Kalata Yopita kwa Aheberi 11:1-40
11 Chikhulupiriro ndi kusakayikira kuti zimene ukuyembekezera zidzachitika,+ umboni wooneka wakuti zinthu zosaoneka zilipodi.
2 Chifukwa cha chikhulupiriro, anthu akale* anali ndi umboni wakuti Mulungu akusangalala nawo.
3 Chifukwa cha chikhulupiriro, timazindikira kuti mawu a Mulungu anachititsa kuti nthawi* zosiyanasiyana zikhale mʼmalo mwake, moti zinthu zooneka zakhalapo kuchokera ku zinthu zosaoneka.
4 Chifukwa cha chikhulupiriro, Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yamtengo wapatali kuposa ya Kaini.+ Ndipo chifukwa cha chikhulupirirocho, Mulungu anamupatsa umboni wakuti anali wolungama chifukwa analandira* mphatso zakezo.+ Ngakhale kuti anafa, iye akulankhulabe+ kudzera mʼchikhulupiriro chakecho.
5 Chifukwa cha chikhulupiriro, Inoki+ anasamutsidwa kuti asafe mozunzika, moti sanapezeke kulikonse chifukwa Mulungu anamusamutsa.+ Asanamusamutse, Mulungu anamupatsa umboni wakuti akusangalala naye.
6 Ndiponso, popanda chikhulupiriro nʼzosatheka kusangalatsa Mulungu. Chifukwa aliyense wofuna kulambira Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi ndipo amapereka mphoto kwa anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.+
7 Chifukwa cha chikhulupiriro, Nowa+ atachenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zinali zisanaoneke,+ anasonyeza kuopa Mulungu ndipo anamanga chingalawa+ kuti banja lake lipulumukiremo. Chifukwa cha chikhulupiriro, anatsutsa dziko+ ndipo anaonedwa kuti ndi wolungama chifukwa cha chikhulupirirocho.
8 Chifukwa cha chikhulupiriro, Abulahamu+ ataitanidwa, anamvera nʼkupita kumalo amene ankayembekezera kuwalandira ngati cholowa. Iye anapitadi, ngakhale kuti sankadziwa kumene akupita.+
9 Chifukwa cha chikhulupiriro, ankakhala monga mlendo mʼdziko limene analonjezedwa.+ Iye ankakhala mʼmatenti+ pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, amenenso Mulungu anawalonjeza kuti adzawapatsa dzikoli.+
10 Chifukwa ankayembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene wokonza mapulani ake ndiponso kuumanga ndi Mulungu.+
11 Chifukwa cha chikhulupiriro, Sara nayenso analandira mphamvu yokhala ndi pakati* ngakhale kuti anali atapitirira zaka zobereka,+ chifukwa ankaona kuti wolonjezayo ndi wokhulupirika.*
12 Pa chifukwa chimenechi, kuchokera kwa mwamuna mmodzi, amene anali ngati wakufa,+ kunabadwa ana ambirimbiri+ ngati nyenyezi zakumwamba komanso osawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.+
13 Onsewa anafa ali ndi chikhulupiriro, ngakhale kuti malonjezowo sanakwaniritsidwe pa nthawi yawo.+ Koma anawaona ali patali+ ndipo anawalandira. Analengezanso poyera kuti iwo anali alendo komanso anthu osakhalitsa mʼdzikolo.
14 Chifukwa anthu amene amalengeza zinthu zimenezi amapereka umboni wakuti akufunafuna mwakhama malo awoawo.
15 Koma akanakhala kuti ankangoganizira za kumene anachokera,+ akanapeza chifukwa chowapangitsa kuti abwerere.
16 Koma tsopano akufunitsitsa malo abwino kwambiri, amene ndi akumwamba. Choncho Mulungu sachita manyazi kutchulidwa kuti Mulungu wawo,+ ndipo wawakonzera mzinda.+
17 Chifukwa cha chikhulupiriro, pamene Abulahamu anayesedwa,+ zinali ngati wapereka kale Isaki nsembe. Choncho munthu amene analandira malonjezo mokondwerayu, anali wokonzeka kupereka nsembe mwana wake yemwe anali mmodzi yekha.+
18 Anali wokonzeka kuchita zimenezo ngakhale kuti anali atauzidwa kuti: “Mbadwa* zimene ndinakulonjeza zidzachokera mwa Isaki.”+
19 Koma ankadziwa kuti akafa, Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa. Moti Mulungu anamubwezeradi mwana wakeyo ndipo zimenezi zinkaimira zinthu zina zamʼtsogolo.+
20 Chifukwa cha chikhulupiriro, Isaki nayenso anadalitsa Yakobo+ ndi Esau,+ ndipo anawauza zimene zidzachitike mʼtsogolo.
21 Chifukwa cha chikhulupiriro, Yakobo atatsala pangʼono kumwalira,+ anadalitsa ana aamuna a Yosefe mmodzimmodzi,+ ndipo kenako analambira Mulungu atatsamira ndodo yake.+
22 Chifukwa cha chikhulupiriro, Yosefe atatsala pangʼono kufa, ananena za kusamuka kwa Aisiraeli, ndipo anapereka malangizo okhudza* mafupa ake.*+
23 Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose atabadwa, makolo ake anamubisa kwa miyezi itatu,+ chifukwa anaona kuti mwanayo anali wooneka bwino.+ Iwo sanaope lamulo la mfumu.+
24 Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose atakula+ anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao,+
25 ndipo anasankha kuzunzidwa limodzi ndi anthu a Mulungu, mʼmalo mochita machimo nʼkusangalala kwa nthawi yochepa.
26 Iye anachita zimenezi chifukwa ankaona kuti kunyozedwa kwake monga Wodzozedwa* kuli ngati chuma chamtengo wapatali kuposa chuma cha ku Iguputo, chifukwa ankaganizira kwambiri mphoto imene adzalandire.
27 Chifukwa cha chikhulupiriro anachoka ku Iguputo,+ koma osati chifukwa choopa mfumu.+ Iye anapitiriza kupirira moleza mtima ngati akuona Wosaonekayo.+
28 Chifukwa cha chikhulupiriro, iye anachita Pasika ndipo anawaza magazi pamafelemu kuti mngelo wa Mulungu asaphe ana awo oyamba kubadwa.+
29 Chifukwa cha chikhulupiriro, anthu a Mulunguwo anawoloka pa Nyanja Yofiira patauma ngati pamtunda,+ koma Aiguputo atayesa kudutsa, nyanjayo inawamiza.+
30 Chifukwa cha chikhulupiriro, mpanda wa Yeriko unagwa, anthu atayenda mouzungulira kwa masiku 7.+
31 Chifukwa cha chikhulupiriro, Rahabi amene anali hule uja sanaphedwe limodzi ndi anthu osamvera, chifukwa iye analandira mwamtendere anthu amene anakafufuza za mzindawo.+
32 Kodi ndiperekenso zitsanzo zina? Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni,+ Baraki,+ Samisoni,+ Yefita,+ Davide+ komanso Samueli+ ndi aneneri ena.
33 Chifukwa cha chikhulupiriro, anthu amenewa anagonjetsa maufumu pankhondo,+ anachita chilungamo, analonjezedwa zinthu zina+ ndiponso anatseka mikango pakamwa.+
34 Sanapse ndi moto,+ sanaphedwe ndi lupanga,+ anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu,+ anamenya nkhondo mwamphamvu+ ndiponso anathamangitsa magulu ankhondo.+
35 Akazi analandira anthu akufa amene anaukitsidwa.+ Koma anthu ena anazunzidwa chifukwa sanalole kusiya chikhulupiriro chawo kuti amasulidwe. Iwo anachita zimenezi kuti adzaukitsidwe pa kuuka kwabwino kwambiri.
36 Ena anakumana ndi mayesero chifukwa ananyozedwa komanso kukwapulidwa. Kuwonjezera pamenepo anamangidwa+ ndiponso kutsekeredwa mʼndende.+
37 Anaponyedwa miyala,+ anayesedwa, anadulidwa pakati, anaphedwa ndi lupanga+ ndiponso anayendayenda atavala zikopa za nkhosa ndi zikopa za mbuzi.+ Ankasowa zinthu, ankazunzidwa+ komanso ankakumana ndi mavuto ena.+
38 Iwo anali abwino kwambiri, osayenera kukhala mʼdziko lotereli. Anayendayenda mʼzipululu, mʼmapiri, mʼmapanga+ ndi mʼmaenje a dziko lapansi.
39 Komabe ngakhale kuti onsewa Mulungu anawapatsa umboni wakuti akusangalala nawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo, sanaone kukwaniritsidwa kwa lonjezolo.
40 Zili choncho chifukwa Mulungu anaoneratu chinthu chabwino kwambiri choti atipatse,+ kuti iwo asakhale angwiro popanda ife.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “makolo athu akale.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “chifukwa anamuchitira umboni polandira.”
^ Kapena kuti, “wodalirika.”
^ Pakati pake panali poti adzabereke “mbadwa” kapena kuti “mbewu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mbewu.”
^ Kapena kuti, “lamulo lokhudza.”
^ Kapena kuti, “okhudza kumuika mʼmanda.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Khristu.”