumu ya Mowabu inagalukira mfumu ya Isiraeli.+ 6  Choncho Mfumu Yehoramu anachoka ku Samariya nʼkukasonkhanitsa Aisiraeli onse. 7  Komanso anatumiza uthenga kwa Yehosafati mfumu ya Yuda wakuti: “Mfumu ya Mowabu yandigalukira. Kodi tipita limodzi kukamenya nkhondo ku Mowabu?” Yehosafati anayankha kuti: “Inde ndipita.+ Inu ndi ine ndife amodzi. Anthu anu ndi anthu anga ndi amodzi. Mahatchi anga nʼchimodzimodzi ndi mahatchi anu.”+ 8  Yehosafati anafunsa kuti: “Tidzera njira iti?” Yehoramu anayankha kuti: “Njira yamʼchipululu cha Edomu.” 9  Kenako mfumu ya Isiraeli inanyamuka limodzi ndi mfumu ya Yuda komanso mfumu ya Edomu.+ Atayenda mozungulira kwa masiku 7, mʼchipululumo munalibe madzi oti anthuwo amwe pamodzi ndi ziweto zimene ankayenda nazo. 10  Kenako mfumu ya Isiraeli inati: “Titani ife! Yehova wasonkhanitsa mafumu atatufe kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu!” 11  Ndiyeno Yehosafati anati: “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova kuti tifunsire kwa Yehova kudzera mwa iye?”+ Mtumiki wina wa mfumu ya Isiraeli anayankha kuti: “Kuli Elisa+ mwana wa Safati, amene ankathirira Eliya madzi osamba mʼmanja.”*+ 12  Yehosafati atamva zimenezo anati: “Ameneyo ali ndi mawu a Yehova.” Choncho mfumu ya Isiraeli, Yehosafati ndi mfumu ya Edomu anapita kwa Elisa. 13  Elisa anafunsa mfumu ya Isiraeli kuti: “Mukufuna chiyani kwa ine?+ Pitani kwa aneneri a bambo anu ndi kwa aneneri a mayi anu.”+ Koma mfumu ya Isiraeliyo inati: “Ayi musatero, chifukwa Yehova wasonkhanitsa mafumu atatufe kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu.” 14  Elisa anayankha kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba amene ndimamʼtumikira, ndikanakhala kuti sindilemekeza Mfumu Yehosafati+ ya Yuda, sindikanakuyangʼanani nʼkomwe kapena kukusamalani.+ 15  Ndiitanireni woimba zeze.”+ Woimba zezeyo atangoyamba kuimba, dzanja la Yehova linayamba kuthandiza Elisa.+ 16  Kenako iye anati: “Yehova wanena kuti, ‘Mukumbe ngalande mʼchigwa* chonsechi, 17  chifukwa Yehova wanena kuti: “Simuona mphepo kapena mvula, koma mʼchigwa chonsechi mudzaza madzi.+ Ndipo inu pamodzi ndi ziweto zanu komanso nyama zanu zina mumwa madziwo.”’ 18  Komatu zimenezi ndi zinthu zazingʼono kwambiri kwa Yehova,+ chifukwa adzaperekanso Amowabu mʼmanja mwanu.+ 19  Choncho mukagwetse mzinda uliwonse wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri+ komanso mzinda uliwonse wabwino kwambiri ndipo mukadule mtengo uliwonse wabwino. Mukatseke akasupe onse amadzi nʼkuwononga malo alionse abwino poponyapo miyala.”+ 20  Ndiyeno pa nthawi yopereka nsembe yambewu mʼmawa,+ anangoona madzi akuchokera cha ku Edomu ndipo malo onsewo anadzaza madzi. 21  Amowabu onse anamva kuti kwabwera mafumu kudzamenyana nawo, choncho anasonkhanitsa amuna onse amene akanatha kunyamula zida nʼkukaima mʼmalire. 22  Atadzuka mʼmawa, dzuwa linawala pamadzi aja ndipo kwa Amowabu amene anali kutsidya linalo, madziwo ankaoneka ofiira ngati magazi. 23  Ataona zimenezi ananena kuti: “Amenewa ndi magazi. Ndiye kuti mafumu aja aphana okhaokha ndi lupanga. Amowabu inu, tiyeni tikatenge zinthu zawo!”+ 24  Iwo atalowa mumsasa wa Aisiraeli, Aisiraeli anayamba kuwapha. Amowabuwo anayamba kuthawa+ ndipo Aisiraeli anawathamangitsa nʼkumawapha mpaka kukafika ku Mowabu. 25  Aisiraeli anayamba kugwetsa mizinda. Pamalo alionse abwino, aliyense anali kuponyapo mwala mpaka kudzaza malo onsewo. Anatseka kasupe aliyense wamadzi+ ndiponso kugwetsa mtengo uliwonse wabwino.+ Mpanda wamiyala wa mzinda wa Kiri-hareseti+ wokha ndi umene unatsala ndipo oponya miyala anazungulira mzindawo nʼkugwetsa mpandawo. 26  Mfumu ya Mowabu itaona kuti ikugonja, inatenga amuna 700 amalupanga kuti adutse nʼkukapeza mfumu ya Edomu,+ koma analephera. 27  Choncho mfumu ya Mowabu inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa amene akanalowa ufumu mʼmalo mwake nʼkumupereka nsembe yopsereza+ pakhoma. Atatero anthu* anakwiyira kwambiri Aisiraeli ndipo iwo anasiya kumenyana ndi mfumu ya Mowabu nʼkubwerera kwawo.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amene anali mtumiki wa Eliya.”
Ayenera kuti akutanthauza asilikali a Edomu ndi Yuda omwe ankathandiza Aisiraeli.