Kalata Yopita kwa Aheberi 10:1-39
-
Nsembe za nyama zinali zosakwanira (1-4)
-
Chilamulo chinkachitira chithunzi zinthu zabwino (1)
-
-
Nsembe ya Khristu ndi yothandiza mpaka kalekale (5-18)
-
Njira yatsopano komanso yamoyo (19-25)
-
Tisaleke kusonkhana pamodzi (24, 25)
-
-
Anawachenjeza zokhudza kuchimwa mwadala (26-31)
-
Tizikhala olimba mtima komanso achikhulupiriro kuti tipirire (32-39)
10 Popeza Chilamulo chimangochitira chithunzi+ zinthu zabwino zimene zikubwera+ ndipo si zinthu zenizenizo, sichingachititse* amene amalambira Mulungu kukhala angwiro pogwiritsa ntchito nsembe zimene amapereka mosalekeza chaka chilichonse.+
2 Zikanakhala choncho, kodi nsembezo sakanasiya kuzipereka? Akanasiya chifukwa zikanakhala kuti anthu ochita utumiki wopatulikawo ayeretsedwa, sakanakhalanso ndi chikumbumtima chakuti ndi ochimwa.
3 Koma mosiyana ndi zimenezo, chaka chilichonse nsembe zimenezi zimawakumbutsa za machimo awo.+
4 Chifukwa nʼzosatheka kuti magazi a ngʼombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.
5 Choncho atabwera padzikoli iye anati: “‘Nsembe zanyama komanso nsembe zina simunazifune, koma munandikonzera thupi.
6 Nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zamachimo simunazivomereze.’+
7 Ndiyeno ine ndinati, ‘Taonani! Ine ndabwera (mumpukutu munalembedwa za ine) kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.’”+
8 Atanena kuti: “Nsembe zanyama, nsembe zopsereza zathunthu, nsembe zamachimo ndiponso nsembe zina simunazifune kapena kuzivomereza,” zomwe ndi nsembe zoperekedwa mogwirizana ndi Chilamulo.
9 Ananenanso kuti: “Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.”+ Akuchotsa dongosolo loyambalo kuti akhazikitse lachiwiri.
10 Tayeretsedwa ndi “chifuniro” chimenecho,+ kudzera mʼthupi la Yesu Khristu limene analipereka nsembe kamodzi kokha.+
11 Komanso, wansembe aliyense amaima pamalo ake kuti achite utumiki wopatulika+ ndiponso kuti apereke nsembe zimodzimodzizo mobwerezabwereza,+ zimene sizingachotseretu machimo.+
12 Koma munthu ameneyu anapereka nsembe imodzi yamachimo yothandiza mpaka kalekale, ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+
13 Kuyambira nthawi imeneyo, akudikira mpaka pamene adani ake adzaikidwe kuti akhale chopondapo mapazi ake.+
14 Kudzera mu nsembe imodzi yokha, iye akuchititsa anthu amene akuyeretsedwa kukhala angwiro+ mpaka kalekale.
15 Nawonso mzimu woyera ukuchitira umboni kwa ife, chifukwa unanena kuti:
16 “‘Pangano limene ndidzapangane nawo pambuyo pa masiku amenewo ndi ili: Ndidzaika malamulo anga mʼmitima yawo ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo awo,’+ akutero Yehova.”*
17 Kenako unanenanso kuti: “Ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo komanso zochita zawo zosonyeza kusamvera malamulo.”+
18 Ndiyeno zimenezi zikakhululukidwa, nsembe yamachimo sikhalanso yofunika.
19 Choncho abale, timalimba mtima kulowa mʼmalo oyera+ chifukwa cha magazi a Yesu.
20 Iye ndi amene anatitsegulira njira imeneyi yomwe ndi yatsopano komanso yamoyo ndipo imadutsa katani yotchingira,+ imene ndi thupi lake.
21 Popeza tili ndi wansembe wamkulu kwambiri woyangʼanira nyumba ya Mulungu,+
22 tiyeni tifike kwa Mulungu ndi mtima wonse komanso tili ndi chikhulupiriro chonse, chifukwa mitima yathu yayeretsedwa* kuti tisakhalenso ndi chikumbumtima choipa,+ ndipo matupi athu asambitsidwa mʼmadzi oyera.+
23 Tiyeni tipitirize kulengeza poyera chiyembekezo chathu ndipo tisagwedezeke,+ chifukwa amene watilonjeza ndi wokhulupirika.
24 Ndipo tiyeni tiganizirane* kuti tilimbikitsane pa nkhani yosonyezana chikondi ndiponso kuchita zabwino.+
25 Tisasiye kusonkhana pamodzi,+ ngati mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane+ ndipo tizichita zimenezi kwambiri, makamaka panopa pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.+
26 Ngati tikuchita machimo mwadala pambuyo podziwa choonadi molondola,+ palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.+
27 Koma pali chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo, ndiponso mkwiyo woyaka moto umene udzawononge otsutsawo.+
28 Munthu aliyense amene wanyalanyaza Chilamulo cha Mose amafa popanda kumuchitira chifundo, ngati anthu awiri kapena atatu apereka umboni.+
29 Ndiye kuli bwanji munthu amene wapondaponda Mwana wa Mulungu, amene akuona magazi a pangano amene anayeretsedwa nawo ngati chinthu wamba,+ amenenso wanyoza mzimu umene Mulungu amasonyezera kukoma mtima kwakukulu?+ Munthu ameneyu akuyenera kulandira chilango chachikulu kwambiri.
30 Popeza tikumudziwa amene anati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzabwezera ndine.” Amenenso anati: “Yehova* adzaweruza anthu ake.”+
31 Kupatsidwa chilango ndi Mulungu wamoyo nʼkoopsa.
32 Komabe, pitirizani kukumbukira masiku akale. Paja mutalandira kuwala kochokera kwa Mulungu,+ munakumana ndi mavuto aakulu.
33 Nthawi zina munkanyozedwa ndiponso kuzunzidwa pagulu* ndipo nthawi zina munkathandiza anthu ena amene ankakumana ndi mavuto ngati amenewa.
34 Munkachitira chifundo anthu amene anali mʼndende, ndipo munkasangalalabe ngakhale katundu wanu akulandidwa,+ podziwa kuti muli ndi chuma chabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa.+
35 Choncho, musasiye kukhala olimba mtima* chifukwa mudzalandira mphoto yaikulu kwambiri.+
36 Mukufunika kukhala opirira+ komanso kuchita chifuniro cha Mulungu kuti mudzalandire zimene Mulunguyo walonjeza.
37 “Kwatsala kanthawi kochepa”+ ndipo “amene akubwerayo afika ndithu, sachedwa.”+
38 “Koma wolungama wanga adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake,”+ ndipo “ngati angabwerere mʼmbuyo, ine sindikondwera naye.”+
39 Ife sitili mʼgulu la anthu obwerera mʼmbuyo kupita kuchiwonongeko,+ koma ndife anthu okhala ndi chikhulupiriro chomwe chingatithandize kudzapeza moyo.
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “anthu sangachititse.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mʼchilankhulo choyambirira “yawazidwa,” kutanthauza kuti yawazidwa magazi a Yesu.
^ Kapena kuti, “tiziderana nkhawa.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kukhala ngati chionetsero mʼbwalo la masewera.”
^ Kapena kuti, “musataye ufulu wanu wa kulankhula.”