Amosi 4:1-13

  • Uthenga wotsutsana ndi ngʼombe za ku Basana (1-3)

  • Yehova ananyoza kulambira kwabodza kwa Aisiraeli (4, 5)

  • Aisiraeli anakana kubwerera kwa Mulungu (6-13)

    • “Konzekera kukumana ndi Mulungu wako” (12)

    • ‘Mulungu amafotokozera munthu zimene akuganiza’ (13)

4  “Tamverani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basana,Amene mumakhala mʼphiri la Samariya,+Inu akazi amene mukuchitira zachinyengo anthu ovutika+ komanso kuphwanya anthu osauka.Ndipo mumauza amuna* anu kuti, ‘Tipatseni chakumwa kuti timwe!’  2  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, walumbira mogwirizana ndi kuyera kwake kuti,‘“Taonani! Masiku adzafika pamene iye adzakukolani ndi ngowe zokolera nyama nʼkukunyamulani.Ndipo otsala adzawakola ndi mbedza.  3  Mudzatulukira pamabowo a mpanda amene muli nawo pafupi.Ndipo mudzaponyedwa kunja, ku Harimoni,” watero Yehova.’  4  ‘Bwerani ku Beteli anthu inu kuti mudzachite zolakwa,*+Bwerani ku Giligala kuti mudzawonjezere machimo.+ Bweretsani nsembe zanu+ mʼmawa.Ndipo pa tsiku lachitatu, mubweretse chakhumi* chanu.+  5  Perekani nsembe zoyamikira za mkate wokhala ndi zofufumitsa.+Ndipo lengezani mokweza za nsembe zanu zaufulu! Chifukwa nʼzimene mumakonda kuchita, inu Aisiraeli,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.  6  ‘Mʼmizinda yanu yonse, ine sindinakupatseni chakudya.Ndipo ndinachititsa kuti mʼnyumba zanu zonse musakhale chakudya.+Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.  7  ‘Ine ndinakumanani mvula kutatsala miyezi itatu kuti mukolole.+Ndinagwetsa mvula mumzinda wina koma mumzinda wina sindinagwetse. Mvula inagwa mʼmunda umodziKoma mʼmunda wina, mmene simunagwe mvula, munauma.  8  Anthu amʼmizinda iwiri kapena itatu anayenda movutikira kupita mumzinda wina kuti akamwe madzi,+Ndipo ludzu lawo silinathe,Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.  9  ‘Ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha komanso matenda a chuku.+ Munachulukitsa minda yanu ya mpesa ndi ya mbewu zina.Koma dzombe linawononga mitengo yanu ya mkuyu ndi ya maolivi,+Ndipo inu simunabwererebe kwa ine,’+ watero Yehova. 10  ‘Ndinakutumizirani mliri ngati wa ku Iguputo.+ Ndinapha anyamata anu ndi lupanga+ ndipo mahatchi anu analandidwa.+ Ndinachititsa kuti fungo lonunkha lamʼmisasa yanu lifike mʼmphuno mwanu,+Koma inu simunabwerere kwa ine,’ watero Yehova. 11  ‘Ndinakubweretserani chiwonongekoNgati chimene Mulungu anabweretsa ku Sodomu ndi Gomora.+ Ndipo inu munali ngati chikuni cholanditsidwa pamoto.Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova. 12  Ndidzakuchitiranso zimenezo, iwe Isiraeli. Ndipo chifukwa chakuti ndidzakuchitira zimenezi,Konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Isiraeli. 13  Taona! Iye ndi amene anapanga mapiri+ ndipo analenganso mphepo,+Amafotokozera munthu zimene akuganiza,Amachititsa kuwala kwa mʼbandakucha kukhala mdima,+Ndiponso amaponda malo okwezeka a dziko lapansi.”+Dzina lake ndi Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ambuye.”
Kapena kuti, “mudzandigalukire.”
Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”