Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 5:1-14
5 Kenako ndinaona mpukutu umene unalembedwa mbali zonse,* uli mʼdzanja lamanja la Mulungu amene anakhala pampando wachifumu.+ Mpukutuwo anaumata molimba ndi zidindo 7 zomatira.
2 Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti: “Ndi ndani ali woyenera kumatula zidindo zimene amatira mpukutuwu nʼkuutsegula?”
3 Koma panalibe aliyense kaya kumwamba, padziko lapansi kapena pansi pa nthaka, amene anatha kutsegula mpukutuwo kapena kuyangʼanamo ndi kuuwerenga.
4 Choncho ndinalira kwambiri chifukwa sipanapezeke wina aliyense woyenera kutsegula mpukutuwo kapena kuyangʼanamo nʼkuuwerenga.
5 Koma mmodzi wa akulu aja anandiuza kuti: “Tonthola. Taona! Mkango wa fuko la Yuda,+ muzu+ wa Davide,+ anapambana pankhondo+ moti ndi woyenera kumatula zidindo 7 zimene amatira mpukutuwo nʼkuutsegula.”
6 Kenako ndinaona mwana wa nkhosa+ amene ankaoneka ngati waphedwa,+ ataimirira pakati pa mpando wachifumu ndi angelo 4 aja komanso pakati pa akulu aja.+ Iye anali ndi nyanga 7 ndiponso maso 7. Maso amenewa akuimira mizimu 7 ya Mulungu,+ imene yatumizidwa padziko lonse lapansi.
7 Nthawi yomweyo iye anapita nʼkukatenga mpukutu umene unali mʼdzanja lamanja la Mulungu amene anakhala pampando wachifumu.+
8 Atatenga mpukutuwo, angelo 4 ndi akulu 24 aja+ anagwada nʼkuwerama pamaso pa Mwanawankhosa. Aliyense wa iwo anali ndi zeze komanso mbale yagolide yodzaza ndi zofukiza. (Zofukizazo zikuimira mapemphero a oyera.)+
9 Iwo ankaimba nyimbo yatsopano+ yakuti: “Inu ndinu woyenera kutenga mpukutuwo ndi kumatula zidindo zake zomatira, chifukwa munaphedwa ndipo ndi magazi anu munagula anthu kuti atumikire Mulungu.+ Anthuwo ndi ochokera mu fuko lililonse, chilankhulo chilichonse, mtundu uliwonse ndi dziko lililonse.+
10 Ndipo munawapanga kuti akhale mafumu+ ndi ansembe a Mulungu wathu,+ moti adzakhala mafumu+ olamulira dziko lapansi.”
11 Kenako, ndinaona ndi kumva mawu a angelo ambiri atazungulira mpando wachifumu limodzi ndi angelo 4 komanso akulu aja. Chiwerengero chawo chinali 10 sauzande kuchulukitsa ndi 10 sauzande* ndiponso mamiliyoni kuchulukitsa ndi masauzande.+
12 Iwo ankanena mofuula kuti: “Mwanawankhosa amene anaphedwa+ ndi woyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi madalitso.”+
13 Ndipo cholengedwa chilichonse chakumwamba, padziko lapansi, pansi pa nthaka,+ panyanja, ndi zinthu zonse zammenemo, ndinazimva zikunena kuti: “Mulungu amene wakhala pampando wachifumu+ komanso Mwanawankhosa,+ atamandidwe, alandire ulemu,+ ulemerero komanso mphamvu mpaka kalekale.”+
14 Ndiyeno angelo 4 aja ankanena kuti: “Ame!” Ndipo akulu aja ankagwada nʼkuwerama ndi kulambira Mulungu.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mkati ndi kunja komwe.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “miyanda kuchulukitsa ndi miyanda.”