Kwa Akolose 2:1-23
2 Ndikufuna kuti mudziwe mavuto aakulu amene ndikukumana nawo chifukwa cha inuyo ndi anthu a ku Laodikaya+ komanso chifukwa cha anthu onse amene sanandionepo maso ndi maso.*
2 Ndikuchita zimenezi kuti mitima yawo ilimbikitsidwe+ ndiponso kuti onse akhale ogwirizana mʼchikondi+ komanso kuti alandire chuma chonse chimene chimabwera chifukwa chomvetsa bwino zinthu, popanda kukayikira chilichonse, nʼcholinga choti adziwe molondola chinsinsi chopatulika cha Mulungu, chomwe ndi Khristu.+
3 Chuma chonse chokhudzana ndi nzeru ndiponso kudziwa zinthu chinabisidwa mosamala mwa iye.+
4 Ndikunena zimenezi kuti munthu aliyense asakupusitseni ndi mfundo zokopa.
5 Ngakhale kuti sindili kumeneko, ndikuganizirabe za inu. Ndasangalala kumva kuti mumachita zinthu mwadongosolo+ komanso kuti muli ndi chikhulupiriro cholimba mwa Khristu.+
6 Tsopano popeza mumakhulupirira Khristu Yesu Ambuye wathu, pitirizani kuyenda mogwirizana naye.
7 Mogwirizana ndi zimene munaphunzira, chikhulupiriro chanu mwa Khristu chikhale ndi mizu yolimba, chipitirize kukula+ ndipo chikhale cholimba+ komanso nthawi zonse muzithokoza Mulungu.+
8 Samalani kuti wina asakugwireni ukapolo,* pogwiritsa ntchito nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake,+ mogwirizana ndi miyambo ya anthu komanso mfundo zimene anthu amʼdzikoli amayendera, osati mogwirizana ndi Khristu,
9 chifukwa iye ali ndi makhalidwe onse a Mulungu.+
10 Simukusowa kalikonse chifukwa cha iye, amene ndi mutu wa boma lililonse ndi ulamuliro uliwonse.+
11 Popeza muli naye pa ubwenzi munadulidwa ndipo mdulidwe wake sunali wochitidwa ndi manja a anthu koma unachitika pamene munavula thupi lauchimo,+ chifukwa mdulidwe wa atumiki a Khristu umakhala wotero.+
12 Zili choncho chifukwa munaikidwa naye limodzi mʼmanda pobatizidwa ubatizo wofanana ndi wake.+ Ndipo popeza muli naye pa ubwenzi komanso mumakhulupirira zinthu zimene Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa+ anapanga ndi mphamvu zake, munaukitsidwa naye limodzi.+
13 Kuwonjezera pamenepo, ngakhale kuti munali akufa chifukwa cha machimo anu komanso chifukwa choti munali osadulidwa, Mulungu anakupatsani moyo kuti mukhale ogwirizana ndi Khristu.+ Mokoma mtima anatikhululukira machimo athu onse+
14 ndipo anafafaniza Chilamulo+ chimene chinali ndi malamulo ambirimbiri+ omwe ankatitsutsa.+ Iye anachichotsa pochikhomerera pamtengo wozunzikirapo.*+
15 Pogwiritsa ntchito mtengo wozunzikirapowo, iye anavula maboma ndi olamulira nʼkuwasiya osavala ndipo anawaonetsa poyera kuti anthu onse aone kuti wawagonjetsa+ nʼkumayenda nawo ngati akaidi.
16 Choncho musalole kuti munthu aliyense akuweruzeni chifukwa cha chakudya ndi chakumwa+ kapena chikondwerero chinachake kapenanso kusunga tsiku limene mwezi watsopano waoneka+ kapena kusunga sabata.+
17 Zinthu zimenezi ndi mthunzi wa zimene zinali kubwera,+ koma zenizeni zake zinakwaniritsidwa ndi Khristu.+
18 Musalole kuti munthu aliyense amene amasangalala ndi kudzichepetsa kwachinyengo komanso kulambira angelo* akulepheretseni kudzalandira mphoto.+ “Munthu woteroyo amaumirira” zinthu zimene waona ndipo maganizo ake ochimwa amamuchititsa kuti azidzitukumula popanda chifukwa chomveka.
19 Sakutsatira amene ndi mutu,+ amene kudzera mwa iye, thupi lonse limapeza zonse zimene limafunikira ndipo ziwalo zake ndi zolumikizana bwino ndi mfundo zake komanso minyewa ndipo limakulabe mothandizidwa ndi Mulungu.+
20 Ngati munafa limodzi ndi Khristu ndipo simukutsatiranso mfundo zimene anthu amʼdzikoli amayendera,+ nʼchifukwa chiyani mukupitiriza kukhala ngati mudakali mbali ya dzikoli, pogonjeranso malamulo akuti:+
21 “Usatenge ichi, kapena usalawe ichi, kapena usakhudze ichi”?
22 Malamulo amenewa akunena za zinthu zimene zimatha munthu akamazigwiritsa ntchito ndipo ndi malamulo komanso zinthu zimene anthu amaphunzitsa.+
23 Ngakhale kuti zinthu zimenezo zimaoneka ngati zanzeru, amene amazichitawo amasankha okha njira yolambirira. Iwo amazunza thupi lawo+ kuti anthu aziona ngati ndi odzichepetsa. Koma zimenezo nʼzosathandiza kwa munthu amene akulimbana ndi zimene thupi limalakalaka.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amene sanaonepo nkhope yanga.”
^ Kapena kuti, “asakugwireni ngati nyama.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “kulambira ngati mmene angelo amachitira.”