2 Samueli 22:1-51
22 Davide analankhula ndi Yehova mawu a nyimbo iyi,+ pa tsiku limene Yehova anamupulumutsa kwa adani ake onse+ ndiponso mʼmanja mwa Sauli.+
2 Iye anati:
“Yehova ndi thanthwe langa, malo anga achitetezo+ ndiponso Wondipulumutsa.+
3 Mulungu wanga ndi thanthwe langa,+ ine ndimathawira kwa iye,Iye ndi chishango changa,+ nyanga* yanga ya chipulumutso* ndi malo anga achitetezo.*+Komanso ndi malo anga othawirako,+ mpulumutsi wanga+ amene amandipulumutsa kwa anthu achiwawa.
4 Ndimapempha Yehova, amene ndi woyenera kutamandidwa, kuti andithandize.Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.
5 Mafunde a imfa anandizungulira;+Gulu la anthu opanda pake linkandiopseza.+
6 Zingwe za Manda* zinandizungulira;+Ndinatcheredwa misampha ya imfa.+
7 Pa nthawi ya mavuto, ndinaitana Yehova,+Ndinapitiriza kuitana Mulungu wanga.
Iye anamva mawu anga ali mʼkachisi wake,Makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+
8 Dziko lapansi linayamba kugwedezeka ndiponso kunjenjemera;+Maziko akumwamba anagwedezeka.+Anagwedezeka chifukwa Mulungu anakwiya.+
9 Utsi unatuluka mʼmphuno mwake,Ndipo moto wowononga unatuluka mʼkamwa mwake;+Makala oyaka anatuluka mwa iye.
10 Iye anaweramitsa kumwamba pamene ankatsika,+Mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake.+
11 Iye anakwera pakerubi+ ndipo anabwera akuuluka.
Anaonekera pamapiko a mngelo.*+
12 Kenako anaika mdima momuzungulira ngati tenti,+Mʼmadzi akuda ndi mʼmitambo yakuda.
13 Mʼkuwala kochokera pamaso pake munatuluka makala oyaka moto.
14 Kenako Yehova ali kumwamba anayamba kugunda ngati mabingu;+Wamʼmwambamwamba anachititsa kuti mawu ake amveke.+
15 Anaponya mivi yake+ ndipo anawabalalitsa;Anaponya mphezi ndipo anawasokoneza.+
16 Pansi pa nyanja panaonekera;+Maziko a dziko lapansi anaonekera chifukwa cha kudzudzula kwa Yehova,Chifukwa cha mphamvu ya mpweya wotuluka mʼmphuno mwake.+
17 Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba;Anandigwira nʼkundivuula mʼmadzi akuya.+
18 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,+Kwa anthu odana nane amene anali amphamvu kuposa ine.
19 Adaniwo anandiukira pa tsiku la tsoka,+Koma Yehova anandithandiza.
20 Ananditenga nʼkundiika pamalo otetezeka;*+Anandipulumutsa chifukwa ankasangalala nane.+
21 Yehova amandidalitsa mogwirizana ndi chilungamo changa;+Amandipatsa mphoto mogwirizana ndi manja anga osalakwa.*+
22 Chifukwa ndasunga njira za Yehova,Ndipo sindinachite chinthu choipa kwambiri, chomwe ndi kusiya Mulungu wanga.
23 Ndimakumbukira ziweruzo zake zonse;+Ndipo sindidzasiya kutsatira malamulo ake.+
24 Ndidzakhalabe wosalakwa+ pamaso pake,Ndipo ndidzayesetsa kupewa cholakwa.+
25 Yehova andipatse mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa,+Komanso chifukwa choti ndine wosalakwa pamaso pake.+
26 Munthu wokhulupirika, mumamuchitira mokhulupirika.+Munthu wamphamvu komanso wosalakwa, mumamuchitira mwachilungamo.+
27 Munthu woyera, mumamusonyeza kuti ndinu woyera,+Koma munthu wamaganizo opotoka mumamusonyeza kuti ndinu wochenjera.+
28 Mumapulumutsa anthu odzichepetsa,+Koma mumanyansidwa ndi anthu odzikweza ndipo mumawatsitsa.+
29 Inu Yehova ndinu nyale yanga;+Yehova ndi amene amandiunikira mumdima.+
30 Ndi thandizo lanu ndingalimbane ndi gulu la achifwamba;Ndi mphamvu za Mulungu ndingakwere khoma.+
31 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+
Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+
32 Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+
Nanga pali thanthwe linanso kupatula Mulungu wathu?+
33 Mulungu woona ndi malo anga otetezeka kwambiri,+Ndipo iye adzasalaza njira yanga.+
34 Amachititsa kuti mapazi anga akhale ngati a mbawala;Amachititsa kuti ndiime pamalo okwera.+
35 Iye amaphunzitsa manja anga kumenya nkhondo;Manja anga angathe kukunga uta wakopa.*
36 Mumandipatsa chishango chanu chachipulumutso,Ndipo kudzichepetsa kwanu kumandikweza.+
37 Mumakulitsa njira kuti mapazi anga azidutsamo,Ndipo mapazi anga sadzaterereka.+
38 Ndidzathamangitsa adani anga nʼkuwapha onse;Ndipo sindidzabwerera mpaka nditawafafaniza.
39 Ndidzawafafaniza ndi kuwaphwanya kuti asadzukenso.+Iwo adzagwera pansi pa mapazi anga.
40 Mudzandipatsa mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo;+Mudzachititsa kuti adani anga agonje.+
41 Mudzachititsa kuti adani anga athawe pamaso panga;+Ndidzapha* anthu amene amadana nane.+
42 Amafuula kuti athandizidwe, koma palibe angawapulumutse;Amafika pofuulira Yehova, koma iye samawayankha.+
43 Ndidzawapera ndipo adzakhala ngati fumbi.Ndidzawapondaponda ngati matope amumsewu.
44 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga ondipezera zifukwa.+
Mudzanditeteza kuti ndikhale mtsogoleri wa mitundu ya anthu.+Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+
45 Anthu ochokera mʼdziko lina adzandiweramira mwamantha;+Zimene adzamve zokhudza ine zidzachititsa kuti azindimvera.
46 Anthu ochokera mʼdziko lina adzachita mantha;Iwo adzatuluka mʼmalo awo otetezeka akunjenjemera.
47 Yehova ndi wamoyo! Litamandike Thanthwe langa!+
Mulungu wanga, yemwe ndi thanthwe limene limandipulumutsa, alemekezeke.+
48 Mulungu woona amabwezera adani anga;+Iye amachititsa kuti mitundu ya anthu izindigonjera;+
49 Iye amandipulumutsa kwa adani anga.
Mumandikweza pamwamba+ pa anthu ondiukira;Mumandipulumutsa kwa munthu wachiwawa.+
50 Nʼchifukwa chake ndidzakuyamikani inu Yehova pakati pa mitundu ya anthu.+Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+
51 Iye amachita zazikulu kuti apulumutse mfumu yake;+Amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa wodzozedwa wake,Kwa Davide ndi mbadwa* zake mpaka kalekale.”+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “mpulumutsi wanga wamphamvu.”
^ Kapena kuti, “malo anga okwezeka achitetezo.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti “pamapiko a mphepo.”
^ Kapena kuti, “otakasuka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “oyera.”
^ Kapena kuti, “wamkuwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndidzakhalitsa chete.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”