Kalata Yopita kwa Aroma 7:1-25

  • Fanizo losonyeza mmene munthu amamasukira ku Chilamulo (1-6)

  • Chilamulo chinathandiza kuti uchimo uonekere (7-12)

  • Kulimbana ndi uchimo (13-25)

7  Ndikulankhula ndi inu abale, amene mumadziwa Chilamulo. Kodi simukudziwa kuti Chilamulo chimakhala ndi mphamvu pa munthu pamene munthuyo ali ndi moyo? 2  Mwachitsanzo, mkazi wokwatiwa amakhala womangidwa kwa mwamuna wake mwalamulo pamene mwamunayo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi amakhala womasuka ku lamulo lokhudza mwamuna wake.+ 3  Ngati mkaziyo angakwatiwe ndi mwamuna wina mwamuna wake ali moyo, ndiye kuti wachita chigololo.+ Koma ngati mwamuna wake wamwalira, mkaziyo wamasuka ku lamulo lokhudza mwamuna wake, choncho sanachite chigololo ngati atakwatiwa ndi mwamuna wina.+ 4  Abale anga, thupi la Khristu linakumasulani ku Chilamulo, kuti mukhale a winawake+ amene anaukitsidwa+ nʼcholinga choti tibale zipatso kwa Mulungu.+ 5  Chifukwa pamene tinkakhala mogwirizana ndi matupi athu ochimwawa, Chilamulo chinachititsa kuti zilakolako za uchimo zimene tinali nazo mʼmatupi* mwathu zionekere. Ndipo zilakolako zimenezi zikanatibweretsera imfa.+ 6  Koma tsopano tamasulidwa ku Chilamulo,+ chifukwa tafa ku Chilamulo chimene chinkatimanga, kuti tikhale akapolo mʼnjira yatsopano motsogoleredwa ndi mzimu,+ osati mʼnjira yakale motsogoleredwa ndi malamulo olembedwa.+ 7  Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi Chilamulo ndi uchimo? Ayi ndithu. Kunena zoona, sindikanadziwa uchimo zikanakhala kuti panalibe Chilamulo.+ Mwachitsanzo, sindikanadziwa kusirira kwa nsanje zikanakhala kuti Chilamulo sichinanene kuti: “Usasirire mwansanje.”+ 8  Koma chifukwa cha lamulo, uchimo unapeza njira yondichititsa kukhala ndi kusirira kwansanje kwa mtundu uliwonse. Chifukwa popanda Chilamulo, uchimo unali wopanda mphamvu.*+ 9  Chilamulo chisanaperekedwe ndinali wamoyo. Koma Chilamulo chitafika, uchimo unakhalanso ndi moyo, koma ineyo ndinafa.+ 10  Ndipo lamulo limene linkafunika kunditsogolera kuti ndipeze moyo,+ linanditsogolera ku imfa. 11  Uchimo unagwiritsa ntchito lamulo limeneli pondinyengerera ndipo unandipha. 12  Choncho Chilamulo pachokha nʼchoyera ndipo malamulo ndi oyera, olungama ndiponso abwino.+ 13  Kodi zimenezi zikutanthauza kuti chinthu chabwino chinachititsa kuti ndife? Ayi. Uchimo ndi umene unachititsa kuti ndife. Chilamulo nʼchabwino, kungoti chinachititsa kuti zidziwike bwino kuti uchimo ukuchititsa kuti ndife.+ Choncho malamulo anatithandiza kudziwa kuti uchimo ndi woipa kwambiri.+ 14  Chifukwa tikudziwa kuti Chilamulo nʼchochokera kwa Mulungu kudzera mwa mzimu, koma ineyo si ine wangwiro ndipo ndinagulitsidwa ku uchimo.+ 15  Sinditha kumvetsa zimene zimandichitikira. Chifukwa zimene ndimafuna kuchita, sindizichita. Koma zimene ndimadana nazo nʼzimene ndimachita. 16  Komabe ngati ndimachita zimene sindikufuna kuchita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti Chilamulo nʼchabwino. 17  Komano amene akuchita zimenezo si inenso, koma uchimo umene uli ndi ine.+ 18  Ndikudziwa kuti mʼthupi langa lochimwali, mulibe chilichonse chabwino. Chifukwa ndimafuna kuchita zabwino, koma sinditha kuzichita.+ 19  Zinthu zabwino zimene ndimafuna kuchita sindichita, koma zoipa zimene sindifuna kuchita nʼzimene ndimachita. 20  Tsopano ngati ndimachita zimene sindifuna ndiye kuti amene ndikuchita zimenezo si inenso, koma uchimo umene uli ndi ine. 21  Zimene zimandichitikira ndi zakuti,* pamene ndikufuna kuchita zinthu zabwino, zoipa zimakhala mkati mwangamu.+ 22  Mumtima mwanga ndimasangalala kwambiri ndi malamulo a Mulungu,+ 23  koma ndimaona lamulo lina mʼthupi* langa likumenyana ndi malamulo amʼmaganizo mwanga+ nʼkundichititsa kukhala kapolo wa lamulo la uchimo+ limene lili mʼthupi* langa. 24  Munthu womvetsa chisoni ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likundichititsa kuti ndifeli? 25  Mulungu adzandipulumutsa kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Choncho mʼmaganizo mwanga ndine kapolo wa malamulo a Mulungu, koma mʼthupi langa ndine kapolo wa lamulo la uchimo.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼziwalo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “unali wakufa.”
Kapena kuti, “Ndimapeza lamulo lakuti.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼziwalo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼziwalo.”