Deuteronomo 18:1-22
18 “Alevi omwe ndi ansembe, komanso fuko lonse la Levi, sadzapatsidwa gawo kapena cholowa pakati pa Aisiraeli. Iwo azidzadya nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, zomwe ndi cholowa chake.+
2 Choncho asamalandire cholowa pakati pa abale awo. Cholowa chawo ndi Yehova, mogwirizana ndi zimene anawauza.
3 Tsopano zinthu zimene ansembe azidzalandira kuchokera kwa anthu ndi izi: Amene akupereka nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa, azipereka kwa wansembe mwendo wakutsogolo, nsagwada ndi chifu.
4 Aziperekanso kwa wansembe mbewu zawo zoyambirira kucha, vinyo wawo watsopano, mafuta awo ndi ubweya wa nkhosa zawo umene ameta moyambirira.+
5 Yehova Mulungu wanu wamusankha pamodzi ndi ana ake, pakati pa mafuko anu onse, kuti atumikire mʼdzina la Yehova nthawi zonse.+
6 Koma Mlevi akatuluka mu umodzi mwa mizinda yanu mu Isiraeli kumene ankakhala,+ ndipo akufuna kupita kumalo amene Yehova wasankha,*+
7 angathe kumatumikira kumeneko mʼdzina la Yehova Mulungu wake mofanana ndi Alevi onse, omwe ndi abale ake, amene akutumikira kumeneko pamaso pa Yehova.+
8 Chakudya chimene azikalandira chikakhale chofanana ndi cha ansembe onse,+ kuwonjezera pa zimene walandira atagulitsa cholowa chimene analandira kwa makolo ake.
9 Mukakalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musakaphunzire kuchita zinthu zonyansa zimene anthu a mitundu yakumeneko akuchita.+
10 Pakati panu pasapezeke munthu wowotcha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ aliyense wochita zamatsenga,+ aliyense woombeza,+ wanyanga,+
11 aliyense wochesula* ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu+ kapena wolosera zamʼtsogolo,+ kapena aliyense wofunsira kwa akufa.+
12 Chifukwa aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akuchita zimenezi, Yehova Mulungu wanu akuwathamangitsa pamaso panu.
13 Mukhale opanda cholakwa pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+
14 Mitundu imene mukuilanda dziko inkamvera anthu ochita zamatsenga+ ndi olosera.+ Koma Yehova Mulungu wanu sanakuloleni kuti muzichita zimenezi.
15 Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine kuchokera pakati pa abale anu, ndipo mudzamumvere mneneri ameneyo.+
16 Adzakupatsani mneneriyu poyankha zimene munapempha Yehova Mulungu wanu ku Horebe, tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Paja munapempha kuti, ‘Mutilole kuti tisamvenso mawu a Yehova Mulungu wathu kapena kuona moto waukuluwu, kuopera kuti tingafe.’+
17 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti, ‘Zimene anenazo ndi zabwino.
18 Ndidzawapatsa mneneri ngati iwe kuchokera pakati pa abale awo.+ Ndidzaika mawu anga mʼkamwa mwake,+ ndipo adzawauza zonse zimene ndidzamulamule.+
19 Ndipo munthu amene sadzamvera mawu anga amene iye adzalankhule mʼdzina langa, adzayankha mlandu kwa ine.+
20 Ngati mneneri wina angadzikuze nʼkulankhula mʼdzina langa mawu amene sindinamulamule kuti alankhule, kapena kulankhula mʼdzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe ndithu.+
21 Koma munganene mumtima mwanu kuti: “Tidzadziwa bwanji kuti si Yehova amene walankhula mawuwo?”
22 Mneneri akalankhula mʼdzina la Yehova, koma zimene walankhulazo osachitika kapena kukwaniritsidwa, ndiye kuti si Yehova amene walankhula mawu amenewo. Mneneriyo walankhula mawu amenewo modzikuza ndipo musachite naye mantha.’”
Mawu a M'munsi
^ Amenewa ndi malo amene Yehova wasankha kuti akhale malo olambirira.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wodutsitsa pamoto mwana wake wamwamuna kapena wamkazi.”
^ Mawu akuti ‘kuchesulaʼ amatanthauza kupweteka kapena kulepheretsa munthu kuchita chinachake mwa njira ya matsenga.