2 Mafumu 8:1-29
8 Elisa anauza mayi amene anamuukitsira mwana+ uja, kuti: “Nyamuka, iwe ndi banja lako, ukakhale mlendo kulikonse kumene ungasankhe, chifukwa Yehova wanena kuti mʼdzikoli mudzakhala njala+ kwa zaka 7.”
2 Choncho mayiyo ndi banja lake ananyamuka nʼkupita kukakhala mʼdziko la Afilisiti+ kwa zaka 7, mogwirizana ndi zimene munthu wa Mulungu woonayo ananena.
3 Zaka 7 zitatha, mayiyo anabwerera kuchokera kudziko la Afilisiti nʼkupita kukapempha mfumu kuti imubwezere nyumba yake ndi munda wake.
4 Pa nthawiyo nʼkuti mfumu ikulankhula ndi Gehazi mtumiki wa munthu wa Mulungu woona, kuti: “Ndifotokozere zinthu zonse zazikulu zimene Elisa wachita.”+
5 Gehazi akufotokozera mfumuyo mmene Elisa anaukitsira munthu wakufa,+ mayi wa mwana amene anaukitsidwayo anafika kwa mfumu nʼkuyamba kupempha kuti amubwezere nyumba yake ndi munda wake.+ Nthawi yomweyo Gehazi anati: “Mbuyanga mfumu, mayi ndimanena uja ndi uyu ndipo mwana wake amene Elisa anamuukitsayo ndi uyu.”
6 Ndiyeno mfumuyo inapempha mayiyo kuti afotokoze nkhani yonse ndipo mayiyo anafotokozadi. Kenako mfumuyo inauza nduna ya panyumba yake kuti: “Mayiyu umʼbwezere zinthu zake zonse komanso umupatse ndalama zimene akanapeza pa zokolola za kumunda kwake kuyambira pamene anachoka mpaka lero.”
7 Kenako Elisa anapita ku Damasiko+ ndipo pa nthawiyo nʼkuti Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya akudwala. Choncho mfumuyo inauzidwa kuti: “Munthu wa Mulungu woona+ uja wabwera kuno.”
8 Mfumuyo itamva zimenezi, inauza Hazaeli+ kuti: “Tenga mphatso ndipo upite kwa munthu wa Mulungu woonayo.+ Ukafunse kwa Yehova kudzera mwa iye kuti, ‘Kodi ndichira matenda angawa?’”
9 Choncho Hazaeli anatenga mphatso nʼkupita kukakumana naye. Mphatsozo anazinyamula pa ngamira zokwana 40. Anatenga chinthu chilichonse chabwino cha ku Damasiko. Atafika kwa Elisa anamuuza kuti: “Mwana wanu Beni-hadadi mfumu ya Siriya wandituma kudzakufunsani kuti, ‘Kodi ndichira matenda angawa?’”
10 Ndiyeno Elisa anayankha Hazaeli kuti: “Pita ukamuuze kuti, ‘Muchira ndithu.’ Koma Yehova wandionetsa kuti afa ndithu.”+
11 Elisa anayangʼanitsitsa Hazaeli mpaka Hazaeliyo anachita manyazi. Kenako munthu wa Mulungu woonayo anayamba kulira.
12 Hazaeli anafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukulira mbuyanga?” Elisa anayankha kuti: “Chifukwa ndikudziwa zoipa zimene iweyo udzachitire Aisiraeli.+ Malo awo otetezedwa udzawatentha ndi moto, amuna amphamvu udzawapha ndi lupanga, ana awo aangʼono udzawanyenyanyenya ndipo akazi awo apakati udzawatumbula.”+
13 Hazaeli atamva mawu amenewa, anati: “Zingatheke bwanji kuti ine mtumiki wanu, galu ngati ine, ndichite zinthu ngati zimenezi?” Koma Elisa anati: “Yehova wandionetsa kuti iweyo udzakhala mfumu ya Siriya.”+
14 Kenako Hazaeli anachoka kwa Elisa nʼkubwerera kwa mbuye wake ndipo iye anamufunsa kuti: “Kodi Elisa wakuuza kuti chiyani?” Hazaeli anayankha kuti: “Wandiuza kuti, ‘Muchira ndithu.’”+
15 Tsiku lotsatira, Hazaeli anatenga chofunda nʼkuchiviika mʼmadzi kenako anaphimba mfumuyo kumaso mpaka inamwalira.+ Ndiyeno Hazaeli anayamba kulamulira mʼmalo mwake.+
16 Mʼchaka cha 5 cha Yehoramu+ mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli, pamene Yehosafati anali mfumu ya Yuda, Yehoramu+ mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, anakhala mfumu.
17 Yehoramu anakhala mfumu ali ndi zaka 32 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8.
18 Iye anayenda mʼnjira ya mafumu a Isiraeli+ ngati mmene anachitira anthu a mʼbanja la Ahabu,+ chifukwa anakwatira mwana wa Ahabu.+ Ndipo iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+
19 Koma Yehova sanafune kuwononga ufumu wa Yuda chifukwa cha Davide mtumiki wake,+ poti anamulonjeza kuti adzamʼpatsa nyale+ nthawi zonse, iyeyo ndi ana ake.
20 Mʼmasiku a Yehoramu, Aedomu anagalukira Yuda+ ndipo kenako anasankha mfumu yoti iziwalamulira.+
21 Choncho Yehoramu anapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse. Kumeneko, iye ananyamuka usiku nʼkukapha Aedomu amene anamuzungulira. Anaphanso atsogoleri a asilikali okwera magaleta ndipo asilikali ena onse anathawira kumatenti awo.
22 Koma Aedomu anapitirizabe kugalukira Yuda mpaka lero. Pa nthawi imeneyi mʼpamenenso Libina+ anagalukira Yuda.
23 Nkhani zina zokhudza Yehoramu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda.
24 Kenako Yehoramu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ Kenako mwana wake Ahaziya+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.
25 Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anakhala mfumu mʼchaka cha 12 cha Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli.+
26 Ahaziya anayamba kulamulira ali ndi zaka 22 ndipo analamulira ku Yerusalemu chaka chimodzi. Mayi ake dzina lawo linali Ataliya+ mdzukulu wa Omuri+ mfumu ya Isiraeli.
27 Iye anayenda mʼnjira ya anthu a mʼbanja la Ahabu+ ndipo anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira anthu a mʼbanja la Ahabuwo, chifukwa anali wachibale wawo.+
28 Choncho iye anapita ku nkhondo ndi Yehoramu mwana wa Ahabu kukamenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya ku Ramoti-giliyadi.+ Koma Asiriyawo anavulaza Yehoramu.+
29 Choncho Mfumu Yehoramu inabwerera ku Yezereeli+ kuti ikachire mabala amene Asiriya anaivulaza ku Rama,* pamene inkamenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.+ Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anali atavulazidwa.*