Kwa Akolose 3:1-25
3 Komabe, ngati munaukitsidwa limodzi ndi Khristu,+ pitirizani kufunafuna zinthu zakumwamba, kumene Khristu wakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+
2 Pitirizani kuganizira zinthu zakumwamba,+ osati zinthu zapadziko lapansi.+
3 Chifukwa munafa ndipo moyo wanu wabisidwa limodzi ndi Khristu amene ndi wogwirizana ndi Mulungu.
4 Khristu, amene ndi moyo wathu,+ akadzaonetsa mphamvu zake,* inunso mudzaonetsa naye limodzi mphamvu zanu mu ulemerero.+
5 Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu+ padziko lapansi kukhala zakufa ku chiwerewere,* zinthu zodetsa, chilakolako chosalamulirika cha kugonana,+ kulakalaka zinthu zoipa komanso dyera limene ndi kulambira mafano.
6 Mulungu adzasonyeza mkwiyo wake kwa anthu amene akuchita zimenezi.
7 Inunso munkachita zomwezo, pamene munkakhala moyo wofanana ndi anthu amenewo.+
8 Koma tsopano muyenera kutaya zonsezo kutali ndi inu. Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa+ komanso mawu achipongwe+ ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.+
9 Musamanamizane.+ Vulani umunthu* wakale+ pamodzi ndi ntchito zake,
10 ndipo muvale umunthu watsopano+ umene Mulungu amapereka. Umunthu watsopano umenewu ndi wopangidwa mogwirizana ndi chifaniziro cha Mulungu.+ Choncho pamene mukudziwa Mulungu molondola, pitirizani kuchititsa umunthu wanu kukhala watsopano.
11 Mukatero, sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti,* kapolo kapena mfulu, chifukwa Khristu amachita zinthu zonse ndipo ife ndife ogwirizana naye.+
12 Choncho monga anthu osankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo chachikulu,+ kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa+ komanso kuleza mtima.+
13 Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse,+ ngakhale pamene wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.+ Mofanana ndi Yehova* amene anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso muzichita chimodzimodzi.+
14 Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ chifukwa chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.+
15 Komanso lolani kuti mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima yanu,+ popeza munaitanidwa ku mtendere umenewu monga ziwalo za thupi limodzi. Ndipo sonyezani kuti ndinu oyamikira.
16 Mawu a Khristu akhazikike mwa inu ndipo akupatseni nzeru zonse. Pitirizani kuphunzitsana ndi kulimbikitsana* ndi masalimo,+ nyimbo zotamanda Mulungu komanso nyimbo zauzimu zoyamikira. Pitirizani kuimbira Yehova* mʼmitima yanu.+
17 Chilichonse chimene mukuchita mʼmawu kapena mu ntchito, muzichita zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, ndipo muziyamika Mulungu Atate kudzera mwa iye.+
18 Inu akazi, muzigonjera amuna anu,+ chifukwa zimenezi ndi zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye.
19 Inu amuna, pitirizani kukonda akazi anu+ ndipo musamawapsere mtima kwambiri.*+
20 Ana inu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse,+ chifukwa zimenezi zimasangalatsa Ambuye.
21 Inu abambo, musamakwiyitse* ana anu,+ kuti asakhale okhumudwa.
22 Inu akapolo, muzimvera anthu amene ndi ambuye anu+ pa zinthu zonse, osati pokhapokha pamene akukuonani pongofuna kusangalatsa anthu,* koma moona mtima ndiponso moopa Yehova.*
23 Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova,*+ osati anthu,
24 chifukwa mukudziwa kuti mphoto imene mudzalandire ndi cholowa chochokera kwa Yehova.*+ Tumikirani Ambuye wanu Khristu monga akapolo.
25 Ndithudi, amene akuchita zolakwa adzalandira chilango chifukwa cha zolakwa zimene akuchitazo,+ chifukwa Mulungu sakondera.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “akadzaonetsedwa.”
^ MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu.”
^ Mawu akuti “Msukuti” akutanthauza munthu wachimidzimidzi.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “kulangizana.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “ndipo musamawachitire nkhanza.”
^ Kapena kuti, “musamapsetse mtima.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “osati mwachiphamaso ngati munthu wongofuna kusangalatsa anthu.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.