Kalata Yopita kwa Aroma 12:1-21
12 Choncho abale, ndikukudandaulirani mwa chifundo chachikulu cha Mulungu kuti mupereke matupi anu+ ngati nsembe yamoyo, yoyera+ ndiponso yovomerezeka kwa Mulungu, yomwe ndi utumiki wopatulika pogwiritsa ntchito luso la kuganiza.+
2 Musamatengere* nzeru za nthawi* ino, koma khalani munthu watsopano posintha kwambiri maganizo anu,+ kuti muzindikire chifuniro cha Mulungu,+ chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.
3 Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu anandisonyeza, ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.+ Koma aliyense aziganiza mwanzeru nʼkumadziweruza mogwirizana ndi chikhulupiriro chimene Mulungu wamupatsa.+
4 Thupi limakhala ndi ziwalo zambiri,+ koma ziwalozo sizigwira ntchito yofanana.
5 Chimodzimodzinso ifeyo, ngakhale kuti tilipo ambiri, ndife thupi limodzi mwa Khristu ndipo ndife ziwalo zolumikizana.+
6 Tili ndi mphatso zosiyanasiyana mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu kumene tinasonyezedwa.+ Choncho kaya tili ndi mphatso ya ulosi, tiyeni tizilosera mogwirizana ndi chikhulupiriro chathu.
7 Ngati tili ndi mphatso ya utumiki, tiyeni tizichitabe utumikiwo. Amene amaphunzitsa, aziphunzitsa ndithu.+
8 Amene amalimbikitsa, azilimbikitsa.+ Wogawa, azigawa mowolowa manja.+ Wotsogolera, azitsogolera mwakhama.+ Ndipo wosonyeza chifundo, azichita zimenezo mosangalala.+
9 Chikondi chanu chisakhale chachiphamaso.+ Muzinyansidwa ndi zoipa+ nʼkumayesetsa kuchita zabwino.
10 Pokonda abale, muzikhala ndi chikondi chenicheni. Pa nkhani yosonyezana ulemu, muziyamba ndi inuyo.+
11 Khalani akhama osati aulesi.+ Yakani ndi mzimu.+ Tumikirani Yehova* monga akapolo.+
12 Kondwerani chifukwa cha chiyembekezo. Muzipirira mavuto.+ Muzilimbikira kupemphera.+
13 Gawanani ndi oyera mogwirizana ndi zimene akusowa.+ Khalani ochereza.+
14 Pitirizani kudalitsa anthu amene akukuzunzani.+ Muzidalitsa, osati kutemberera.+
15 Muzisangalala ndi anthu amene akusangalala ndipo muzilira ndi anthu amene akulira.
16 Muziona ena mmene inuyo mumadzionera. Musamaganize modzikuza, koma khalani ndi mtima wodzichepetsa.+ Musamadzione ngati anzeru.+
17 Musamabwezere choipa pa choipa.+ Muziganizira zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino.
18 Ngati nʼkotheka, yesetsani mmene mungathere kuti muzikhala mwamtendere ndi anthu onse.+
19 Okondedwa, musamabwezere zoipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.+ Chifukwa Malemba amati: “‘Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine,’ watero Yehova.”*+
20 Koma “ngati mdani wako ali ndi njala, umʼpatse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, umʼpatse chakumwa. Chifukwa ukatero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.”*+
21 Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa pochita chabwino.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Musamaumbidwe.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kutanthauza kufewetsa ndiponso kusungunula mtima wa munthu wovuta.