Kalata Yopita kwa Aheberi 2:1-18
2 Nʼchifukwa chake zinthu zimene tinamva tiyenera kuziganizira mozama kuposa nthawi zonse,+ kuti tisatengeke pangʼonopangʼono nʼkusiya chikhulupiriro.+
2 Chifukwa ngati mawu amene angelo ananena+ analidi oona, ndipo chilango chinaperekedwa mwachilungamo pa tchimo lililonse ndi kusamvera kulikonse,+
3 ndiye tidzapulumuka bwanji ngati titanyalanyaza chipulumutso chachikulu chonchi?+ Ambuye wathu ndi amene anayamba kunena za chipulumutsochi+ ndipo anthu amene anamumva anatitsimikizira zimenezo.
4 Mulungu nayenso anachitira umboni za chipulumutsochi pogwiritsa ntchito zizindikiro, zinthu zodabwitsa, ntchito zamphamvu zosiyanasiyana+ komanso mzimu woyera umene anaupereka mogwirizana ndi chifuniro chake.+
5 Dziko lapansi limene likubweralo, limene ife tikunena, sanaliike pansi pa ulamuliro wa angelo.+
6 Koma mboni ina inanena penapake kuti: “Munthu ndi ndani kuti muzimuganizira, kapena mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimusamalira?+
7 Munamutsitsa pangʼono poyerekeza ndi angelo. Munamuveka ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu ndipo munamuika kuti azilamulira ntchito za manja anu.
8 Mwaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.”+ Popeza Mulungu anaika zinthu zonse pansi pa Mwana wake,+ ndiye kuti palibe chilichonse chimene anasiya osachiika pansi pa Mwanayo.+ Komabe, panopa sitikuona kuti zinthu zonse zili pansi pake.+
9 Koma tikuona Yesu, amene anamutsitsa pangʼono poyerekeza ndi angelo.+ Panopa amuveka ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu chifukwa chakuti anafa.+ Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, zimenezi zinamuchitikira kuti alawe imfa mʼmalo mwa munthu aliyense.+
10 Zinthu zonse zinakhalapo kuti zipereke ulemerero kwa Mulungu komanso zinakhalapo kudzera mwa iye. Choncho kuti athandize ana ambiri kukhala ndi ulemerero,+ zinali zoyenera kuti achititse Mtumiki Wamkulu wachipulumutso chawo+ kukhala wangwiro kudzera mʼmavuto amene anakumana nawo.+
11 Chifukwa onse, woyeretsa ndi amene ayeretsedwawo,+ amachokera kwa mmodzi.+ Choncho iye sachita manyazi kuwatchula kuti “abale” ake,+
12 pamene akunena kuti: “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani poimba nyimbo pakati pa mpingo.”+
13 Komanso pamene akunena kuti: “Ine ndidzamudalira.”+ Ndiponso kuti: “Taonani! Ine ndi ana amene Yehova* wandipatsa.”+
14 Popeza “ana” onsewo ndi a magazi ndi mnofu, iyenso anakhala wa magazi ndi mnofu.+ Anachita izi kuti kudzera mu imfa yake, awononge Mdyerekezi,+ amene ali ndi njira yobweretsera imfa.+
15 Anachitanso zimenezi kuti amasule onse amene anali mu ukapolo moyo wawo wonse chifukwa choopa imfa.+
16 Chifukwa sikuti iye akuthandiza angelo, koma akuthandiza mbadwa* za Abulahamu.+
17 Choncho iye anayenera kukhala ngati “abale” ake pa zinthu zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo komanso wokhulupirika pa zinthu zokhudza Mulungu, nʼcholinga choti apereke nsembe yophimba machimo a anthu+ kuti tigwirizanenso ndi Mulungu.
18 Popeza iye anavutika pamene ankayesedwa,+ amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.+