Danieli 3:1-30

  • Fano lagolide la Mfumu Nebukadinezara (1-7)

    • Analamula kuti aliyense alambire fano (4-6)

  • Aheberi atatu anawaneneza kuti sakumvera (8-18)

    • “Sititumikira milungu yanu” (18)

  • Anaponyedwa mungʼanjo yamoto (19-23)

  • Anapulumutsidwa modabwitsa mungʼanjo yamoto (24-27)

  • Mfumu inalemekeza Mulungu wa Aheberi (28-30)

3  Mfumu Nebukadinezara inapanga fano lagolide limene linali lalitali mikono 60* ndipo mulifupi mwake linali mikono 6.* Fanoli analiimika mʼchigwa cha Dura, mʼchigawo cha Babulo. 2  Kenako Mfumu Nebukadinezara inatumiza uthenga kwa masatarapi,* akuluakulu a boma, abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu a zamalamulo ndi oyangʼanira onse a zigawo kuti asonkhane kumwambo wotsegulira fano limene Mfumu Nebukadinezara inaimika. 3  Choncho masatarapi, akuluakulu a boma, abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu a zamalamulo ndi oyangʼanira onse a zigawo, anasonkhana kumwambo wotsegulira fano limene Mfumu Nebukadinezara inaimika. Iwo anaimirira patsogolo pa fano limene Nebukadinezara anaimika. 4  Wolengeza mauthenga anafuula kuti: “Mfumu ikukulamulani, inu anthu a mitundu yosiyanasiyana komanso olankhula zinenero zosiyanasiyana, 5  kuti mukangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamngʼono, zeze wamakona atatu, choimbira chazingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zina zonse zoimbira, mugwade nʼkuwerama mpaka nkhope zanu pansi ndipo mulambire fano lagolide limene Mfumu Nebukadinezara yaimika. 6  Aliyense amene sagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi nʼkulambira fanolo, nthawi yomweyo aponyedwa mungʼanjo yoyaka moto.”+ 7  Choncho anthu onse atangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamngʼono, zeze wamakona atatu, choimbira chazingwe ndi zipangizo zina zonse zoimbira, anthu onse a mitundu yosiyanasiyana komanso olankhula zinenero zosiyanasiyana, anagwada nʼkulambira fano lagolide limene Mfumu Nebukadinezara inaimika. 8  Pa nthawi imeneyo, Akasidi ena anapita kwa mfumu kukaneneza* Ayuda. 9  Iwo anauza Mfumu Nebukadinezara kuti: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale. 10  Inuyo mfumu munalamula kuti munthu aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamngʼono, zeze wamakona atatu, choimbira chazingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zina zonse zoimbira, agwade nʼkulambira fano lagolide. 11  Munalamulanso kuti aliyense amene sagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi nʼkulambira fanolo aponyedwe mungʼanjo yoyaka moto.+ 12  Koma pali Ayuda ena amene munawaika kuti aziyangʼanira ntchito za boma mʼchigawo cha Babulo. Amuna amenewa ndi Shadireki,* Misheki* ndi Abedinego.+ Iwo sakukumverani inu mfumu ndipo sakutumikira milungu yanu moti akukana kulambira fano lagolide limene mwaimika.” 13  Ndiyeno Nebukadinezara anapsa mtima kwambiri ndipo analamula kuti abweretse Shadireki, Misheki ndi Abedinego. Choncho anabweretsadi amuna amenewa pamaso pa mfumu. 14  Nebukadinezara anawafunsa kuti: “Kodi ndi zoonadi kuti inu Shadireki, Misheki ndi Abedinego simukutumikira milungu yanga+ komanso kuti mukukana kulambira fano lagolide limene ndaimika? 15  Ndiye ngati ndinu okonzeka kugwada nʼkulambira fano lagolide, mukamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamngʼono, zeze wamakona atatu, choimbira chazingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zina zonse zoimbira, zili bwino. Koma mukakana kulambira, nthawi yomweyo muponyedwa mungʼanjo yoyaka moto. Ndipo ndi mulungu uti amene angakupulumutseni mʼmanja mwanga?”+ 16  Ndiye Shadireki, Misheki ndi Abedinego anayankha mfumuyo kuti: “Inu Mfumu Nebukadinezara, palibenso china chimene ife tinganene kwa inu pa nkhani imeneyi. 17  Ngati mungatiponyere mungʼanjo yoyaka moto, Mulungu wathu amene tikumutumikira akhoza kutipulumutsa. Iye akhozanso kutipulumutsa mʼmanja mwanu mfumu.+ 18  Koma ngakhale atapanda kutipulumutsa, dziwani mfumu kuti ife sititumikira milungu yanu kapena kulambira fano lagolide limene mwaimika.”+ 19  Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima kwambiri ndi Shadireki, Misheki ndi Abedinego ndipo nkhope yake inasintha.* Iye analamula kuti ngʼanjoyo aisonkhezere kuwirikiza ka 7 kuposa mmene ankachitira nthawi zonse. 20  Iye analamula asilikali ake ena amphamvu kuti amange Shadireki, Misheki ndi Abedinego nʼkuwaponya mungʼanjo yoyaka motoyo. 21  Choncho amuna amenewa anamangidwa atavala nsalu zawo zakunja, zovala zawo, zipewa zawo ndi zovala zawo zina zonse ndipo anawaponya mungʼanjo yoyaka moto ija. 22  Koma chifukwa chakuti mfumu inalamula zimenezi itapsa mtima kwambiri komanso ngʼanjo ya motoyo inali yotentha kwambiri, asilikali amene anatenga Shadireki, Misheki ndi Abedinego aja ndi amene anaphedwa ndi malawi a moto. 23  Koma amuna atatuwa, Shadireki, Misheki ndi Abedinego, anagwera mungʼanjo ya motoyo ali omangidwa. 24  Ndiyeno Mfumu Nebukadinezara inachita mantha kwambiri ndipo inanyamuka mwachangu nʼkufunsa nduna zake zapamwamba kuti: “Kodi sitinaponye amuna atatu pamoto titawamanga?” Ndunazo zinayankha mfumuyo kuti: “Inde, mfumu.” 25  Ndiyeno mfumu inati: “Taonani! Inetu ndikuona amuna 4 akuyendayenda pakati pa moto ali osamangidwa komanso sakupsa, ndipo munthu wa 4 akuoneka ngati mwana wa milungu.” 26  Nebukadinezara anayandikira khomo la ngʼanjo yoyaka motoyo nʼkunena kuti: “Shadireki, Misheki ndi Abedinego, inu atumiki a Mulungu Wamʼmwambamwamba,+ tulukani ndipo mubwere kuno!” Atatero, Shadireki, Misheki ndi Abedinego anatuluka pakati pa motowo. 27  Masatarapi, akuluakulu a boma, abwanamkubwa ndi nduna zapamwamba za mfumu amene anasonkhana kumeneko,+ anaona kuti amuna amenewa+ motowo sunawawotche* ngakhale pangʼono. Tsitsi la kumutu kwawo ndi limodzi lomwe silinawauke. Zovala zawo sizinasinthe ndipo sankamveka ngakhale fungo la moto. 28  Kenako Nebukadinezara ananena kuti: “Atamandike Mulungu wa Shadireki, Misheki ndi Abedinego+ amene anatumiza mngelo wake nʼkudzapulumutsa atumiki ake. Atumiki akewo anamudalira ndipo sanamvere lamulo la mfumu, moti anali okonzeka kufa* mʼmalo motumikira kapena kulambira mulungu wina aliyense kupatulapo Mulungu wawo.+ 29  Choncho ine ndikuika lamulo lakuti, anthu a mtundu uliwonse kapena olankhula zinenero zosiyanasiyana amene anganene chilichonse chotsutsana ndi Mulungu wa Shadireki, Misheki ndi Abedinego ayenera kudulidwa nthulinthuli ndipo nyumba zawo zisandutsidwe zimbudzi za anthu onse,* chifukwa palibe mulungu wina amene amatha kupulumutsa anthu ake mofanana ndi ameneyu.”+ 30  Kenako mfumu inakweza paudindo* Shadireki, Misheki ndi Abedinego mʼchigawo cha Babulo.+

Mawu a M'munsi

Pafupifupi mamita 27. Onani Zakumapeto B14.
Pafupifupi mamita 2.7. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “kukanenera zoipa.”
Kapena kuti, “Sadirake.”
Kapena kuti, “Mesake.”
Kapena kuti, “ndipo anawakwiyira kwambiri.”
Kapena kuti, “anaona kuti motowo unalibe mphamvu pa iwo.”
Kapena kuti, “kupereka matupi awo.”
Mabaibulo ena amati, “kudzala; milu yandowe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “inachititsa kuti zinthu zizimuyendera bwino.”