Deuteronomo 26:1-19
26 “Mukakalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu, ndipo mukakalitengadi nʼkumakhalamo,
2 mukatenge zina mwa zipatso zoyambirira pa zokolola* zonse zamʼmunda mwanu zimene mudzakolole mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Mukaziike mʼdengu nʼkupita nazo kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuika dzina lake.+
3 Muzikapita kwa wansembe amene azidzatumikira masiku amenewo nʼkumuuza kuti, ‘Lero ndikuvomereza pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti ndalowadi mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo athu kuti adzatipatsa.’+
4 Ndiyeno wansembeyo azikalandira dengulo mʼmanja mwanu nʼkuliika pafupi ndi guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu.
5 Kenako muzikanena pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Bambo anga anali munthu wongoyendayenda wa Chiaramu*+ ndipo anapita ku Iguputo+ ndi anthu ochepa amʼbanja lawo+ nʼkukakhala kumeneko monga mlendo. Koma ali kumeneko anakhala mtundu waukulu ndi wamphamvu.+
6 Ndipo Aiguputo anayamba kutizunza komanso kutipondereza, moti ankatigwiritsa ntchito yowawa yaukapolo.+
7 Choncho tinayamba kufuulira Yehova, Mulungu wa makolo athu, ndipo Yehova anamva mawu athu nʼkuona masautso athu, mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu.+
8 Pamapeto pake Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula,+ zinthu zochititsa mantha, zizindikiro ndiponso zodabwitsa.+
9 Ndiyeno anatibweretsa kumalo ano nʼkutipatsa dziko ili, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+
10 Choncho ndabweretsa zipatso zoyambirira mwa zipatso za mʼdziko limene Yehova anandipatsa.’+
Ndipo muzikaziika pamaso pa Yehova Mulungu wanu nʼkugwada pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
11 Mukatero muzikasangalala chifukwa cha zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wanu wapereka kwa inuyo ndi anthu a mʼnyumba yanu, komanso kwa Mlevi ndi mlendo amene akukhala pakati panu.+
12 Mukamaliza kusonkhanitsa chakhumi+ chonse cha zokolola zanu mʼchaka chachitatu, chaka chopereka chakhumi, muzikapereka chakhumicho kwa Mlevi, mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye ndipo azidzadya nʼkukhuta mʼmizinda yanu.*+
13 Kenako muzidzanena pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Ndachotsa zinthu zonse zopatulika mʼnyumba mwanga nʼkuzipereka kwa Mlevi, mlendo amene akukhala pakati pathu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye,+ mogwirizana ndi zimene munandilamula. Sindinaphwanye kapena kunyalanyaza malamulo anu.
14 Sindinadyeko zina mwa zimenezi pa nthawi imene ndinali pa chisoni,* kapena kutengapo zina mwa zimenezi ndili wodetsedwa, kapena kupereka zina mwa zinthu zimenezi chifukwa cha munthu wakufa. Ndamvera mawu a Yehova Mulungu wanga ndipo ndachita zonse zimene munandilamula.
15 Tsopano yangʼanani pansi kuchokera kumwamba, kumalo anu oyera okhalako, ndipo mudalitse anthu anu Aisiraeli ndi dziko limene mwatipatsa,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ mogwirizana ndi zimene munalumbira kwa makolo athu.’+
16 Lero Yehova Mulungu wanu akukulamulani kuti muzitsatira malangizo ndi zigamulo zimenezi. Choncho muzisunga ndi kutsatira zimenezi ndi mtima wanu wonse+ komanso moyo wanu wonse.
17 Lero Yehova wakutsimikizirani kuti adzakhala Mulungu wanu ngati mukuyenda mʼnjira zake ndi kusunga malangizo ake,+ malamulo ake+ ndi zigamulo zake+ ndiponso ngati mukumvera mawu ake.
18 Ndipo lero mwatsimikizira Yehova kuti mudzakhala anthu ake komanso chuma chake chapadera,+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani. Ndiponso mwamutsimikizira kuti mudzasunga malamulo ake onse.
19 Zikadzatero adzakukwezani pamwamba pa mitundu ina yonse imene anapanga.+ Zimenezi zidzachititsa kuti mutamandidwe, mutchuke komanso kuti mulandire ulemerero mukapitiriza kukhala anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu,+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani.”
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “zipatso.”
^ Mabaibulo ena amati, “munthu wa Chiaramu amene watsala pangʼono kufa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”
^ Kutanthauza kukhala pa chisoni chifukwa cha imfa ya munthu amene ankamukonda.