Kalata Yopita kwa Aheberi 4:1-16

  • Kuopsa kosalowa mumpumulo wa Mulungu (1-10)

  • Anawalimbikitsa kuti alowe mumpumulo wa Mulungu (11-13)

    • Mawu a Mulungu ndi amoyo (12)

  • Yesu, mkulu wa ansembe wapamwamba (14-16)

4  Choncho, popeza lonjezo lolowa mumpumulo wake lidakalipo, samalani kuopera kuti wina wa inu angalephere kukwaniritsa zofunika kuti akalowe mu mpumulowo.+ 2  Uthenga wabwino unalengezedwa kwa ife,+ ngati mmenenso anaulengezera kwa makolo athu. Koma mawu amene iwo anamva sanapindule nawo, chifukwa analibe chikhulupiriro chofanana ndi cha amene anamvera mawuwo. 3  Ife amene tasonyeza chikhulupiriro tikulowadi mumpumulowo. Ponena za mpumulo umenewu iye anati: “Choncho ndinalumbira nditakwiya kuti, ‘Sadzalowa mumpumulo wanga,’”+ ngakhale kuti anali atamaliza ntchito zake pa nthawi imene dziko linkakhazikitsidwa.*+ 4  Ponena za tsiku la 7, penapake anati: “Ndipo Mulungu anapuma pa ntchito zake zonse pa tsiku la 7.”+ 5  Panonso akunena kuti: “Sadzalowa mumpumulo wanga.”+ 6  Choncho, popeza mwayi wolowa mumpumulowo udakalipo, ndipo amene anali oyamba kumva uthenga wabwino sanalowemo chifukwa cha kusamvera,+ 7  patapita nthawi, Mulungu ananena mu salimo la Davide, ngati mmene tanenera kale mu kalatayi kuti: “Lero anthu inu mukamva mawu a Mulungu, musaumitse mitima yanu.”+ Choncho wapatula tsiku limene akulitchula kuti “Lero.” 8  Chifukwa Yoswa+ akanawalowetsa mʼmalo ampumulo, Mulungu sakananenanso pambuyo pake za tsiku lina. 9  Choncho mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu.+ 10  Munthu amene walowa mumpumulo wa Mulungu, ndiye kuti wapumanso pa ntchito zake, ngati mmene Mulungu anapumira pa ntchito zake.+ 11  Choncho, tiyeni tichite zonse zimene tingathe kuti tilowe mumpumulo umenewo, nʼcholinga choti wina asakhale wosamvera ngati makolo athuwo.+ 12  Chifukwa mawu a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu,+ ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse.+ Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu komanso mafupa* ndi mafuta amʼmafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake. 13  Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino moti ifeyo tidzayankha kwa Mulunguyo pa zochita zathu.+ 14  Choncho, popeza tili ndi mkulu wa ansembe wapamwamba, Yesu Mwana wa Mulungu,+ amene anapita kumwamba, tiyeni tipitirize kulengeza zoti timamukhulupirira.+ 15  Chifukwa mkulu wa ansembe amene tili nayeyu, si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni pa zofooka zathu.+ Koma ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa pa zinthu zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.+ 16  Choncho, tiyeni tizifika kumpando wachifumu wa Mulungu ndipo tizipemphera ndi ufulu wa kulankhula+ kuti atichitire chifundo komanso kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi yoyenera.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuponya mbewu pansi.” Mbewuzo zikutanthauza ana a Adamu ndi Hava.
Mʼchilankhulo choyambirira, “malo amene mafupa amalumikizana.”