Kalata Yopita kwa Aheberi 3:1-19

  • Yesu ndi wamkulu kuposa Mose (1-6)

    • Zinthu zonse zinapangidwa ndi Mulungu (4)

  • Chenjezo lakuti tisakhale opanda chikhulupiriro (7-19)

    • “Lero mukamva mawu a Mulungu” (7,15)

3  Choncho, abale athu oyera, amene muli mʼgulu la anthu oitanidwa kumwamba,+ ganizirani za Yesu, mtumwi ndi mkulu wa ansembe amene tikumuvomereza.+ 2  Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamuika kukhala mtumwi ndi mkulu wa ansembe,+ ngati mmenenso Mose analili wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu.+ 3  Yesu akuyenera kupatsidwa ulemerero waukulu+ kuposa Mose, chifukwa womanga nyumba amakhala wolemekezeka kuposa nyumbayo. 4  Nʼzoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu. 5  Mose anali mtumiki wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu ndipo utumiki wakewo unali umboni wa zinthu zimene zidzanenedwe mʼtsogolo. 6  Koma Khristu anali mwana ndipo ankayangʼanira nyumba ya Mulungu mokhulupirika.+ Ife tikhalabe nyumba ya Mulunguyo+ tikapitiriza kukhala ndi ufulu wa kulankhula komanso kugwira mwamphamvu chiyembekezo chimene timachinyadira mpaka mapeto. 7  Choncho mogwirizana ndi zimene mzimu woyera ukunena+ kuti: “Lero mukamva mawu a Mulungu, 8  musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima kwambiri, ngati mmene zinalili pa tsiku limene anandiyesa mʼchipululu.+ 9  Mʼchipululumo, makolo anu anandiyesa ngakhale kuti anali ataona ntchito zanga kwa zaka 40.+ 10  Nʼchifukwa chake ndinanyansidwa ndi mʼbadwo umenewo, ndipo ndinati, ‘Mitima yawo imasochera nthawi zonse ndipo njira zanga sakuzidziwa.’ 11  Choncho ndinalumbira nditakwiya kuti, ‘Sadzalowa mumpumulo wanga.’”+ 12  Chenjerani abale kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo nʼkukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.+ 13  Mʼmalomwake, pitirizani kulimbikitsana tsiku ndi tsiku, nthawi iliyonse imene mukuti “Lero,”+ kuti chinyengo champhamvu cha uchimo chisaumitse mtima wa aliyense wa inu. 14  Chifukwa timachita nawo zimene Khristu akuchita, ngati zinthu zimene tinkadalira poyamba tazigwira mwamphamvu mpaka mapeto.+ 15  Paja Malemba amati: “Lero mukamva mawu a Mulungu, musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima kwambiri.”+ 16  Kodi paja ndi ndani amene anamva koma nʼkupsetsa mtima Mulungu? Kodi si anthu onse amene anatuluka mʼdziko la Iguputo motsogoleredwa ndi Mose?+ 17  Komanso, kodi Mulungu ananyansidwa ndi ndani kwa zaka 40?+ Kodi si anthu amene anachimwa aja, amene anafera mʼchipululu?+ 18  Nanga kodi analumbirira ndani kuti sadzalowa mumpumulo wake? Kodi si omwe aja amene sanamumvere? 19  Choncho, tikuona kuti sakanatha kulowa mumpumulowo chifukwa anali opanda chikhulupiriro.+

Mawu a M'munsi