Deuteronomo 2:1-37

  • Anayenda mʼchipululu kwa zaka 38 (1-23)

  • Anagonjetsa Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni (24-37)

2  “Ndiyeno tinatembenuka nʼkulowera kuchipululu kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira, mogwirizana ndi zimene Yehova anandiuza.+ Ndipo tinayenda masiku ambiri mʼdera lapafupi ndi phiri la Seiri. 2  Kenako Yehova anandiuza kuti, 3  ‘Mwayenda kwa nthawi yaitali mʼdera lapafupi ndi phirili. Tsopano mulowere kumpoto. 4  Auze anthuwo kuti: “Mudutsa mʼmalire a dziko la abale anu, mbadwa za Esau,+ amene akukhala ku Seiri.+ Iwo adzachita nanu mantha,+ choncho muyenera kukhala osamala kwambiri. 5  Musalimbane nawo,* chifukwa sindikupatsani mbali iliyonse ya dziko lawo, ngakhale kachigawo kokwana phazi limodzi lokha, chifukwa ndinapereka phiri la Seiri kwa Esau kuti likhale malo ake.+ 6  Mudzawapatse ndalama pa chakudya chimene mudzadye, ndipo mudzapereke ndalama pa madzi amene mudzamwe.+ 7  Chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita. Iye akudziwa bwino kuti mukuyenda mʼchipululu chachikuluchi. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu zaka 40 zimenezi, ndipo simunasowe kanthu.”’+ 8  Choncho tinadutsa pafupi ndi abale athu, mbadwa za Esau,+ amene akukhala ku Seiri, ndipo sitinayende njira ya Araba, Elati ndi Ezioni-geberi.+ Kenako tinatembenuka nʼkudutsa njira ya mʼchipululu cha Mowabu.+ 9  Ndiyeno Yehova anandiuza kuti, ‘Usalimbane ndi Amowabu kapena kuchita nawo nkhondo, chifukwa sindidzakupatsa mbali iliyonse ya dziko lawo kuti likhale lako. Ndinapereka Ari kwa mbadwa za Loti+ kuti akhale malo awo. 10  (Kale mʼdzikoli munkakhala Aemi,+ anthu amphamvu kwambiri ndiponso ochuluka. Iwo anali ataliatali ngati Aanaki. 11  Arefai+ nawonso ankaoneka ngati Aanaki,+ ndipo Amowabu ankawatchula kuti Aemi. 12  Poyamba, Ahori+ ankakhala ku Seiri, koma mbadwa za Esau zinawalanda dzikolo nʼkuwapha ndipo iwo anayamba kukhala mʼdzikolo,+ mofanana ndi zimene Aisiraeli adzachite ndi dziko limene ndi cholowa chawo, limene Yehova adzawapatsadi.) 13  Tsopano nyamukani muwoloke chigwa cha Zeredi.’* Choncho tinawolokadi chigwa cha Zeredi.+ 14  Panadutsa zaka 38 kuti tiyende kuchokera ku Kadesi-barinea nʼkuwoloka chigwa cha Zeredi,* mpaka mʼbadwo wonse wa amuna opita kunkhondo utatha pakati pathu, mogwirizana ndi zimene Yehova analumbira kwa iwo.+ 15  Pogwiritsa ntchito dzanja lake, Yehova anawachotsa pakati panu mpaka onse anatha.+ 16  Amuna onse opita kunkhondo pakati pa anthuwo atatha kufa,+ 17  Yehova analankhulanso ndi ine kuti, 18  ‘Lero mudutsa malire a dziko la Mowabu, kapena kuti Ari. 19  Mukafika pafupi ndi Aamoni, musawavutitse kapena kulimbana nawo, chifukwa sindidzakupatsani mbali iliyonse ya dziko la Aamoni kuti likhale lanu. Dziko limeneli ndinalipereka kwa mbadwa za Loti kuti likhale lawo.+ 20  Dziko limenelinso linkadziwika kuti ndi la Arefai.+ (Kale mʼdzikoli munkakhala Arefai ndipo Aamoni ankawatchula kuti Azamuzumi. 21  Anthu amenewa anali amphamvu kwambiri komanso ochuluka ndipo anali ataliatali ngati Aanaki.+ Koma Yehova anawagonjetsa pamaso pa Aamoni, ndipo Aamoniwo anawathamangitsa moti anatenga dzikolo nʼkumakhalamo. 22  Mulungu anachitanso zimenezi kwa mbadwa za Esau zimene zikukhala ku Seiri.+ Iye anagonjetsa Ahori+ pamaso pawo kuti mbadwa za Esauzo zitenge dzikolo nʼkumakhalamo mpaka lero. 23  Koma Aavi ankakhala mʼmidzi mpaka kukafika ku Gaza.+ Iwo ankakhala mʼmidzi imeneyi mpaka pamene Akafitorimu+ ochokera ku Kafitori,* anawawononga nʼkuyamba kukhala mʼmidzi yawoyo.) 24  Nyamukani ndipo muwoloke chigwa cha Arinoni.*+ Taonani, ndapereka mʼmanja mwanu Sihoni+ yemwe ndi munthu wa Chiamori, mfumu ya Hesiboni. Choncho yambani kulanda dziko lake ndipo muchite naye nkhondo. 25  Lero ndichititsa kuti anthu onse okhala pansi pa thambo, amene amva za inu, achite nanu mantha kwambiri nʼkuyamba kukuopani. Iwo adzasokonezeka maganizo ndipo adzanjenjemera* chifukwa cha inu.’+ 26  Kenako ndinatumiza amithenga kuchokera mʼchipululu cha Kademoti+ kupita kwa Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni, kuti akanene uthenga wamtendere kuti,+ 27  ‘Ndilole ndidutse mʼdziko lako. Ndidzangodutsa mumsewu ndipo sindidzakhotera kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 28  Ndidzadya chakudya komanso kumwa madzi amene udzandigulitse. Ungondilola kuti ndidutse mʼdziko lako 29  mpaka kukawoloka Yorodano nʼkulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wathu anatipatsa. Izi nʼzimene mbadwa za Esau zimene zikukhala ku Seiri komanso Amowabu amene akukhala ku Ari anandichitira.’ 30  Koma Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni sinatilole kuti tidutse mʼdziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ komanso kuti aumitse mtima wake, nʼcholinga choti amupereke mʼmanja mwanu monga mmene zilili lero.+ 31  Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Taona, ndayamba kale kupereka Sihoni ndi dziko lake kwa iwe. Yamba kulanda dziko lake.’+ 32  Sihoni atatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kudzamenya nafe nkhondo ku Yahazi,+ 33  Yehova Mulungu wathu anamupereka kwa ife ndipo tinamugonjetsa limodzi ndi ana ake komanso anthu ake onse. 34  Pa nthawi imeneyo, tinalanda mizinda yake yonse ndi kuwononga mzinda wina uliwonse. Tinapha amuna, akazi ndi ana ndipo sitinasiye munthu aliyense ndi moyo.+ 35  Ziweto zokha nʼzimene tinatenga pamodzi ndi zinthu zimene tinatenga mʼmizinda imene tinalanda. 36  Kuchokera ku Aroweli,+ mzinda umene uli mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni,* (kuphatikizapo mzinda umene uli mʼchigwacho), mpaka kukafika ku Giliyadi, panalibe mzinda umene sitinathe kuugonjetsa. Yehova Mulungu wathu anawapereka onsewo kwa ife.+ 37  Koma simunayandikire dziko la Aamoni,+ dera lonse lamʼmbali mwa chigwa cha Yaboki,*+ kapena mizinda yamʼdera lamapiri, kapenanso malo alionse amene Yehova Mulungu wathu anatiletsa.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Musawavutitse.”
Kapena kuti, “khwawa la Zeredi.”
Kapena kuti, “khwawa la Zeredi.”
Kutanthauza Kerete.
Kapena kuti, “khwawa la Arinoni.”
Kapena kuti, “adzamva ululu ngati umene munthu amamva pobereka.”
Kapena kuti, “khwawa la Arinoni.”
Kapena kuti, “khwawa la Yaboki.”