Kwa Afilipi 2:1-30

  • Akhristu azikhala odzichepetsa (1-4)

  • Kudzichepetsa kwa Khristu komanso kukwezedwa kwake (5-11)

  • Yesetsani kuti mudzapulumuke (12-18)

    • Kuwala ngati zounikira (15)

  • Anatumiza Timoteyo ndi Epafurodito (19-30)

2  Muzichita zonse zimene mungathe kuti muzilimbikitsana mwa Khristu, muzitonthozana mwachikondi, muzisonyeza mzimu wokonda kuchitira zinthu limodzi,* muzisonyezana chikondi chachikulu komanso chifundo. 2  Mukamachita zimenezi, mudzachititsa kuti chimwemwe changa chisefukire. Muzisonyeza kuti mumaganiza mofanana, muli ndi chikondi chofanana komanso kuti ndinu ogwirizana kwambiri ndipo maganizo anu ndi amodzi.+ 3  Musamachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano+ kapena chifukwa chodzikuza,+ koma modzichepetsa, muziona kuti ena amakuposani.+ 4  Musamaganizire zofuna zanu zokha,+ koma muziganiziranso zofuna za ena.+ 5  Khalani ndi maganizo amenenso Khristu Yesu anali nawo.+ 6  Ngakhale kuti iye ankaoneka ngati Mulungu,+ sanaganizirepo zoti ayese kulanda udindo wa Mulungu kuti akhale wofanana naye.+ 7  Ayi sanachite zimenezo, koma anasiya zonse zimene anali nazo nʼkukhala ngati kapolo+ ndipo anakhala munthu.*+ 8  Kuposanso pamenepo, atakhala munthu,* anadzichepetsa ndipo anakhala womvera mpaka imfa,+ inde imfa yapamtengo wozunzikirapo.*+ 9  Pa chifukwa chimenechi, Mulungu anamukweza nʼkumupatsa udindo wapamwamba+ ndipo mokoma mtima anamupatsa dzina loposa lina lililonse.+ 10  Anachita zimenezi kuti mʼdzina la Yesu, onse apinde mawondo awo, kaya ali kumwamba, padziko lapansi kapena pansi pa nthaka.*+ 11  Komanso kuti aliyense avomereze poyera kuti Yesu Khristu ndi Ambuye,+ zimene zidzapereka ulemerero kwa Mulungu Atate. 12  Abale ndi alongo anga okondedwa, pamene ndinali nanu limodzi, nthawi zonse munkamvera. Simunachite zimenezi pa nthawi yokhayo imene ine ndinalipo koma ngakhale panopa pamene sindilinso ndi inu, mukumvera kwambiri. Mofanana ndi zimenezi, aliyense wa inu apitirize kuyesetsa kuchita zimenezi mwamantha ndi kunjenjemera kuti adzapulumuke. 13  Chifukwa Mulungu ndi amene amakulimbitsani. Amakupatsani mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zochitira zinthuzo. Iye amachita zimenezi chifukwa ndi zimene zimamusangalatsa. 14  Mukamachita zinthu muzipewa kungʼungʼudza+ komanso kukangana+ 15  kuti mukhale opanda chifukwa chokunenezerani komanso osalakwa. Mukhale ana a Mulungu+ opanda chilema pakati pa mʼbadwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota.+ Pakati pa mʼbadwo umenewu inu mukuwala ngati zounikira mʼdzikoli.+ 16  Pamene mukuchita zimenezi, mugwire mwamphamvu mawu amoyo.+ Mukatero ndidzakhala ndi chifukwa chosangalalira mʼtsiku la Khristu, chifukwa ndidzadziwa kuti sindinathamange pachabe kapena kuchita khama pachabe. 17  Komabe, ngakhale kuti ndikuthiridwa ngati nsembe yachakumwa,+ ndikuwonjezera pa nsembe+ zimene inu mukupereka komanso pa utumiki wopatulika umene* mukuchita mokhulupirika. Choncho ndikusangalala ndipo nonsenu ndikukondwera nanu limodzi. 18  Ndikukulimbikitsani kuti inunso musangalale limodzi ndi ine. 19  Koma ine, ndikuyembekeza kuti Ambuye Yesu andilola kutumiza Timoteyo+ kwa inu posachedwapa kuti ndidzalimbikitsidwe ndikadzamva mmene zinthu zilili kwa inu. 20  Chifukwa ndilibe wina amene ali ndi mtima ngati wake, amene angasamaliredi moona mtima zosowa zanu. 21  Anthu ena onse akungoganizira zofuna zawo zokha, osati za Yesu Khristu. 22  Koma inu mukudziwa chitsanzo chabwino chimene Timoteyo anasonyeza, kuti monga mwana+ ndi bambo ake, watumikira ngati kapolo limodzi ndi ine pofalitsa uthenga wabwino. 23  Choncho, ndikuyembekezera kukutumizirani munthu ameneyu ndikangodziwa mmene zinthu zikhalire kwa ine. 24  Ndithudi, ndikukhulupirira kuti Ambuye andilola kuti inenso ndibwere posachedwa.+ 25  Koma panopa ndikuona kuti ndi bwino kuti ndikutumizireni Epafurodito. Ameneyu ndi mʼbale wanga, wantchito mnzanga ndi msilikali mnzanga. Iye ndi nthumwi yanu komanso amanditumikira pa zosowa zanga.+ 26  Ndikufuna kumutumiza chifukwa akulakalaka kukuonani nonsenu ndipo akuvutika maganizo chifukwa munamva kuti ankadwala. 27  Nʼzoona kuti anadwaladi mpaka kutsala pangʼono kufa. Koma Mulungu anamuchitira chifundo. Ndipotu chifundo chimenecho sanachitire iye yekha, koma anachitiranso ine kuti chisoni changa chisawonjezeke. 28  Choncho, ndikumutumiza mofulumira kwambiri kuti inu mukamuona mukhalenso osangalala ndiponso kuti nkhawa zanga zichepe. 29  Ndiye monga mwa nthawi zonse, mulandireni ndi manja awiri ngati mmene mumachitira polandira otsatira a Ambuye. Mumulandire mwachimwemwe ndipo abale ngati amenewa muziwalemekeza kwambiri,+ 30  chifukwa anatsala pangʼono kufa pamene ankagwira ntchito ya Khristu* ndipo anaika moyo wake pachiswe* kuti adzanditumikire mʼmalo mwa inu, popeza simukanatha kubwera kuno kuti mudzandithandize.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “wokonda kugawana mzimu kulikonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anakhala wofanana ndi anthu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “atayamba kuoneka ngati munthu.”
Kutanthauza anthu amene anamwalira ndipo adzaukitsidwa.
Kapena kuti, “pa ntchito yotumikira anthu imene.”
Mabaibulo ena amati, “ntchito ya Ambuye.”
Kapena kuti, “anaika moyo wake pangozi.”