Kalata yachiwiri yopita kwa Timoteyo 3:1-17
3 Koma dziwa kuti masiku otsiriza+ adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.
2 Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika,
3 osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi ena, onenera ena zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino,
4 ochitira anzawo zoipa, osamva za ena, odzitukumula chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu,
5 ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.+ Anthu amenewa uziwapewa.
6 Ena mwa anthuwa amalowerera mozemba mʼmabanja nʼkumachititsa amayi ena kuti akhale akapolo awo. Amayiwa amakhala ofooka chifukwa cha machimo awo ndiponso otengeka ndi zilakolako zosiyanasiyana.
7 Nthawi zonse amaphunzira, koma satha kudziwa choonadi molondola.
8 Mofanana ndi Yane ndi Yambure, amene anatsutsa Mose, anthu amenewanso akupitiriza kutsutsa choonadi. Iwo ali ndi maganizo opotoka kwambiri, ndipo sakuyenerera chikhulupirirochi.
9 Koma sangapite patali, chifukwa kupusa kwawo kuonekera bwino kwa anthu onse, ngati mmene zinakhalira ndi anthu awiri aja.+
10 Koma iwe wayesetsa kutsatira zimene ndimaphunzitsa, moyo wanga,+ cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa ndi kupirira kwanga.
11 Ukudziwanso mmene ndinazunzikira komanso masautso amene ndinakumana nawo ku Antiokeya,+ ku Ikoniyo+ ndi ku Lusitara.+ Komabe ndinapirira ndipo Ambuye anandipulumutsa ku zonsezi.+
12 Pajatu onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mogwirizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.+
13 Koma anthu oipa ndi achinyengo adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.+
14 Koma iwe, pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo,+ chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa.
15 Kuyambira pamene unali wakhanda,+ wadziwa malemba oyera+ amene angakupatse nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke chifukwa chokhulupirira Khristu Yesu.+
16 Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,+ ndipo ndi othandiza pophunzitsa,+ kudzudzula, kukonza zinthu ndi kulangiza mwachilungamo,+
17 kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera kwambiri ndi wokonzeka mokwanira kugwira ntchito iliyonse yabwino.