2 Mbiri 27:1-9

  • Yotamu, mfumu ya Yuda (1-9)

27  Yotamu+ anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa mwana wa Zadoki.+ 2  Yotamu ankachita zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Uziya bambo ake,+ kungoti sanachite makani nʼkukalowa mʼkachisi wa Yehova.+ Koma anthu ankachitabe zoipa. 3  Iye anamanga geti lakumtunda la nyumba ya Yehova+ ndipo pakhoma la mpanda wa Ofeli anamangapo zinthu zambiri.+ 4  Komanso anamanga mizinda+ mʼdera lamapiri la Yuda+ ndipo mʼdera lankhalango anamangamo nsanja+ ndiponso malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 5  Yotamu anamenyana ndi mfumu ya Aamoni+ ndipo patapita nthawi anawagonjetsa. Choncho chaka chimenecho Aamoni anamʼpatsa matalente* a siliva 100, tirigu wokwana miyezo 10,000 ya kori* komanso balere wokwana miyezo 10,000 ya kori. Aamoni anamupatsanso zinthu zimenezi mʼchaka chachiwiri ndi chachitatu.+ 6  Choncho Yotamu anapitiriza kukhala wamphamvu popeza anatsimikiza kuyenda mʼnjira za Yehova Mulungu wake. 7  Nkhani zina zokhudza Yotamu, zimene anachita komanso nkhondo zonse zomwe anamenya, zinalembedwa mʼBuku la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda.+ 8  Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira zaka 16 ku Yerusalemu.+ 9  Kenako Yotamu mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide.+ Ndiyeno mwana wake Ahazi anakhala mfumu mʼmalo mwake.+

Mawu a M'munsi

Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Muyezo wa kori unali wokwana malita 220. Onani Zakumapeto B14.