Kwa Aefeso 4:1-32

  • Ogwirizana mʼthupi la Khristu (1-16)

    • Mphatso za amuna (8)

  • Umunthu wakale komanso watsopano (17-32)

4  Choncho ine, amene ndili mʼndende+ chifukwa cha Ambuye, ndikukuchondererani kuti muzichita zinthu mogwirizana+ ndi kuitana kumene anakuitanani. 2  Nthawi zonse muzichita zinthu modzichepetsa,*+ mofatsa, moleza mtima+ ndiponso muzilolerana chifukwa cha chikondi.+ 3  Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera, pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chimene chimatigwirizanitsa.+ 4  Pali thupi limodzi+ ndi mzimu umodzi,+ mogwirizana ndi chiyembekezo chimodzi+ chimene anakuitanirani. 5  Palinso Ambuye mmodzi,+ chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi, 6  ndi Mulungu mmodzi amenenso ndi Atate wa anthu onse. Iye ndi wamkulu kuposa wina aliyense, amachita zinthu kudzera mwa tonsefe ndipo mphamvu yake imagwira ntchito mwa onse. 7  Tsopano aliyense wa ife anapatsidwa kukoma mtima kwakukulu mogwirizana ndi mmene Khristu anamuyezera mphatso yaulereyi.+ 8  Chifukwa Malemba amanena kuti: “Atakwera pamalo apamwamba, anatenga anthu ogwidwa ukapolo ndipo anapereka amuna kuti akhale mphatso.”+ 9  Ndiye kodi mawu akuti “atakwera” amatanthauza chiyani? Amatanthauza kuti choyamba anatsika pansi, kutanthauza padziko lapansi. 10  Amene anatsikayo ndi amenenso anakwera+ kukakhala pamwamba kwambiri kuposa kumwamba konse,+ kuti zinthu zonse zikwaniritsidwe. 11  Ndipo pa mphatso zimene anaperekazo, ena anawapereka kuti akhale atumwi,+ ena aneneri,+ ena alaliki*+ ndipo ena abusa ndi aphunzitsi,+ 12  nʼcholinga choti athandize* oyerawo kuti aziyenda mʼnjira yoyenera, kuti azigwira ntchito yotumikira ena komanso kuti amange mpingo umene uli ngati thupi la Khristu,+ 13  mpaka tonse tidzakhale ogwirizana pa zimene timakhulupirira komanso podziwa molondola Mwana wa Mulungu. Zikadzatero, tidzakhala anthu achikulire, amene afika pa msinkhu wa munthu wamkulu+ ngati mmene Khristu analili. 14  Choncho tisakhalenso ana. Tisamatengeketengeke ngati kuti tikukankhidwa ndi mafunde ndiponso tisamatengeke kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya zinthu zachinyengo zimene anthu amaphunzitsa+ popeka mabodza mochenjera. 15  Koma tizilankhula zoona ndiponso kusonyeza chikondi. Tikatero tidzakhala achikulire mʼzinthu zonse ndipo tidzatha kuchita zinthu mogwirizana ndi Khristu, amene ndi mutu.+ 16  Tili ngati thupi,+ ndipo chifukwa cha iye, ziwalo zonse za thupi limeneli ndi zolumikizana bwino ndipo zimathandiza thupilo kuti lizigwira bwino ntchito. Chiwalo chilichonse cha thupili chikamagwira ntchito yake, thupili limakula bwino ndipo tidzapitiriza kukondana.+ 17  Choncho ndikunena komanso kuchitira umboni mwa Ambuye, kuti musapitirize kuyenda ngati mmene anthu a mitundu ina amayendera,+ potsatira maganizo awo opanda pake.+ 18  Iwo ali mumdima wa maganizo ndipo ndi otalikirana ndi moyo umene umachokera kwa Mulungu, chifukwa cha umbuli umene uli mwa iwo komanso chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo. 19  Popeza iwo sakuthanso kuzindikira makhalidwe abwino, anadzipereka okha ku khalidwe lopanda manyazi*+ kuti achite zonyansa zamtundu uliwonse mwadyera. 20  Koma inu simunaphunzire kuti Khristu ndi wotero. 21  Yesu ankaphunzitsa choonadi, moti ngati munamva zimene ankaphunzitsa ndiponso munaphunzitsidwa ndi iye, ndiye kuti zinthu zimenezo mukuzidziwa bwino. 22  Munaphunzitsidwa kuti muvule umunthu wakale+ umene umagwirizana ndi makhalidwe anu akale, umenenso ukuipitsidwa chifukwa cha zilakolako zachinyengo za umunthuwo.+ 23  Ndipo mupitirize kusintha kuti mukhale atsopano pa kaganizidwe kanu komanso mmene mumaonera zinthu.*+ 24  Ndipo muvale umunthu watsopano+ umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Mukachita zimenezi mudzatha kuchita zimene zilidi zolungama ndi zokhulupirika. 25  Choncho, popeza tsopano mwataya chinyengo, aliyense wa inu azilankhula zoona kwa mnzake,+ chifukwa ndife ziwalo zolumikizana.+ 26  Ngati mwakwiya, musachimwe.+ Dzuwa lisalowe mudakali okwiya.+ 27  Musamupatse mpata Mdyerekezi.*+ 28  Munthu wakuba asiye kubako, koma azigwira ntchito molimbikira. Azigwira ntchito yabwino ndi manja ake+ kuti azitha kupeza zinthu zimene angathe kugawana ndi munthu wosowa.+ 29  Mawu owola asamatuluke pakamwa panu,+ koma pazituluka mawu abwino okha kuti alimbikitse ena pakafunika kutero, kuti athandize anthu amene akumvetsera.+ 30  Komanso, musamamvetse chisoni mzimu woyera wa Mulungu,+ umene Mulunguyo anaugwiritsa ntchito pokuikani chidindo+ kuti mudzamasulidwe ndi dipo+ pa tsiku lachipulumutso. 31  Chidani chachikulu,+ kupsa mtima, mkwiyo, kulalata, mawu achipongwe+ komanso zinthu zonse zoipa zichotsedwe mwa inu.+ 32  Koma muzikomerana mtima, muzisonyezana chifundo chachikulu+ komanso muzikhululukirana ndi mtima wonse, ngati mmene inunso Mulungu anakukhululukirani ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndi maganizo odzichepetsa.”
Kapena kuti, “olalikira uthenga wabwino.”
Kapena kuti, “aphunzitse.”
MʼChigiriki a·sel′gei·a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “komanso mphamvu yoyendetsa maganizo anu.” Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu wa maganizo anu.”
Kapena kuti, “Musamupatse malo Mdyerekezi.”