Kalata Yopita kwa Aroma 3:1-31
3 Kodi kukhala Myuda kuli ndi ubwino wotani, kapena phindu la mdulidwe nʼchiyani?
2 Ubwino wake ndi wambiri. Choyamba, mawu opatulika a Mulungu anaikidwa mʼmanja mwa Ayuda.+
3 Nanga bwanji ngati ena anali osakhulupirika? Kodi kupanda chikhulupiriro kwawoko kukutanthauza kuti Mulungunso ndi wosakhulupirika?
4 Ayi. Ngakhale munthu aliyense atakhala wabodza,+ Mulungu angapezekebe kuti ndi wonena zoona+ mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Mukamalankhula, mumalankhula zachilungamo kuti muwine pamene mukuweruzidwa.”+
5 Komabe ngati kusalungama kwathu kukusonyeza bwino kuti Mulungu ndi wolungama, ndiye tinene kuti chiyani? Kodi tingati Mulungu ndi wosalungama akamaonetsa mkwiyo wake? (Ndikulankhula ngati mmene anthu ena amalankhulira.)
6 Ayi! Nanga Mulungu akapanda kutero, dziko adzaliweruza bwanji?+
7 Koma ngati chifukwa cha bodza langa choonadi cha Mulungu chaonekera kwambiri ndipo zimenezo zamubweretsera ulemerero, nʼchifukwa chiyani ndikuweruzidwa ngati wochimwa?
8 Ndilekerenji kunena zimene ena amatinamizira kuti timanena zija, zakuti: “Tiyeni tichite zoipa kuti pakhale zinthu zabwino”? Anthu amene amanena zimenezi adzaweruzidwa mogwirizana ndi chilungamo.+
9 Ndiye kodi zikatero Ayudafe tili pabwino kuposa ena? Ayi ndithu. Chifukwa monga tanena kale, Ayuda ndiponso Agiriki, onse amalamuliridwa ndi uchimo+
10 mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Palibe munthu wolungama ndi mmodzi yemwe.+
11 Palibe amene ali wozindikira ngakhale pangʼono komanso palibe amene akuyesetsa kufunafuna Mulungu.
12 Anthu onse apatuka, ndipo onse akhala opanda pake. Palibiretu ndi mmodzi yemwe amene akusonyeza kukoma mtima.”+
13 “Mmero wawo* ndi manda otseguka. Iwo amalankhula zachinyengo ndi lilime lawo.”+ “Mʼmilomo yawo muli poizoni wa njoka.”+
14 “Ndipo mʼkamwa mwawo mwadzaza matemberero ndi mawu opweteka.”+
15 “Mapazi awo amathamangira kukakhetsa magazi.”+
16 “Zonse zimene amachita zimakhala zowononga ndiponso zobweretsa mavuto,
17 ndipo njira ya mtendere sakuidziwa.”+
18 “Maso awo saona chifukwa choopera Mulungu.”+
19 Tikudziwa kuti zinthu zonse zimene Chilamulo chimanena zimagwira ntchito kwa amene amatsatira Chilamulo. Cholinga chake nʼkuchititsa anthu kuti asowe chonamizira komanso kusonyeza kuti dziko lonse lili ndi mlandu pamaso pa Mulungu ndipo ndi loyenera kulandira chilango.+
20 Choncho palibe munthu amene amaonedwa wolungama ndi Mulungu chifukwa chotsatira Chilamulo,+ popeza Chilamulo chimatithandiza kudziwa bwino uchimo.+
21 Koma tsopano, zadziwika kuti munthu akhoza kukhala wolungama kwa Mulungu popanda kutsatira Chilamulo.+ Zimenezi zinatchulidwanso mʼChilamulo komanso zimene aneneri analemba.+
22 Kuonedwa wolungama ndi Mulungu kumeneku kungatheke kwa onse amene amasonyeza kuti amakhulupirira Yesu Khristu, chifukwa palibe kusiyana.+
23 Popeza anthu onse ndi ochimwa ndipo amalephera kusonyeza bwinobwino ulemerero wa Mulungu.+
24 Ndipo kuonedwa olungama chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu+ kumene wakusonyeza powamasula ndi dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu,+ kuli ngati mphatso yaulere.+
25 Mulungu anamupereka ngati nsembe yoti anthu agwirizanenso ndi Mulunguyo+ pokhulupirira magazi ake.+ Anachita zimenezi pofuna kuonetsa chilungamo chake chifukwa anasonyeza kuti ndi wosakwiya msanga pokhululuka machimo amene anachitika kale.
26 Anachita zimenezi kuti asonyeze chilungamo chake+ pa nthawi inoyo poona kuti munthu amene amakhulupirira Yesu ndi wolungama.+
27 Choncho, kodi pamenepa palinso chifukwa chodzitamira? Palibetu. Kodi tizidzitama chifukwa chotsatira Chilamulo?+ Ndithudi ayi, koma chifukwa chotsatira lamulo la chikhulupiriro.
28 Taona kuti munthu amakhala wolungama mwa chikhulupiriro, osati potsatira Chilamulo.+
29 Kapena kodi iye ndi Mulungu wa Ayuda okha?+ Kodi si Mulungu wa anthu a mitundu inanso?+ Inde, iye ndi Mulungunso wa anthu a mitundu ina.+
30 Popeza Mulungu ndi mmodzi,+ iye adzaona kuti anthu odulidwa ndi olungama+ chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Adzaonanso kuti anthu osadulidwa ndi olungama+ chifukwa cha chikhulupiriro chawo.
31 Kodi pamenepa tikuthetsa Chilamulo mwa chikhulupiriro chathu? Ayi! Mʼmalomwake, tikulimbikitsa Chilamulo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Kukhosi kwawo.”