Kalata Yopita kwa Aroma 13:1-14

  • Kugonjera olamulira (1-7)

  • Chikondi chimakwaniritsa Chilamulo (8-10)

  • Tizichita zinthu ngati masana (11-14)

13  Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu,+ chifukwa palibe ulamuliro umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola.+ Olamulira amene alipowa ali mʼmaudindo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.+ 2  Choncho amene akutsutsana ndi ulamuliro, akutsutsana ndi zimene Mulungu anakonza. Amene akutsutsana ndi zimene Mulungu anakonza adzalandira chiweruzo. 3  Chifukwa olamulira amaopsa ngati ukuchita zoipa, osati ngati ukuchita zabwino.+ Choncho kodi ukufuna kuti usamaope olamulira? Pitiriza kuchita zabwino,+ ndipo olamulira adzakutamanda. 4  Olamulirawo ndi mtumiki wa Mulungu kuti zinthu zikuyendere bwino. Koma ngati ukuchita zoipa, chita mantha chifukwa sagwira lupanga pachabe, popeza iwo ndi mtumiki wa Mulungu wosonyeza mkwiyo wa Mulungu kwa munthu wochita zoipa. 5  Choncho pali chifukwa chabwino choti muzigonjera, osati chabe chifukwa choopa mkwiyowu koma chifukwanso cha chikumbumtima chanu.+ 6  Nʼchifukwa chake mumakhomanso misonkho, popeza iwo ndi antchito a Mulungu otumikira anthu ndipo akukwaniritsa cholinga chimenechi nthawi zonse. 7  Muzipereka kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, mʼpatseni msonkho.+ Amene amafuna ndalama ya chiphaso, mʼpatseni ndalama ya chiphaso. Amene amafuna kuopedwa, muopeni.+ Amene amafuna kupatsidwa ulemu, mʼpatseni ulemu wake.+ 8  Anthu inu musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, kupatulapo kukondana,+ popeza amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo.+ 9  Chifukwa malamulo onena kuti, “usachite chigololo,+ usaphe munthu,+ usabe,+ usasirire mwansanje,”+ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili mʼmawu awa akuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 10  Chikondi sichilimbikitsa munthu kuchitira mnzake zoipa,+ choncho chikondi chimathandiza munthu kuti akwaniritse lamulo.+ 11  Chitani zimenezi, makamakanso chifukwa chakuti nyengo ino mukuidziwa, kuti tili kale mu nthawi yoti mudzuke ku tulo,+ chifukwa panopa chipulumutso chathu chili pafupi kwambiri kusiyana ndi nthawi imene tinakhala okhulupirira. 12  Usiku uli pafupi kutha ndipo masana ayandikira. Choncho tiyeni tivule ntchito za mdima+ ndipo tivale zida za kuwala.+ 13  Tiyeni tikhale ndi khalidwe loyenera+ ngati anthu amene akuchita zinthu masana. Tizipewa maphwando oipa,* kumwa mwauchidakwa,* chiwerewere, khalidwe lopanda manyazi,*+ mikangano ndiponso nsanje.+ 14  Koma valani Ambuye Yesu Khristu,+ ndipo musamakonzekere kuchita zimene thupi limalakalaka.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “maphwando aphokoso.”
Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti “kumwa mwauchidakwa” amatanthauza kumwa mowa kwambiri ndiponso mosadziletsa nʼcholinga chofuna kuledzera.
MʼChigiriki a·sel′gei·a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.