2 Mbiri 21:1-20

  • Yehoramu, mfumu ya Yuda (1-11)

  • Uthenga umene Eliya analemba (12-15)

  • Mapeto omvetsa chisoni a Yehoramu (16-20)

21  Kenako Yehosafati, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndiyeno mwana wake Yehoramu anakhala mfumu mʼmalo mwake.+ 2  Azichimwene ake a Yehoramu, ana a Yehosafati, anali Azariya, Yehiela, Zekariya, Azariya, Mikayeli ndi Sefatiya. Onsewa anali ana a Yehosafati mfumu ya Isiraeli. 3  Bambo awo anawapatsa mphatso zambiri zasiliva ndi zagolide, zinthu zina zamtengo wapatali komanso mizinda ya ku Yuda+ yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Koma ufumu anaupereka kwa Yehoramu+ chifukwa ndi amene anali woyamba kubadwa. 4  Yehoramu atayamba kulamulira mu ufumu wa bambo ake, anapha ndi lupanga azichimwene ake onse+ ndiponso akalonga ena a Isiraeli. Iye anachita zimenezi kuti alimbitse ufumu wake. 5  Yehoramu anakhala mfumu ali ndi zaka 32 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8.+ 6  Iye anayenda mʼnjira ya mafumu a Isiraeli+ ngati mmene anachitira anthu a mʼbanja la Ahabu, chifukwa anakwatira mwana wa Ahabu.+ Ndipo iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova. 7  Koma Yehova sanafune kuwononga nyumba ya Davide chifukwa cha pangano limene anachita ndi Davide,+ poti anamulonjeza kuti adzamʼpatsa nyale nthawi zonse, iyeyo ndi ana ake.+ 8  Mʼmasiku a Yehoramu, Aedomu anagalukira Yuda+ ndipo kenako anasankha mfumu yoti iziwalamulira.+ 9  Choncho Yehoramu ndi akuluakulu a asilikali ake anapita kumeneko pamodzi ndi magaleta ake onse. Ndiyeno ananyamuka usiku nʼkukapha Aedomu amene anamuzungulira komanso atsogoleri a asilikali okwera magaleta. 10  Koma Aedomu akupitirizabe kugalukira Yuda mpaka lero. Pa nthawi imeneyinso Libina+ anagalukira Yehoramu chifukwa Yehoramuyo anali atasiya Yehova Mulungu wa makolo ake.+ 11  Komanso iye anamanga malo okwezeka+ mʼmapiri a ku Yuda zomwe zinachititsa kuti anthu a ku Yerusalemu achite uhule wauzimu ndipo iye anasocheretsanso Yuda. 12  Kenako analandira kalata yochokera kwa mneneri Eliya+ yakuti: “Yehova Mulungu wa Davide kholo lanu wanena kuti, ‘Sunayende mʼnjira za Yehosafati+ bambo ako kapena mʼnjira za Asa+ mfumu ya Yuda. 13  Koma wayenda mʼnjira ya mafumu a Isiraeli+ nʼkuchititsa kuti Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu achite uhule wauzimu+ ngati uhule wa anthu a mʼbanja la Ahabu.+ Waphanso ngakhale azichimwene ako,+ anthu a mʼnyumba ya bambo ako, amene anali abwino kuposa iweyo. 14  Choncho Yehova adzalanga koopsa anthu ako, ana ako ndi akazi ako, ndipo adzawononga katundu wako yense. 15  Iweyo udzadwala matenda ambiri kuphatikizapo matenda amʼmatumbo, mpaka matumbo ako azidzatuluka tsiku ndi tsiku chifukwa cha matendawo.’” 16  Kenako Yehova anachititsa+ kuti Afilisiti+ ndi Aluya,+ amene anali pafupi ndi Aitiyopiya, aukire Yehoramu. 17  Choncho iwo anafika mwamphamvu mpaka analowa mu Yuda. Anthuwo anatenga katundu yense amene anali mʼnyumba ya mfumu+ komanso ana ake ndi akazi ake. Sanamusiyire mwana aliyense kupatulapo Yehoahazi,*+ mwana wake wamngʼono kwambiri. 18  Kenako Yehova anamudwalitsa matenda amʼmatumbo osachiritsika.+ 19  Patatha zaka ziwiri zathunthu akudwala, matumbo ake anatuluka chifukwa cha matendawo ndipo matenda atafika poipa kwambiri, iye anamwalira. Anthu ake sanawotche zonunkhira pa maliro ake ngati mmene anachitira pa maliro a makolo ake akale.+ 20  Yehoramu anakhala mfumu ali ndi zaka 32 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8. Iye atafa, palibe amene anadandaula. Choncho anamuika mu Mzinda wa Davide,+ koma osati mʼmanda a mafumu.+

Mawu a M'munsi

Ankadziwikanso kuti Ahaziya.