Kalata Yopita kwa Aroma 10:1-21
10 Abale, chimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pemphero langa lochonderera kwa Mulungu ndi lakuti anthu a mtundu wanga apulumutsidwe.+
2 Chifukwa ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka potumikira Mulungu,+ koma sakumudziwa molondola.
3 Ndipo chifukwa chosadziwa chilungamo cha Mulungu,+ iwo sanagonjere chilungamocho+ koma anafuna kukhazikitsa chawochawo.+
4 Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo,+ kuti aliyense wokhulupirira akhale wolungama.+
5 Pajatu Mose analemba zokhudza mmene munthu angachitire chilungamo mogwirizana ndi Chilamulo, anati: “Aliyense amene akuchita zimenezi adzakhala ndi moyo chifukwa cha malamulo.”+
6 Koma za chilungamo chimene chimabwera chifukwa cha chikhulupiriro, Malemba amati: “Mumtima mwako usanene kuti,+ ‘Kodi ndani adzapite kumwamba?’+ kuti akatsitse Khristu.
7 Kapena, ‘Kodi ndani adzapite kuphompho?’+ kuti akaukitse Khristu.”
8 Koma kodi lemba limati chiyani? Limati: “Mawu a chilamulowo ali pafupi ndi inu, ali mʼkamwa mwanu ndi mumtima mwanu,”+ amenewa ndi “mawu” a chikhulupiriro amene tikulalikira.
9 Chifukwa ngati ukulengeza ‘mawu amene ali mʼkamwa mwakowo,’ akuti Yesu ndi Ambuye,+ ndipo mumtima mwako ukukhulupirira kuti Mulungu anamuukitsa, udzapulumuka.
10 Kuti munthu akhale wolungama amayenera kukhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake, koma ndi pakamwa pake amalengeza+ poyera chikhulupiriro chake kuti apulumuke.
11 Paja lemba lina limati: “Palibe wokhulupirira iye amene adzakhumudwe.”+
12 Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki,+ popeza kwa onsewo Ambuye ndi mmodzi, amene amapereka mowolowa manja kwa onse oitana pa dzina lake.
13 Chifukwa “aliyense woitana pa dzina la Yehova* adzapulumuka.”+
14 Komabe, kodi angaitane bwanji pa dzina lake ngati samukhulupirira? Angakhulupirire bwanji ngati sanamvepo za iye? Nanga angamve bwanji za iye popanda wina kulalikira?
15 Ndipo angalalikire bwanji ngati sanatumidwe?+ Zili ngati mmene Malemba amanenera kuti: “Mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwambiri.”+
16 Ngakhale zili choncho, si onse amene anatsatira uthenga wabwino. Chifukwa Yesaya anati: “Yehova,* kodi ndani wakhulupirira zimene anamva kwa ife?”+
17 Choncho munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.+ Ndipo zimene wamvazo zimachokera mʼmawu onena za Khristu.
18 Koma ndifunse kuti, Kodi kumva sanamve? Pajatu “mawu awo anamveka padziko lonse lapansi, ndipo uthenga wawo unamveka mpaka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.”+
19 Komanso ndifunse kuti, Kodi si zoona kuti Aisiraeli anadziwa?+ Choyamba Mose anati: “Ndidzakuchititsani nsanje pogwiritsa ntchito anthu omwe si Aisiraeli. Ndidzakukwiyitsani koopsa pogwiritsa ntchito mtundu wopusa.”+
20 Koma Yesaya analankhula molimba mtima kwambiri kuti: “Anthu amene anandipeza ndi amene sankandifunafuna.+ Ndinadziwika kwa anthu amene sanafunse za ine.”+
21 Koma ponena za Aisiraeli iye anati: “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu osamvera ndiponso amakani.”+